Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Abale ali pamsonkhano womwe unachitikira ku Tbilisi mu 1992

GEORGIA | 1991-1997

“Mulungu Ndiye Anakulitsa”—1 Akor. 3:6.

“Mulungu Ndiye Anakulitsa”—1 Akor. 3:6.

M’bale Genadi Gudadze anatumikirapo monga woyang’anira dera chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1990

DZIKO la Georgia linalandira ufulu wodzilamulira mu 1991, pamene ulamuliro wa Soviet Union unatha. Komabe anthu a m’dzikoli ankakhala movutika kwambiri chifukwa cha kusintha kumeneku komanso zipwirikiti zomwe zinayamba chifukwa cha kusemphana maganizo pa nkhani zandale. M’bale Genadi Gudadze, yemwe anali woyang’anira dera pa nthawi imeneyo, ananena kuti anthu ankakhala pamzere tsiku lonse kuti agule buledi.

Pa nthawi imeneyi, abale ndi alongo ankalalikira anthu amene ankadikira kugula buledi pamzere. M’bale Gudadze ananenanso kuti: “Zikuoneka kuti anthu ambiri ankamvetsera uthenga wathu pa nthawiyi ndipo tinalandira makalata ambiri a anthu omwe ankafuna kuphunzira Baibulo.”

Misonkhano ikatha, abale ankalengeza mayina komanso maadiresi a anthu amene ankafuna kuphunzira Baibulo. Ndiyeno abale ndi alongo ankadzipereka kuti aziphunzira ndi anthuwo.

Akulalikira anthu amene ali pamzere, omwe akufuna kugula buledi m’zaka za m’ma 1990

M’bale Levani Sabashvili, yemwe anali mkulu ku Tbilisi, ananena kuti panali banja lina lomwe linapempha kuti liziphunzira Baibulo. Iye anati: “Palibe amene anadzipereka kuti aziphunzira ndi banjali. Izi zinachitika chifukwa choti banjali linkakhala kutali kwambiri komanso abale ndi alongo anali kale ndi maphunziro ambiri a Baibulo.”

Patatha miyezi ingapo, banjali linatumizanso kalata ina. Ataona kuti sanayankhidwenso kalata imeneyi, anatumiza kalata yachitatu n’kuchenjeza abalewo kuti akapanda kutumiza munthu woti azikawaphunzitsa Baibulo, akhala ndi “mlandu wa magazi.” (Mac. 20:26, 27) M’bale Levani ananena kuti: “Inali nthawi yokondwerera chaka chatsopano, ndipo pa nthawiyi sitinkakonda kulalikira. Koma tinaona kuti sitichita bwino ngati titalephera kupitako.”

Banja limeneli, lomwe mayina awo anali a Roini ndi akazi awo a Nana Grigalashvili, sanakhulupirire ataona M’bale Levani ndi m’bale wina atafika kunyumba kwawo. Ngakhale kuti kunja kunkazizira kwambiri, tsiku lomwelo anayamba kuphunzira Baibulo ndipo patapita nthawi, anabatizidwa. Panopa, a Roini ndi akazi awo, pamodzinso ndi ana awo akuchita upainiya.

Sanatope Kufufuza Anthu Achidwi

Anthu amene anamva uthenga wabwino anasangalala kwambiri ndi zimene anaphunzira m’Baibulo. Anthuwa ankadzipereka kwambiri kulalikira komanso kugwiritsa ntchito mphamvu ndi zinthu zawo pothandiza ena. Mwachitsanzo, a Badri ndi a Marina Kopaliani ankayenda m’madera akutali osiyanasiyana kuti akathandize anthu amene ankafuna kumva uthenga wabwino. Ankachita zimenezi ngakhale kuti anali ndi udindo waukulu wosamalira ana awo.

Kumapeto kwa mlungu uliwonse, a Badri ndi akazi awo komanso ana awo awiri achinyamata, Gocha ndi Levani, ankakonda kukalalikira ku Dusheti, dera lamapiri lokongola kwambiri kumpoto kwa Tbilisi. Nthawi zina ankayenda ulendo wa makilomita 150 m’misewu yokhotakhota kuti akalalikire m’midzi yakutali.

