Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akulalikira pamalo ena okwerera zikepi ku Khulo

GEORGIA

“Ichi Ndi Cholowa cha Atumiki a Yehova”—Yes. 54:17.

“Ichi Ndi Cholowa cha Atumiki a Yehova”—Yes. 54:17.

ABALE ndi alongo a ku Georgia akuyesetsa kulalikira uthenga wabwino ndipo Yehova akudalitsa khama lawo. Zimenezi zachititsa kuti uthenga wabwino ulalikidwe pafupifupi paliponse m’dziko la Georgia.

Ofalitsa akukonzekera kupita kolalikira ku Ushguli. Mzindawu uli m’dera lokwera kwambiri mamita 2,200

Zaka zapitazi, apainiya komanso abale ndi alongo odzipereka akhala akulalikira m’madera amene salalikidwa kawirikawiri. Abalewa amalalikira m’madera amapiri komanso m’midzi yakutali komwe ndi kovuta kufikako. Popita m’maderawa amayendera galimoto zamphamvu kwambiri ndipo nthawi zina amakwera zikepi zoyenda panthambo zamagetsi.

Akulalikira ku Svaneti

Kungoyambira m’chaka cha 2009, ofesi ya nthambi ya ku Georgia yakhala ikudziwitsa abale za mipingo imene ili ndi magawo omwe kulibiretu ofalitsa. Ofesiyi inapempha abale ndi alongo kuti azikalalikira m’madera amenewa. Koma kuti ofalitsa asamukire m’maderawa amafunika kusintha zambiri pa moyo wawo.

Mlongo Ana ndi mwamuna wake Temuri Bliadze

Mwachitsanzo, M’bale Temuri Bliadze ndi mkazi wake Ana anamva zoti kudera lamapiri la Ajaria kukufunika olalikira ambiri. Pa nthawiyi anali atangokwatirana kumene komanso atagula malo oti amangepo nyumba. Komabe anaona kuti uwu ndi mwayi wawo woti akatumikire kugawo lomwe kunkafunika ofalitsa ambiri.

Banjali linaganiza zopita kuderali n’kukakhalako kwa mlungu umodzi. M’bale Temuri anafotokoza zimene anaona atangofika m’derali. Anati: “Abale ndi alongo amene tinawapeza kuderali ankayenda wapansi mitunda italiitali kuti akalalikire kumidzi yosiyanasiyana. Ndiye popeza tinali ndi galimoto yamphamvu, tinaona kuti ithandiza kwambiri pa ntchito yolalikira kuderali.”

Mkazi wake Ana ananenanso kuti: “Sizinali zophweka kusiyana ndi abale athu komanso mpingo umene tinauzolowera. Koma tinaona kuti Yehova atidalitsa kwambiri tikasamukira kuderali.” Tsopano patha zaka zitatu M’bale Temuri ndi mkazi wake akutumikira m’kagulu ka m’tauni ya Keda, yomwe ili ku Ajaria.

Apainiya Anapeza Njira Yopezera Ndalama

Apainiya apadera akanthawi omwe anatumizidwa kumadera amene kunali ofalitsa ochepa, anathandiza kwambiri. Nthawi imene anauzidwa kuti akatumikire m’maderawa itatha, apainiya ambiri anaganiza zokhalabe komweko kuti athandize anthu omwe ankaphunzira nawo Baibulo.

Alongo awiri, omwe onse mayina awo ndi Khatuna, anatumizidwa m’tauni ya Manglisi. M’tauniyi munalibe wa Mboni aliyense ndipo apainiyawa analalikira anthu ochuluka zedi. Mwachitsanzo, mwezi woyamba anachititsa maphunziro a Baibulo 9, mwezi wachiwiri 12, mwezi wachitatu 15 ndipo wa 4 anachititsa maphunziro 18. Nthawi yawo yokhala kuderali itatha, alongowa anaganiza zokhalabe kuderalo kuti apitirizebe kuthandiza anthuwo.

