Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
Werengani nkhani zonena za a Mboni za Yehova padziko lonse komanso a Mboni za Yehova a ku Georgia.
Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Akudziwitsa a Mboni za Yehova padziko lonse kuti amawakonda komanso amawayamikira.
Tikuyesetsa Kuti Ntchito Yolalikira Padziko Lonse Izikhala Pamalo Oyamba
Kodi anthu amene poyamba ankatumikira pa Beteli achita chiyani kuti azikwanitsa utumiki wawo watsopano?
“Ndinu Aneba Abwino”
Pa May 7 ndi 8, 2016, anthu anaona malo ku Brooklyn Heights, New York ndipo izi zinathandiza kuti anthuwa adziwe zokhudza Beteli ya ku Brooklyn.
Msonkhano Watsopano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
Kuyambira January 2016, misonkhano ya mkati mwa mlungu inasintha.
Mapulogalamu a pa JW Broadcasting ‘Ndi Othandiza Komanso Olimbikitsa Kwambiri’
Mapulogalamu a JW Broadcasting anakhazikitsidwa mu 2014 ndipo tsopano akupezeka m’zilankhulo 90. Kodi amene amaonera mapulogalamuwa anena zotani?
Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi
Mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Kyrgyzstan ndi ku Armenia unali wosangalatsa kwambiri.
Lipoti la Milandu la 2016
Kodi a panali milandu yotani yokhudza a Mboni za Yehova mu 2016?
Malipoti Apadera —Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana
Nkhani za posachedwapa zonena za zimene a Mboni za Yehova achita ku Germany, Belize, Burundi, Nepal, Italy, Argentina, Uganda, Congo (Kinshasa) ndi ku Papua New Guinea.
Africa
Werengani zimene a Mboni ena anakumana nazo komanso zimene a Mboni za Yehova achita pa ntchito yophunzitsa Baibulo ku Ghana, Guinea-Bissau, Liberia, Malawi, Togo komanso Sierra Leone.
America
Zimene a Mboni ena anakumana nazo ku Brazil, Haiti, Mexico, United States ndi Venezuela.
Asia ndi Middle East
Zimene zinachitika ku Hong Kong, Mongolia, Philippines ndi Sri Lanka.
Europe
Werengani zimene zinachitikira a Mboni ena a ku Azerbaijan, Britain, Bulgaria, Georgia, Denmark, Hungary, Norway ndi Ukraine.
Oceania
Nkhani zochititsa chidwi zochokera ku Australia, Guam, New Caledonia, Papua New Guinea ndi Timor-Leste.
Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Georgia
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zachidule zokhudza dziko la Georgia, anthu ake, chikhalidwe chawo komanso chinenero chawo chomwe ndi chosiyana kwambiri ndi zinenero za mayiko olizungulira.
Anthu Oyambirira Kuphunzira Choonadi
Anthu ena omwe anaphunzira choonadi m’mayiko ena, anapita m’dziko la Georgia ndipo anayamba kulalikira.
Misonkhano Inawathandiza Kukhala Ndi Chikhulupiriro Cholimba
Kodi misonkhano komanso mabuku achijojiya zinathandiza bwanji kuti anthu ambiri aphunzire choonadi ku Georgia?
Ndinkafunitsitsa Nditasintha Zochita Zanga
Atamaliza kugwira ntchito ya usilikali, a Davit Samkharadze anapempha Mulungu kuti awathandize kusintha moyo wawo. Tsiku lotsatira a Davit anakumana ndi a Mboni za Yehova.
Ndinapempha Yehova kuti Anditsogolere
M’bale Tamazi Biblaia anapempha Yehova kuti amutsogolere asanasamukire ku Jvari.
“Zinthu Zonse N’zotheka kwa Mulungu”
Mlongo Natela atapemphedwa kuti athandize nawo posindikiza mabuku othandiza kuphunzira Baibulo ku Georgia, anakumana ndi vuto lina.
