Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

DOMINICAN REPUBLIC

Ufulu Wolalikira

Ufulu Wolalikira

Trujillo Anaphedwa

Pofika mu 1960, ulamuliro wa Trujillo unkatsutsidwa kwambiri ndi mayiko akunja komanso anthu a m’dzikolo. Ngakhale kuti panali mavutowa, mu January 1961, Milton Henschel anabwera kuchokera kulikulu lathu kudzachititsa msonkhano wa masiku atatu. Panafika anthu 957 ndipo anthu 27 anabatizidwa. M’bale Henschel anathandiza abale kuti ayambe kukonzanso dongosolo loti ntchito yolalikira iziyenda bwino komanso kuti alembe mapu a magawo.

Panali oyang’anira madera awiri. Wina anali Enrique Glass, wina Julián López. Julián anati: “M’dera langa munali mipingo yonse ya kumpoto ndi mipingo iwiri ya kum’mawa. Enrique ankayendera mipingo ina yonse ya kum’mawa ndiponso ya kum’mwera.” Oyang’anira derawa anathandiza kuti abale ndi alongo azitsogoleredwanso ndi gulu komanso azilimbikitsidwa.

Salvino ndi Helen Ferrari akupita ku Dominican Republic mu 1961

Salvino ndi Helen Ferrari amene analowa kalasi yachiwiri ya Giliyadi anatumizidwanso m’dzikoli mu 1961. Poyamba anali amishonale ku Cuba ndipo zimene anaphunzira kumeneko zinathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira ku Dominican Republic. Salvino anadzakhala mu Komiti ya Nthambi mpaka pamene anamwalira mu 1997. Helen wakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 79 ndipo zaka zambiri n’zimene wakhala akuchita umishonale.

Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene banja la a Ferrari linafika m’dzikoli, Trujillo anaphedwa. Izi zinachitika usiku wa pa May 30, 1961 pamene anthu anaombera koopsa galimoto yake. Koma kuphedwa kwa Trujillo sikunachititse kuti m’dzikoli mukhale mtendere. Mavuto anapitirira kwa zaka zingapo.

Ntchito Yolalikira Inkayenda Bwino

M’dzikoli munafikanso amishonale ena monga William Dingman amene analowa kalasi yoyamba ya Giliyadi ndi mkazi wake Estelle. Kunafikanso Thelma Critz ndi Flossie Coroneos kuchokera kunthambi ya ku Puerto Rico. Iwo anafika patangodutsa masiku awiri kuchokera pamene Trujillo anaphedwa. William anati: “Tinapeza dziko lonse lili njenjenje ndipo asilikali anali paliponse. Anthu ankaopa kuti pachitika zinazake zoopsa ndipo aliyense ankasechedwa kwambiri. Tinaimitsidwa m’marodibuloko ambirimbiri ndipo ankasanthula chilichonse m’zikwama zathu. Ngakhale tinthu ting’onoting’ono ankatitulutsa m’chikwama n’kutiyang’anitsitsa.” Kulalikira pa nthawi imeneyi kunali kovuta kwambiri.

Thelma Critz ndi Estelle komanso William Dingman adakali m’dzikoli ndipo akhala akuchita umishonale kwa zaka 67

William anati: “Mu ulamuliro wa Trujillo anthu ankauzidwa kuti a Mboni za Yehova ndi anthu achikomyunizimu oipa kwambiri. . . . Koma pang’ono ndi pang’ono tinathandiza anthu kuyamba kutimvetsa n’kusiya kudana nafe.” Ntchito yathu inayambanso kuyenda bwino ndipo anthu ambiri ankamvetsera uthenga wabwino. Pofika chakumapeto kwa chaka chautumiki cha 1961 m’dzikoli munali apainiya apadera 33.