Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Baibulo la Dziko Latsopano Ndi Lolimba Kwambiri

Baibulo la Dziko Latsopano Ndi Lolimba Kwambiri

A MBONI ZA YEHOVA amaona kuti Baibulo ndi buku lofunika kwambiri kuposa buku lina lililonse. Nthawi zonse, timaliphunzira komanso kuligwiritsa ntchito pophunzitsa ena za uthenga wabwino. (Mat. 24:14) Choncho, pokonza Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika limene linatuluka mu 2013, abale anayesetsa kuti Baibuloli likhale lokongola komanso lolimba kwambiri.

Choncho abale ogwira ntchito yosindikiza mabuku ku Wallkill, anapita kukakambirana za mapulani osindikiza Baibuloli ndi mkulu wa kampani ina yopanga mabuku. Abalewo atamuuza mapulaniwo mkuluyo anati: “N’zosatheka kupanga Baibulo limene mukufunalo.” Iye ananenanso kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti Mabaibulo ambiri amakhala okongola koma osalimba. Amangokonzedwa m’njira yakuti azioneka bwino akasiyidwa patebulo kapena pashelefu basi.”

Mabaibulo ena a Dziko Latsopano amene anasindikizidwa m’mbuyomu anali osalimba. Choncho abale amene amagwira ntchito yosindikiza mabuku ku Wallkill anayamba kufufuza njira yoti asindikize Mabaibulo olimba zedi, amene sangawonongeke ngakhale atamagwiritsidwa ntchito mwakathithi m’nyengo iliyonse. Atafufuza, anasindikiza Mabaibulo angapo omwe anawatumiza m’madera osiyanasiyana, n’cholinga choti abale akawagwiritse ntchito mongoyeserera.

Patatha miyezi 6, anaitanitsa Mabaibulo aja, kuti awaonenso. Mabaibulowo anali okwana 1,690. Ndipotu panachitika zinthu zina zimene zinayesadi kulimba kwa Mabaibulowa. Mwachitsanzo, Baibulo lina linapondedwa ndi galimoto, lina linaiwalidwa panja n’kunyowa ndi mvula usiku wonse, ndipo lina linamira m’madzi osefukira.

Pa nthawi imene ntchito yoyesa Mabaibulo inali m’kati mu 2011, tinagula makina apamwamba kwambiri osindikizira mabuku komanso okonzera zikuto, omwe tinawaika ku Ebina m’dziko la Japan ndiponso ku Wallkill. Cholinga chake sichinali kungosindikiza Mabaibulo ambiri chabe nthawi imodzi, koma kuti Mabaibulo omwe angasindikizidwe m’malo awiri onsewa azioneka mofanana.

Zikuto Zopindika

Poyamba zikuto zinkapindika

Chakumayambiriro kwa 2012, ntchito yosindikiza Mabaibulo a Dziko Latsopano amene anatulutsidwa mu 1984 inayambika ku Ebina, m’dziko la Japan komanso ku Wallkill. Mabaibulowa anapangidwa pogwiritsa ntchito zikuto zatsopano. Koma poikira zikuto, makina atsopanowa anagwiritsa ntchito guluu ndi kansalu kenakake, zinthu zomwe sanazigwiritse ntchito pa Mabaibulo omwe anayesedwa aja. Choncho kansalu kameneka ndi guluu zinachititsa kuti zikuto za Mabaibulowo zizipindika. Zonse zimene anthu ogwira ntchito yokonza Mabaibulowo anachita pofuna kuthana ndi vutoli zinakanika, moti ntchitoyi inaima.

Kampani ina inavomereza kuti nthawi zambiri zikuto zofewa zimapindika ndipo n’zovuta kuthana ndi vutoli. Koma abale sanasinthe kuti ayambe kusindikiza Mabaibulo a zikuto zolimba. Iwo anayesetsabe kufufuza njira yoti asindikizire Mabaibulo a zikuto zofewa, omwe sangawonongeke msanga. Patapita miyezi pafupifupi 4 akuyesera njira zosiyanasiyana, anapeza kansalu kena komanso guluu wamtundu wina. Iwo anatulukira zoti ngati atagwiritsa ntchito zinthu zimenezi, zikutozo zingakhale zokongola, zofewa ndiponso sizingapindike. Choncho ntchito yosindikiza Mabaibulo ija inayambikanso.

Makina osindikizira mabuku ku Wallkill

Panakonzedwa zoti Baibulo la Dziko Latsopano, lomwe linakonzedwanso lidzatulutsidwe pa October 5, 2013, pamsonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Pa August 9, 2013, mafailo a Baibulo anatumizidwa ku Wallkill ndi ku Ebina kudzera pa Intaneti kuti ntchito yosindikiza iyambike. Ndipo tsiku lotsatira, ntchitoyo inayamba. Abale anamaliza kusindikiza komanso kuikira chikuto Baibulo loyamba pa August 15. Kenako kwa masiku 7 otsatira, anthuwo anagwira ntchito mwakhama, masana ndi usiku. Ankafuna kuti asindikize, aike zikuto, ndiponso atumize Mabaibulo oposa 1,600,000, kuti munthu aliyense amene angakafike pamsonkhano wapachakawo alandire.

Mabaibulo atsopanowa ndi okongola komanso olimba zedi. Koma chomwe chikuchititsa kuti Mabaibulowa akhale apadera kwambiri ndi uthenga wake wosavuta kumva, womwe ungathandize anthu kudzapeza moyo wosatha. Patangotha tsiku limodzi chilandirireni Baibuloli, mlongo wina ku United States analemba kuti: “Panopa ndikumvetsa mawu a Mulungu mosavuta chifukwa ndikugwiritsa ntchito Baibulo latsopanoli.”