Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GEORGIA | 1991-1997

Anaphunzitsa Ena Kuti Akhale Akulu ndi Atumiki Othandiza

Anaphunzitsa Ena Kuti Akhale Akulu ndi Atumiki Othandiza

Joni Shalamberidze with Tamazi Biblaia in the early 1990’s

Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1990, mipingo yambiri inali ndi mkulu kapena mtumiki wothandiza mmodzi. Nthawi zambiri mipingo inkapangidwa ndi timagulu tingapo tomwe tinkasonkhana m’malo osiyanasiyana. Zimenezi zinkachitika chifukwa magulu ena ankakhala m’madera komanso m’midzi yakutali kwambiri.

M’bale Joni Shalamberidze ndi M’bale Pavle Abdushelishvili anatumizidwa ku Telavi, mzinda womwe unali m’chigawo cha Kakheti kuti akathandize mpingo wa kumeneko. Abalewa anali atatumikirapo m’madera ena akutali asanapite kumeneku. Mpingo wa ku Telavi unali ndi ofalitsa 300 koma kunalibe mkulu ngakhale mmodzi. Mpingowu unapangidwa ndi magulu 13 ndipo ankakumana m’madera osiyanasiyana.

M’bale Pavle Abdushelishvili

Abale aja atafika m’tauniyi, anazindikira kuti abale ndi alongo a mumpingowo anali ndi vuto lina. M’bale Shalamberidze anati: “Abale ambiri anali ndi minda yaikulu zedi ndipo ena ankachita ulimi wa mphesa. Popeza anthu ambiri a m’madera akumidzi amakonda kuthandizana akamakolola, abale ndi alongo ankakhala nthawi yaitali ali ndi anthu osakonda Yehova.”1 Akor. 15:33.

M’bale Shalamberidze ndi M’bale Abdushelishvili anaganiza zouza abalewo kuti akamafuna kuti ena awathandize kukolola, azipempha abale ndi alongo. Ankaona kuti zimenezi zithandiza kuti abale ndi alongowo azilimbikitsana akamagwira ntchitoyo. (Mlal. 4:9, 10) M’bale Shalamberidze anati: “Zimenezi zinachititsa kuti abale ndi alongo azigwirizana kwambiri.” Pamene abale awiriwa ankachoka ku Kakheti, patatha zaka zitatu, mumpingowu munali akulu 5 komanso atumiki othandiza okwana 12.

Misonkhano Inathandiza Kuti Azilalikira Mogwira Mtima

Ntchito yathu inali yoletsedwa m’dziko la Georgia mpaka chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1990. Pa nthawi imeneyi abale ndi alongo ankakumana m’timagulu ting’onoting’ono. Pamisonkhano imeneyi ankachita Phunziro la Buku la Mpingo komanso Phunziro la Nsanja ya Olonda basi. Misonkhanoyi inawathandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Komabe, vuto linali lakuti misonkhanoyi sikanawathandiza kuti azilalikira mogwira mtima.

Vuto limeneli linatha ulamuliro wachikomyunizimu utangotha. Pa nthawiyi abale ankalambira Yehova momasuka moti gulu la Yehova linakonza zoti mipingo izichita Sukulu ya Utumiki wa Mulungu komanso Msonkhano wa Utumiki mlungu uliwonse.

Mlongo Naili Khutsishvili, ndi mchemwali wake Lali Alekperova, saiwala zimene zinkachitika pamisonkhano imeneyi. Mlongo Alekperova anati: “Titamva zoti tiyamba kuchita misonkhano imeneyi, mitima yathu inkangoti phaphapha. Tinkafunitsitsa titaona alongo nawonso akukamba nkhani pamisonkhano.”

