ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI
Malipoti Apadera a Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana
Ankagawira Anzawo Zimene Achita Dawunilodi
Ku Cuba, ndi anthu ochepa chabe amene amagwiritsa ntchito Intaneti. Makampani ena a mafoni anatsegula mashopu oti anthu azitha kugwiritsira ntchito Intaneti koma pa mtengo wokwera. Pofuna kuti abale azipindula ndi webusaiti ya jw.org, ofesi ya nthambi ya dzikolo inakonza zoti wofalitsa mmodzi azipanga dawunilodi zinthu zosiyanasiyana pa webusaitiyi kenako azigawira ena mumpingo. Zimenezi zikuthandiza kwabasi.
Anaona Kuti Nyumba ya Ufumu Ndi Yofunika Kuposa Foni
Ku Republic of Georgia kuli kamtsikana kena kazaka 10 dzina lake Teona, ndi ka mchemwali kake ka zaka 8 dzina lake Tamuna. Tiatsikanati tinkafuna kugula foni.
Ndiyeno agogo awo omwe anapuma pantchito, anakonza zoti mwezi uliwonse aziwapatsa ndalama, koma mwadzidzidzi agogowo anamwalira. Achibale anakonza zoti ndalama zomaliza zimene agogowo anafunika kulandira ziperekedwe kwa tiatsikana tija kuti tikagule foni. Koma ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu ya mumpingo wawo inali itatsala pang’ono kuyamba. Iwo ataganizira nkhaniyi analemba kalata kumpingo ndipo anati: “Paja kwangotsala milungu iwiri kuti ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu iyambe. Agogo athu aja ankafunitsitsa kuthandiza nawo pa ntchitoyi. Ndiye m’malo mogula foni, taganiza zoti tipereke ndalama zonse zimene anatipatsa kuti zithandize pa ntchitoyi. Chonde timangireni Nyumba ya Ufumu yabwino.”Kabaibulo ka Chitetamu
Pa January 17, 2014, mumzinda wa Dili ku Timor-Leste, M’bale Geoffrey Jackson wa M’bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu m’Chitetamu. Chilankhulochi chimalankhulidwa kwambiri m’dzikolo. Kale Mabaibulo a m’chilankhulochi ankasindikizidwa ndi tchalitchi cha Katolika ndipo ankakana kuwagulitsa kwa a Mboni za Yehova kapena wina aliyense amene akuphunzira ndi a Mboni. Baibulo lawolo linamasulira zinthu zambiri molakwika, anachotsamo zinthu zina, linali ndi mawu ovuta ndiponso mawu ena analembedwa molakwika. Baibulo la m’Chitetamu litatulutsidwa, mmishonale wina dzina lake Darren yemwe amakhala ku Timor-Leste anati: “Anthu ambiri akulikonda Baibuloli chifukwa linamasuliridwa molondola moti anthuwo
akufuna Baibulo lawolawo. Lili ndi zilembo zikuluzikulu choncho ndi losavuta kuwerenga makamaka kwa anthu amene alibe magetsi. Panopa anthu ambiri ayamba kuphunzira Baibulo.”“Yehova Amaona Kuti Ndine Wofunika”
Mu January 2014, ntchito yomasulira mabuku m’Chiromane inafika pachimake ku Macedonia. Tikutero chifukwa panakhazikitsidwa gulu lachikhalire la abale oti azimasulira mabuku. Ndipo panakonzedwanso kuti mabuku azimasuliridwanso m’zilembo za Chisiriliki. Zimenezi n’zothandiza kwambiri chifukwa mabuku ambiri a anthu olankhula Chiromane amalembedwa m’zilembo zimenezi.
Anthu ambiri olankhula Chiromane akusangalala chifukwa gulu lathu likusindikiza mabuku m’chilankhulo chawo. Mlongo wina anati: “Ndakhala ndikuganiza kuti anthu amaona kuti ndine wosafunika chifukwa
ndimalankhula Chiromane. Koma ndikusangalala kwambiri kuona kuti Yehova amaona kuti ndine wofunika ndipo wandipatsa mabuku a m’chilankhulo changa. Zimenezi zandithandiza kuti ndimuyandikire kwambiri.”“Ndikusangalala kudziwa kuti Yehova amaona kuti ndine wofunika ndipo wandipatsa mabuku a m’chilankhulo changa”
Nthambi ya ku United States Ikuyang’aniranso Mayiko Ena
Pa February 1, 2014, nthambi ya ku United States inayamba kuyang’anira ntchito yolalikira ku Jamaica ndi ku Cayman Islands. Tsopano nthambiyi iziyang’anira ntchito ya ofalitsa oposa 1.2 miliyoni a m’madera 50 adziko la United States, Bahamas, Bermuda, Virgin Islands, Puerto Rico ndiponso zilumba zotchedwa Turks and Caicos.
Apainiya a ku Japan
Abale ndi alongo ambiri ku Japan akuwonjezera zochita pa ntchito yolalikira. Zimenezi zachititsa kuti chiwerengero cha apainiya chiwonjezeke. Dzikoli lili pa nambala 4 pa mayiko omwe ali ndi apainiya ambiri. Pamene chaka cha utumiki cha 2014 chinkayamba, anthu 2,646 anayamba upainiya zimene zinawonjezera chiwerengero cha apainiya kufika pa 65,668. M’mwezi wa March 2014, hafu ya ofalitsa inachita nawo upainiya.