Tsiku lina, mayi wina anapempha a Badri ndi akazi awo kuti apite kuntchito kwake. A Badri anati: “Titafika tinalowa m’chipinda china chachikulu ndipo tinapeza anthu pafupifupi 50 akutidikirira. Poyamba tinkachita mantha, koma titapemphera kwa Yehova, tinayamba kukambirana nawo mavesi a m’chaputala 24 cha Mateyu, omwe amanena za masiku otsiriza. Munthu wina anadabwa kwambiri ndi zimene tinafotokoza ndipo anafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani abusa a kutchalitchi kwathu satiphunzitsa zimenezi?’”

Mwambo wa Chikumbutso Unathandiza Kuti Anthu Ambiri Amvetsere Uthenga Wathu

Mwambo wokumbukira imfa ya Yesu unathandiza kuti anthu ambiri a m’dziko la Georgia amve uthenga wabwino. Mwachitsanzo, m’chaka cha 1990 pa mwambo womwe unachitikira kunyumba kwa Mlongo Ia Badridze ku Tbilisi, unathandiza kwambiri kuti anthu a m’dera lomwe mlongoyu ankakhala amvetsere uthenga wathu.

Mlongo Ia Badridze analandira anthu 200 omwe anachitira Chikumbutso m’nyumba yake

Pokonzera mwambowu, mlongoyu ndi ana ake anachotsa katundu pabalaza kuti anthu achitirepo mwambowu. Koma vuto linali loti analibe mipando yokwanira. Ndiye kodi akanaipeza kuti? Ku Georgia, si zachilendo kuona mabanja akubwereka mipando komanso matebulo kuti agwiritse ntchito pochita mwambo winawake. Choncho, popeza mlongoyu anangobwereka mipando yokha, eni a mipandoyo anamufunsa kuti, “Kodi simukufunanso matebulo? Nanga muzikaika pati chakudya?”

Anthu onse omwe anabwera kumwambo wokumbukira imfa ya Yesu anakwanira m’nyumba ya mlongoyu, yomwe ili pansanjika ya nambala 13. Pamwambowu panafika anthu 200 ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri azifunsa mafunso okhudza a Mboni za Yehova.

Mwambo wa Chikumbutso Wosaiwalika

Mu 1992 abale anachita lendi maholo akuluakulu kuti achitiremo mwambo wa Chikumbutso m’madera osiyanasiyana m’dzikoli. Mbale Davit Samkharadze amene amakhala ku Gori, anena kuti woyang’anira dera wawo anawafunsa dongosolo lomwe anakonza la mwambo wa Chikumbutso.

Atamuuza kuti apangira mwambowu m’nyumba zawo, anawafunsa kuti: “Kodi m’dera lanu mulibe holo yayikulu? Ngati ilipo bwanji osachita lendi?” Popeza holoyo inali yayikulu kwambiri yokwana anthu oposa 1,000, abale ndi alongo omwe pa nthawiyo anali ongopitirira pang’ono 100, sankaona kufunika kopanga lendi holo yayikulu choncho.

Woyang’anira dera uja atadziwa maganizo a abalewa, ananena kuti: “Ngati wofalitsa aliyense ataitana anthu 10 ndiye kuti holo ikhoza kudzadza.” Ngakhale kuti zimene woyang’anira derayu ananena zinkaoneka ngati zosathandiza kwenikweni, abale ndi alongo anayesetsa kutsatira zimene anawauza. Abalewa anadabwa kwambiri kuti pa tsiku la Chikumbutsolo panafika anthu okwana 1,036. *

Apainiya Akhama Anayamba Kulalikira M’madera Omwe Uthenga Unali Usanafike

Pofika m’chaka cha 1992, ku Georgia kunali madera ena omwe uthenga wabwino unali usanafike. Koma kodi uthenga wabwino ukanafika bwanji kumadera amenewa pamene m’dzikoli munali mavuto azachuma?