Mlongo Khutsishvili ananena kuti: “Ndikukumbukira m’chitsanzo china, mwininyumba akuwerenga nyuzipepala papulatifomu ndipo anamva anthu akugogoda. Kenako anauza anthuwo kuti alowe, ndipo alongo awiri anatulukira kudzera pakhomo lolowera m’holoyo n’kupita papulatifomu.” Mlongo Alekperova anawonjezera kuti: “Nthawi zina abale ndi alongo ankachita zinthu zomwe sungaziyembekezere. Komabe, zitsanzo zimenezi zinatithandiza kuti tizilalikira mogwira mtima.”

Pankafunika Mabuku Ambiri

Kwa zaka zambiri, abale angapo a ku Georgia ankasindikiza mabuku pamanja pogwiritsa ntchito zipangizo zing’onozing’ono ndipo ankachita zimenezi m’nyumba zawo. Koma kenako chiwerengero cha abale ndi alongo chinayamba kuchuluka ndipo mabuku anayamba kufunika ambiri. Abale ataona zimenezi anaganiza zoyamba kusindikiza mabuku pogwiritsa ntchito makampani ena omwe akanasindikiza mabuku athu pa mtengo wosaboola m’thumba.

Abale ankadula zilembo za m’nyuzipepala n’kuzimata pachikuto cha buku kapena magazini yachingelezi, kuti akonze magazini yachijojiya yoti akaisindikize

Abalewa ankachita khama zedi akamakonza magazini kapena buku loti likasindikizedwe. Choyamba ankamasulira magaziniyo n’kutaipa mawuwo pamapepala mofanana ndi magazini yachingelezi. Akatero ankadula zithunzi za m’magazini yachingelezi ija ndipo ankazimata m’mipata yomwe anasiya potaipa. Kenako, ankadula zilembo zokongola za m’nyuzipepala n’kuzimata mwadongosolo pachikuto cha magaziniyo. Zikatero ankatenga magaziniyo n’kupita nayo kukampani yosindikiza mabuku kuti ikasindikizidwe.

Magazini oyambirira achijojiya omwe anasindikizidwa

Abale anagula makompyuta atangoyamba kufala. Abale awiri achinyamata, omwe mayina awo ndi Levani Kopaliani ndi Leri Mirzashvili, anakaphunzira mmene angagwiritsire ntchito makompyutawa. M’bale Leri anati: “Poyamba zinkativuta kwambiri kugwiritsa ntchito kompyuta. Koma Yehova anatithandiza zedi moti pasanapite nthawi tinayamba kutha kutaipa komanso kuika zithunzi m’magazini athu.”

N’zoona kuti abalewa ankakumana ndi mavuto akamagwira ntchito imeneyi. Komabe abale ndi alongo a m’dziko la Georgia anasangalala kwambiri chifukwa tsopano ankalandira magazini okhala ndi zithunzi zakalala. Pasanapite nthawi, anthu ofuna mabuku athu anayamba kuchuluka, moti zinali zovuta kuti abale azikwanitsa kusindikiza mabuku okwanira. Pa nthawi imeneyi m’pamene gulu la Yehova linathandiza abale kuti ayambe kusindikiza mabuku okwanira.

Zinthu Zinayamba Kuyenda Bwino

Abale ndi alongo a m’dziko la Georgia anali ndi mwayi wokumana ndi abale oyendera nthambi ochokera ku Germany pamsonkhano wa mayiko wa m’chaka cha 1992. Msonkhanowu unachitikira ku St. Petersburg m’dziko la Russia. M’bale Genadi Gudadze anati: “Abalewo anatifotokozera mmene ntchito yomasulira mabuku imayendera. Anatiuzanso kuti adzatumiza abale oti adzatiphunzitse ntchito yomasulira.”

Kusindikiza mabuku athu m’Chijojiya sinali nkhani yamasewera. Chijojiya chili ndi zilembo zosiyana kwambiri ndi zilembo za ma afabeti ena. Komanso pulogalamu ya MEPS, yomwe timagwiritsira ntchito pokonza mabuku athu kuti azioneka ofanana ndi achingelezi, inalibe afabeti yachijojiya. Ndiyeno, abale anayamba kujambula zilembo za afabeti yachijojiya n’cholinga choti ntchito yokonza komanso kusindikiza mabuku isamavute.

