ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI
Mwambo Wotsegulira Ofesi ya Nthambi ku Sri Lanka
ABALE ndi alongo a ku Sri Lanka anavala zovala za kwawoko n’kukalandira alendo 130 ochokera m’mayiko 19. Alendowo anadzakhala nawo pa mwambo wotsegulira nthambi pachilumba chokongolachi. Panali ana amene anaimba nyimbo za Ufumu. Abale ndi alongo ankacheza, kuchita masewero, kudya ndiponso kumvetsera nyimbo zosangalatsa.
Loweruka pa January 11, 2014, anatsegulira ofesi ya nthambiyi komanso kuipereka kwa Yehova. Panali anthu okwana 893 ndipo nkhani zake zinkamasuliridwa m’zilankhulo zitatu. M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe lolamulira anafunsa gululo kuti: “Kodi mukufuna kupereka ofesi yatsopanoyi kwa Yehova Mulungu?” Anthuwo anavomera poomba m’manja kwa nthawi yaitali kwambiri.
Tsiku lotsatira, anthu, 7,701 anamvetsera pulogalamuyi ndipo M’bale Sanderson anakamba nkhani yolimbikitsa kwambiri. Ena mwa anthuwa anasonkhana m’malo ena ndipo ankachita kuonera pulogalamuyi m’masikirini. Kunena zoona abale ndi alongo m’madera osiyanasiyana a chilumbachi anali ndi mwayi woonera pulogalamuyi ndipo ‘anasangalala kwambiri.’ Iwo anaimba nyimbo za Ufumu komanso ankamva pamene anzawo kumalo enawo ankaimba.—