Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GEORGIA

Ndinaona Ndi Maso Anga Zimene Baibulo Limanena

Pepo Devidze

Ndinaona Ndi Maso Anga Zimene Baibulo Limanena
  • CHAKA CHOBADWA 1976

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1993

  • MBIRI YAKE Anakulira m’banja limene linali la chipembedzo cha Orthodox ndipo ankatsatira kwambiri miyambo ya chipembedzochi. Ataphunzira choonadi, anatumikirapo pa Beteli ndi mwamuna wake. Panopa akuchita upainiya wapadera.

NDINAMVA koyamba za Mboni za Yehova ndili kukoleji mumzinda wa Kutaisi. Munthu wina yemwe ndinkakhala moyandikana naye nyumba, anandiuza kuti a Mboni za Yehova sagwiritsa ntchito zifaniziro popemphera komanso sakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Zimenezi zinali zosiyana kwambiri ndi zimene ndinkakhulupirira.

Nditabwerera kwathu ku Tsageri, chakumapeto kwa chaka cha 1992, ndinapeza kuti a Mboni za Yehova amalalikiranso kumeneko. Mayi anga ankandiuza zinthu zambiri zabwino zokhudza a Mboni za Yehova. Ndiye popeza ndinkadana ndi a Mboni, mayi anga anandiuza kuti, “Kandimverere anakanena za m’maluwa. Ungachite bwino kucheza nawo wekha kuti umvetse zimene ndikunenazi.”

Abale awiri amene ankachita upainiya, a Pavle komanso a Paata, ankakonda kucheza ndi banja lina m’derali. Apainiyawa akafika, anthu ambiri ankapezerapo mwayi womvetsera komanso wofunsa mafunso osiyanasiyana. Ndiye tsiku lina nanenanso ndinaganiza zoti ndikamvetsere nawo. Ndikafunsa funso, abalewo ankandiyankha pogwiritsa ntchito Baibulo ndipo ankandiuza kuti ndiwerenge. Zimenezi zinandichititsa chidwi zedi, chifukwa ndinkaona ndi maso anga zimene Baibulo limanena.

Kenako ndinayamba kupezeka pa kagulu kena komwe kankaphunzira Baibulo ndi abalewa. Chakumapeto kwa chaka chotsatira, ineyo komanso anthu ena 9 tinabatizidwa. Patapita nthawi, nawonso mayi anga anabatizidwa.

Ndikaganizira kale langa, ndimathokoza kwambiri abale amene anandiphunzitsa Baibulo aja, chifukwa ankandilola kuti ndione ndekha mayankho a mafunso anga kuchokera m’Baibulo. Zimenezi zinachititsa kuti ndisiyiretu kukhala ndi maganizo olakwika okhudza a Mboni za Yehova chifukwa ndinaona ndekha m’Baibulo kuti zimene tinkakhulupirira kutchalitchi kwathu zinali zabodza. Ndiye ndikaganizira zimenezi, ndimaona kuti ndi bwino kuti nanenso ndikamalalikira, ndizipatsa anthu mwayi woti awerenge okha zimene Baibulo limanena kuti amvetse mfundo za m’Baibulo.