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1970, banja la a Datikashvili, lomwe linkakhala m’dziko la Georgia, linasamukira ku United States. Mwana mmodzi wa m’banjali, dzina lake Marina, anaphunzira choonadi. Mwana ameneyu anathandiza kwambiri pamene abale ku Beteli ya ku Brooklyn anayamba kujambula zilembo za afabeti yachijojiya kuti aziike mu pulogalamu ya MEPS. Atamaliza kujambula zilembozi, abale a ku ofesi ya nthambi ya ku Germany anasindikiza timapepala tina komanso kabuku kakuti, “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.”

Anathandizidwa pa Ntchito Yomasulira Mabuku

Mu 1993, M’bale Michael Fleckenstein ndi mkazi wake Silvia, anafika ku Tbilisi ndipo ankachokera ku Germany. M’baleyu anapita ku Georgia kuti akayambitse ntchito yomasulira. M’bale Michael ananena kuti: “Ndimakumbukirabe msonkhano umene unachitika ku St. Petersburg. Patapita chaka ndi miyezi 6 titafika ku Tbilisi, tinadabwa kwambiri abale akutisonyeza kagulu ka abale amene ankagwira bwinobwino ntchito yomasulira.”

Leri Mirzashvili, Paata Morbedadze ndi Levani Kopaliani akugwira ntchito m’dipatimenti yomasulira mabuku ku Tbilisi mu 1993

Patangopita miyezi yochepa, kagulu ka anthu 11 kankagwira ntchito yomasulira m’nyumba ina yaing’ono. Maphunziro amene abale omwe amagwira ntchito yomasulira anaphunzitsidwa ndi gulu la Yehova, anathandiza kuti abale ndi alongo azilandira mabuku pa nthawi yake.

Anapitirizabe Kutumiza Mabuku Ngakhale Kuti Zinthu Sizinali Bwino

Ulamuliro wachikomyunizimu utatha, panayamba kuchitika nkhondo zapachiweniweni m’mayiko onse omwe anali pansi pa ulamuliro wa Soviet Union, kuphatikizaponso dziko la Georgia. Pa nthawi imeneyi, ulendo wopita mayiko ena unkakhala woopsa.

M’bale Zaza Jikurashvili ndi M’bale Aleko Gvritishvili (ali limodzi ndi akazi awo). Abalewa ankanyamula mabuku pa nthawi yovuta kwambiri m’dziko la Georgia

Mwachitsanzo, mwezi wa November 1994, M’bale Aleko Gvritishvili akupita m’dziko lina ndi abale ena awiri anakumana ndi kagulu ka anthu komwe kanali ndi mfuti. Anthuwa anawaimitsa n’kuwauza kuti atsike m’galimotoyo. M’bale Gvritishvili ananena kuti: “Anthuwa anapsa mtima kwambiri ataona mabuku athu. Anatilamula kuti tikhale pamzere ngati kuti akufuna kutipha. Pa nthawiyi tinapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima. Patapita maola awiri, mmodzi mwa anthuwa ananena kuti, ‘Tengani mabuku anuwa muzipita. Mukadzabweranso tidzawotcha galimotoyi ndiponso tidzakuonetsani zoopsa.’”

Abale athu anapitirizabe kutumiza mabuku ngakhale ankaopsezedwa chonchi. M’bale Zaza Jikurashvili, yemwe anagwira ntchito yotamandika zedi ponyamula mabuku kupita nawo m’dziko la Georgia, anati: “Tinkayesetsa kuchita khama chifukwa tinkaona kuti mabukuwa ndi ofunika kwambiri kwa abale athu. Timathokoza kwambiri akazi athu chifukwa ankatithandiza kwambiri.”