M’bale Tamazi Biblaia, yemwe ankakhala m’chigawo chakumadzulo kwa dziko la Georgia anati: “Woyang’anira dera anatiuza kuti tikumane n’kukambirana zomwe tingachite kuti tikwanitse kulalikira madera amenewa. Pa nthawiyi sitinkadziwa zimene tingachite kuti tikhale ndi apainiya apadera. Koma chomwe tinkadziwa n’choti uthenga wabwino ukufunika kulalikidwa mwamsanga.” (2 Tim. 4:2) Kenako panasankhidwa apainiya okwana 16 n’kuwatumiza m’madera osiyanasiyana.—Onani mapu patsamba 117.

Madera amene kunatumizidwa apainiya kuti akalalikire kwa miyezi 5

Mu May 1992, ku Tbilisi kunachitika msonkhano wa maola atatu. Cholinga cha msonkhanowu chinali kulimbikitsa apainiya amene anatumizidwa m’madera osiyanasiyana kuti akachite upainiya kwa miyezi 5. Mwezi uliwonse, akulu ankayendera apainiyawa kuti akawalimbikitse komanso kuwapatsa zinthu zina zofunika.

Mlongo Manea Aduashvili ndi Mlongo Nazy Zhvania, omwe anali apainiya, anatumizidwa m’tauni ya Ozurgeti. Mlongo Aduashvili yemwe anali ndi zaka 60 pa nthawiyo, anati: “Tinkadziwa kuti panali mayi wina wachidwi, yemwe ankakhala pafupi ndi tauni ya Ozurgeti. Choncho titangofika m’tauniyi, tinapita kuti tikakumane naye. Titafika kunyumba yake, tinapeza mayiyu akutidikira komanso anali ndi anthu ena okwana 30 amene anawaitana. Tsiku limeneli tinayamba kuphunzira Baibulo ndi anthu angapo.”

Miyezi yotsatira tinachititsa maphunziro ambiri. Pamene miyezi 5 inkatha, anthu 12 anali oti akhoza kubatizidwa.

Khama Lawo Linapindula

Abale awiri omwe anali apainiya, a Pavle Abdushelishvili ndi Paata Morbedadze, anatumizidwa m’tauni ya Tsageri. Tauni imeneyi ili m’dera limene anthu ambiri ali m’zipembedzo zachikhristu, koma amatsatirabe miyambo yakale.

Dera la m’chigawo cha Tsageri

Pamene nyengo yozizira kwambiri inkayandikira, abale ndi alongo omwe ankachita upainiya aja anali atatsala pang’ono kumaliza miyezi 5 imene anapemphedwa kuti akachite upainiya. Pa nthawiyi, M’bale Paata yemwe ankachitanso upainiya m’dera lina, anaitanidwa kuti akathandize nawo kumasulira mabuku. Choncho M’bale Pavle, yemwe ankachita upainiya ndi M’bale Paata, anatsala yekha ndipo ankafunika kusankha kupitirizabe upainiya kapena kubwerera kwawo. Iye anati: “Ndinkadziwa kuti ku Tsageri kumazizira osati masewera. Koma ndinaona kuti anthu amene ndinkawaphunzitsa Baibulo ankafunika kuwathandizabe. Choncho ndinaganiza zokhalabe m’derali ngakhale kuti kuchita zimenezi sikunali kophweka.”

M’bale Pavle ananenanso kuti: “Ndinkakhala ndi banja lina la m’deralo. Nthawi zambiri ndinkatha tsiku lonse ndili mu utumiki. Madzulo ndinkapita kukacheza ndi banja lija kwinaku tikuwotha moto m’chipinda chochezera, chomwe chinali munsanjika yachiwiri ya nyumbayo. Ndikatopa ndinkapita kuchipinda changa, n’kuvala chipewa, ndipo kenako ndinkagona nditafunda bulangete lotentha bwino.”

Patapita nthawi akulu anapita kukaona M’bale Pavle ndipo anapeza kuti ankaphunzira ndi anthu 11. Anthuwa anavomerezedwa kukhala ofalitsa osabatizidwa ndipo m’kupita kwa nthawi anthu onsewa anabatizidwa.

^ ndime 20 Mu 1992, m’dziko la Georgia munali ofalitsa akhama okwana 1,869. Anthu amene anabwera pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu anali okwana 10,332.