Ndiye popeza sankagwira ntchito, anafunika kupeza njira yopezera zinthu zofunikira pa moyo. Anthu ambiri a ku Manglisi amakonda mankhwala enaake opangidwa ndi zibalobalo za mitengo ya paini. Amakhulupirira kuti mankhwala amenewa angathandize kuti munthu akhale wathanzi. Choncho, alongowa ankatolera zibalobalo zaziwisi za mitengoyi n’kupanga mankhwalawa n’kumakawagulitsa kumsika.

Koma tsiku lina, mayi wina yemwe ankaphunzira naye Baibulo anawabweretsera anapiye nkhuku. Mayiyo anawauza kuti amaweta nkhuku. Ndiye nkhuku yake ina inaikira mazira pamalo ena n’kuswa iye osadziwa. Tsiku lina anangoiona ikubwera ndi anapiye. Popeza sankafuna kuti akhalenso ndi nkhuku zina, anaganiza zongopereka anapiyewo kwa alongowa. Alongowo anangoti laponda la mphawi moti anayamba kuweta nkhuku.

Mmodzi mwa alongowa anati: “Takhala kuno kwa zaka 5 ndipo nthawi yonseyi Yehova, abale ndi alongo komanso anthu ena omwe tikuphunzira nawo Baibulo atithandiza kwambiri.” Panopa m’tauniyi muli kagulu ka abale ndi alongo omwe amalalikira mwakhama.

Mlongo Khatuna Kharebashvili akulalikira ndi Mlongo Khatuna Tsulaia ku Manglisi

Amachita Upainiya M’gawo la Chinenero China

Zaka zapitazi, anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana akhala akubwera m’dziko la Georgia. Apainiya ambiri anaona kuti akhozanso kumalalikira anthu amenewa. Choncho anayamba kuphunzira zinenero zomwe anthuwo amayankhula monga Chiarabu, Chiazebaijani, Chitchainizi, Chingelezi, Chiperisiya komanso Chitekishi.

Apainiya ambiri akusonkhana ndi magulu komanso mipingo ya zinenero zina ndipo ena asamukira m’mayiko omwe kukufunika ofalitsa ambiri. Mwachitsanzo, M’bale Giorgi ndi M’bale Gela, anasamukira m’dziko lina ali ndi zaka za m’ma 20. M’bale Giorgi anati: “Tinkafuna kumupatsa Yehova zinthu zamtengo wapatali. Tinaganiza kuti njira ina yochitira zimenezi ndi kusamukira kudziko komwe kulibe ofalitsa ambiri.”

M’bale Gela amaona kuti anachita bwino kwambiri kusamukira kudziko lina. Iye anati: “Kutumikira monga mkulu m’dziko limeneli kwandiphunzitsa zambiri. Ndimaona kuti ndili ndi mwayi waukulu chifukwa Yehova amandigwiritsa ntchito kuthandiza ‘ana a nkhosa.’”Yoh. 21:17.

M’bale Giorgi anawonjezera kuti: “Sikuti tinangoyenda moyera, komabe sitinalole kuti mavuto amene tinkakumana nawo atisokoneze n’kuyamba kuganiza zobwerera kwathu. Tinkaona kuti tikungochita zimene tinkayenera kuchita basi.”

Mbale wina, yemwenso dzina lake ndi Gela, anapita kukatumikira m’dziko la Turkey kwa zaka zingapo. Iye anati: “Nditangofika m’dzikoli, ndinavutika kwambiri kuphunzira chinenero chatsopano moti sindinkasangalala. Koma nditachidziwa bwino, ndinayamba kucheza bwinobwino ndi abale ndi alongo komanso kulalikira. Zimenezi zinachititsa kuti ndizisangalala kwambiri.”

Mlongo Nino wachita upainiya ku Istanbul m’dziko la Turkey kwa zaka zoposa 10 ndipo anati zaka zimene wakhala m’dzikoli ndi zosaiwalika. Iye ananena kuti: “Ndimaona kuti Yehova wandithandiza kungochokera pamene ndinafika m’dzikoli. Ukamachita upainiya m’dziko lina, tsiku lililonse umakumana ndi zinthu zosangalatsa zofanana ndi zimene zimatchulidwa mu Buku Lapachaka.”