Baibulo la M’Chijojiya
Mipukutu ya Baibulo yoyambirira ya Chijojiya inali ya m’zaka za m’ma 400 C.E. kapena zakazi zisanafike.
“Mulungu Ndiye Anakulitsa” —1 Akor. 3:6.
Kungochokera pamene dziko la Georgia linalandira ufulu wodzilamulira anthu ambiri anaphunzira choonadi.
Anaphunzitsa Ena Kuti Akhale Akulu ndi Atumiki Othandiza
Ulamuliro wachikomyunizimu utangotha, kodi a Mboni za Yehova anatani kuti ayambirenso kuchita misonkhano yampingo, misonkhano ikuluikulu komanso ntchito yomasulira mabuku?
Mwamuna Wanga Sankafuna Kusiya Kuwerenga
A Badri Kopaliani ankafunitsitsa kuwerenga Baibulo limene analandira monga mphatso moti anatenga tchuthi kwa masiku angapo kuti amalize kuliwerenga.
Munali Kuti Nthawi Yonseyi?
Chisanathe chaka atangobatizidwa, a Artur Gerekhelia anachoka kwawo komanso anasiya bizinezi yotentha n’kusamukira kumene kunkafunika olalikira ambiri.
Ndinkaganiza Kuti Zinthu Zikundiyendera
Mlongo Madona Kankia anali munthu wotchuka m’chipani cha chikomyunizimu ku Georgia koma kenako anasankha kuyamba moyo watsopano.
Chikondi Chenicheni Sichitha
Pa nthawi imene kunali nkhondo ku Abkhazia, M’bale Igor Ochigava ndi M’bale Gizo Narmania anathandiza a Mboni za Yehova anzawo komanso anthu ena kupeza chakudya ndiponso anawalimbikitsa ndi uthenga wabwino.
Ndinaona Ndi Maso Anga Zimene Baibulo Limanena
Chifukwa chakuti ankadana ndi a Mboni za Yehova, a Pepo anachita zimene mayi awo anawauza kuti: “Kandimverere anakanena za m’maluwa. Ungachite bwino kucheza nawo wekha kuti umvetse zimene ndikunenazi.”
Anadalitsidwa ‘pa Nthawi Yabwino ndi pa Nthawi Yovuta.’ —2 Tim. 4:2.
M’zaka zimenezi, chiwerengero cha a Mboni za Yehova chinawonjezeka. Koma kenako anthu ena anayamba kuwatsutsa.
Sanasiye Kutumikira Yehova Ngakhale Kuti Ankaopsezedwa
Kodi anthu ankaona bwanji nkhanza zimene anthu ena ankachitira a Mboni za Yehova ku Georgia?
“Ichi Ndi Cholowa cha Atumiki a Yehova” —Yes. 54:17.
Yehova anadalitsa ofalitsa amene ankalalikira mwakhama.
Anakumbukira Mlengi Wawo Wamkulu
Mpainiya mmodzi pa apainiya atatu alionse a ku Georgia ali ndi zaka 25 kapena kuchepa.
Anthu Ambiri Olankhula Chikadishi Akuphunzira Choonadi
Anthu oopa Mulungu akusangalala kumva uthenga wa m’Baibulo m’chinenero chawo.
Akhristu Oona Amasonyeza Chikondi Chenicheni
Agogo awiri anaona kuti a Mboni za Yehova anzawo anawasonyeza chikondi.
Zaka 100 Zapitazo —1917
Ophunzira Baibulo ambiri ankaona kuti chaka cha 1917 ndi chimene anayesedwa komanso kupetedwa. Ngakhale kuti anakumana ndi mavutowa, anthu okhulupirika anapitirizabe kugwira ntchito za Ufumu.
Ziwerengero Zonse za 2016
Lipoti la pachakali likusonyeza zimene a Mboni za Yehova achita m’chaka cha 2016.
Lipoti la Chaka cha Utumiki cha 2016 la Mboni za Yehova Padziko Lonse
Lipotili likunena za abale ndi alongo, nthambi, mayiko, anthu amene anapezeka pa Chikumbutso ndi zina.