Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GEORGIA

Ndinapempha Yehova kuti Anditsogolere

Tamazi Biblaia

Ndinapempha Yehova kuti Anditsogolere
  • CHAKA CHOBADWA 1954

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1982

  • MBIRI YAKE Anathandiza nawo kusindikiza mabuku pa nthawi imene kuchita zimenezi kunali koletsedwa. Analinso mmodzi wa oyang’anira madera oyamba a ku Georgia, ngakhale kuti anali ndi ana 4.

TSIKU lina mayi anga anakwiya koopsa atamva zoti ineyo ndi mkazi wanga Tsitso, tayamba kusonkhana ndi a Mboni za Yehova. Kenako anaganiza zouza nkhaniyi achibale anga ena. Ankaganiza kuti akachita zimenezi achibale angawo andithandiza kuti ndisiye kusonkhana ndi a Mboni za Yehova. Achibale angawo anandiuza kuti ngati ndikufuna kukhalabe pamudzipo ndisiye kusonkhana ndi a Mboni, apo ayi ndione kolowera.

Atandiuza zimenezi, ndinaganiza zosamukira m’tauni. Pa nthawiyi ndinkadziwa ntchito yowotcherera zitsulo, choncho ndinaganiza zosamukira m’tauni ya Kutaisi, yomwe ndi tauni yachiwiri pa matauni aakulu kwambiri ku Georgia. Ndinkaona kuti ndikapita kumeneku sindikavutika kupeza ntchito. Ndinkaonanso kuti tingachite bwino kusamukira kumeneko chifukwa kunali ofalitsa ochepa. Choncho, ndinapempha Yehova kuti anditsogolere.

Kenako, ndinakumana ndi munthu wina yemwe ndinkaphunzira naye Baibulo. Munthuyu ankakhala m’tauni ina yaing’ono yotchedwa Jvari. Atamva zoti ndikuganiza zosamukira ku Kutaisi, anandipempha kuti ndisamukire kumene ankakhala. Iye anati: “Tili ndi nyumba ndipo ineyo ndi banja langa tikhoza kumakakhala m’chipinda chimodzi. Inuyo mukhoza kumakakhala m’chipinda china.”

Popeza ndinkafuna kuti Yehova anditsogolere, ndinamuuza kuti ndisamukira kwawoko pokhapokha nditapeza ntchito komanso nyumba yoti ndipange lendi ku Jvari. Ndinadabwa kwambiri munthuyo atabweranso chakumadzulo n’kundiuza kuti pali malo angapo omwe akufuna anthu antchito.

Patangotha masiku angapo, ine ndi banja langa tinasamukira ku Jvari. Titangofika kumeneko ndinayamba ntchito ya malipiro abwino zedi. Abwana anga anandiuza kuti ndizikhala m’nyumba ya kampani yomwe inali yaikulu kwabasi. Kenako, abale anandipempha kuti ndizithandiza nawo pa ntchito yosindikiza mabuku athu. Ndiye popeza nyumba yathu inali yaikulu, tinavomera kuti tikhoza kumagwiritsa ntchito nyumbayo pogwira ntchito imeneyi.

Kwa zaka zambiri, tinkachitira mwambo wa Chikumbutso komanso zochitika zina zapadera m’nyumbayi. Ndimasangalala kuti anthu oposa 500 anabatizidwira m’nyumba mwathu. Ndimaona kuti tinachita bwino kwambiri kupempha kuti Yehova atitsogolere n’kuchita zimene ankafuna kuti tichite.