Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GEORGIA

Chikondi Chenicheni Sichitha

Chikondi Chenicheni Sichitha

M’bale Ochigava: Ineyo ndi M’bale Narmania tinali m’kagulu kamene kankasonkhana m’tauni ya Tkvarcheli mumzinda wa Abkhazia. Ndiye popeza mpingo umene kagulu kathuko kankasonkhana unali mumzinda wa Jvari, womwe uli pamtunda wa makilomita 85, ineyo ndinkapita kumeneko mwezi uliwonse kuti ndikatenge mabuku. Mu 1992, ulamuliro wa Soviet Union utangotha kumene, chigawo cha Abkhazia chinkafuna kukhala dziko lodziimira palokha. Zimenezi zinachititsa kuti pachitike nkhondo yodetsa nkhawa ya pakati pa asilikali a dziko la Georgia ndi gulu lomwe linagalukira boma. Nkhondoyi inachititsa kuti anthu akhale pa mavuto oopsa.

M’bale Gizo Narmania ndi M’bale Igor Ochigava

Abale awiriwa anathandiza abale ndi alongo pa nthawi imene ku Abkhazia kunkachitika nkhondo.

M’bale Narmania: Ndinabatizidwa ndili ndi zaka 21 ndipo pa nthawiyi kunali kutangotsala chaka chimodzi kuti nkhondo iyambe. Nkhondoyo itayamba, abale anasokonezeka kwambiri chifukwa cha mantha. Koma M’bale Ochigava, anali mkulu wabwino kwambiri moti ankatilimbikitsa. Ankakonda kunena kuti: “Panopa m’pamene anthu akufunika kulimbikitsidwa kwambiri. Ndipo n’zotheka kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba ngati sitisiya kulalikira.” Choncho, tinayamba kulalikira anthu amene tinkakhala nawo pafupi n’cholinga choti tiwalimbikitse ndi uthenga wabwino wa m’Baibulo. Koma tinkachita zimenezi mosamala kwambiri.

M’bale Ochigava: Nkhondoyi inachititsa kuti tisinthe njira yomwe tinkadutsa tikamapita komanso tikamachokera kotenga mabuku ku Jvari. Ndiye popeza ndinakulira m’derali, sindinavutike kupeza njira ina yomwe inkadutsa m’minda ya tiyi komanso m’mapiri. Komabe kudutsa njira imeneyi kunalinso koopsa chifukwa ndikanakumana ndi magulu a asilikali kapena ndikanatha kuponda bomba. Sindinkafuna kuika moyo wa abale anga pachiswe, choncho ndinaganiza zomapita ku Jvari ndekha kamodzi pa mwezi. Ndimaona kuti Yehova anandithandiza kwambiri chifukwa nthawi zonse ndinkakwanitsa kukatenga mabuku omwe anathandiza kuti abale ndi alongo apitirizebe kukonda Yehova.

Ngakhale kuti nkhondo sinafike m’dera lakwathu la Tkvarcheli, komabe inatikhudza kwambiri chifukwa misewu inatsekedwa. Zimenezi zinachititsa kuti tivutike koopsa. Pamene nyengo yozizira inkayamba, chakudya chinayamba kusowa ndipo tinkada nkhawa kuti tikhoza kufa ndi njala. Mitima yathu inakhala m’malo titamva zoti abale athu a ku Jvari akonza zoti atitumizire thandizo la chakudya.

M’bale Narmania: Tsiku lina M’bale Ochigava anatipempha ngati zinali zotheka kuti chakudya chimene chinkachokera ku Jvari chidzafikire kwathu. M’baleyu anatiuza kuti akupita ku Jvari kuti akatenge chakudyacho ndipo ankafuna kuti chizidzagawidwira panyumba pathupo. Titamva zimenezi tinayamba kuda nkhawa kwambiri chifukwa tinkaona kuti zigawenga zikhoza kumuchita chipongwe. Chinanso chimene chinkatidetsa nkhawa n’choti ankafunika kudutsa njira imene kunkakhala mbava ndiponso magulu a asilikali komanso ankayenera kudutsa malo achipikisheni angapo.Yoh. 15:13.

Tinawombera kuphazi M’bale Ochigava atabwerera bwinobwino patapita masiku 5. M’baleyu anayenda bwino kwambiri ndipo chakudya chomwe anakatenga ku Jvari chinatisunga kwa miyezi ingapo. Pa nthawi yovutayi, tinaonadi kuti chikondi chimene Akhristu enieni amasonyeza sichitha.1 Akor. 13:8