M’bale Gvritishvili ananena kuti: “Abale ambiri amene ankanyamula mabuku kupita nawo ku Georgia anali okwatira.” Ndiye n’chiyani chimene chinkachititsa abale amenewa kuti asiye mabanja awo kunyumba, n’kumagwira ntchitoyi pa nthawi yomwe zinthu zinali zovuta kwambiri? M’baleyu anapitiriza kunena kuti: “Tinkachita zimenezi chifukwa chokonda Yehova. Tinkaona kuti ndi njira ina yosonyezera kuti timayamikira kwambiri chifukwa cha zimene amatichitira. Tinkafunanso kutsanzira Yehova pa nkhani yokonda abale ndi alongo athu omwe ankadalira mabukuwo.”

Abale amenewa timawataira kamtengo chifukwa sanasiye kunyamula mabuku ngakhale pa nthawi imene kuchita zimenezi kunali koopsa kwambiri. M’kupita kwa nthawi, abale anatulukira njira zina zabwino zomwe ankadutsa akamakatenga mabuku ku Germany.

Msonkhano Wachigawo Unalimbikitsa Kwambiri Abale ndi Alongo

M’chaka cha 1995, zinthu zinasintha m’dziko la Georgia ndipo zachipwirikiti zija zinatha. Zimenezi zitachitika, abale anakonza zoti pachitike misonkhano yachigawo. Misonkhanoyi inachitika chakumapeto kwa chaka cha 1996, ndipo anthu okwana 6,000 ochokera m’madera osiyanasiyana a m’dziko la Georgia anafika pamsonkhanowu. Misonkhanoyi inachitikira ku Gori, Marneuli ndi Tsnori.

Abale akuchita msonkhano wachigawo ku Gori mu 1996

Anthu amene anasonkhana ku Gori saiwala zimene zinachitika pamsonkhanowu. Abalewa ankaganiza zochitira msonkhanowu muholo ina yomwe anachitiramo Chikumbutso. Koma malowa anali ochepa kwambiri chifukwa ankayembekezera kuti padzabwera anthu oposa 2,000. Ankaona kuti ngati atadzachitira muholo imeneyi adzapanikizana kwambiri. Choncho anaganiza zopeza malo ena ndipo anawapezadi pamalo ena okongola kwambiri omwe anali paphiri lina.

M’bale Kako Lomidze, yemwe ankatumikira m’Komiti ya Msonkhano Wachigawo, anati: “Msonkhanowu utangotha, abale ndi alongo anasangalala kwambiri kucheza ndiponso kuimbira limodzi nyimbo. Zimenezi zinasonyeza kuti abale ndi alongo amagwirizana kwambiri chifukwa cha chikondi.”Yoh. 13:35.

Oyang’anira Madera Anathandiza Kuti Mipingo Ipitirize Kukula

Kungochokera mu 1996, abale anakonza zoti oyang’anira dera aziyendera mipingo ya m’dzikoli kwa mlungu wonse wathunthu. Pa nthawiyi panali oyang’anira dera ochepa, choncho anasankha abale ena kuwonjezera pa abale amene ankachita kale utumikiwu, m’zigawo zonse za dziko la Georgia.

‘Ntchito zachikhulupiriro’ za abale amenewa, zinathandiza kwambiri kuti mipingo ikule. Zinathandizanso kuti abale a m’mipingo yosiyanasiyana azitsatira malangizo a gulu la Yehova. (1 Ates. 1:3) Kungochokera mu 1990 kufika mu 1997, chiwerengero cha ofalitsa chinakula kwambiri. Mwachitsanzo, mu 1990 m’dziko la Georgia munali ofalitsa 904. Pofika mu 1997, m’dzikoli munali ofalitsa 11,082 omwe ankalalikira uthenga wabwino.

Khama limene abale ndi alongo akale anasonyeza linathandiza kuti uthenga wabwino ufike paliponse m’dziko la Georgia. Koma sikuti Yehova analekera pomwepa podalitsa abale ndi alongo a m’dziko la Georgia.