Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sukulu ya Apainiya m’dera lina pafupi ndi ku Zugdidi

GEORGIA | 1998-2006

Anadalitsidwa ‘pa Nthawi Yabwino ndi pa Nthawi Yovuta.’—2 Tim. 4:2.

Anadalitsidwa ‘pa Nthawi Yabwino ndi pa Nthawi Yovuta.’—2 Tim. 4:2.

KUYAMBIRA m’zaka za m’ma 1990, chiwerengero cha Mboni za Yehova komanso cha anthu achidwi m’dziko Georgia chinayamba kuchuluka kwambiri. Mwachitsanzo, m’chaka cha 1998, pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu panafika anthu okwana 32,409.

Komabe panali vuto lina. Ofalitsa ambiri, ngakhalenso akulu ena, anali atangophunzira kumene choonadi ndipo sankadziwa zambiri. Choncho abale ndi alongo ankafunika kuphunzitsidwa kulalikira komanso kuchita zinthu zosiyanasiyana zokhudza kulambira. Koma kodi abalewa akanaphunzitsidwa bwanji?

Gulu la Yehova Linawathandiza Kwambiri

M’bale Arno komanso mkazi wake Sonja Tüngler, amene anali atangomaliza kumene maphunziro a Sukulu ya Giliyadi ku Germany, anatumizidwa m’dziko la Georgia mu March 1998. M’chaka chomwecho, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti m’dzikoli mumangidwe ofesi ndipo inkayang’aniridwa ndi ofesi ya nthambi ya dziko la Russia.

Kenako anasankha abale oti akhale m’Komiti ya Dziko n’cholinga choti aziyang’anira ntchito yolalikira. Dziko la Georgia litangovomereza ntchito yathu, abale anayamba kuitanitsa mabuku kuchokera ku ofesi ya nthambi yomwe pa nthawiyo inali ku Germany. Kuvomerezedwa kwa ntchito yathu kunathandizanso kuti abale azitha kugula malo oti amangepo Nyumba za Ufumu komanso ofesi ya nthambi.

Anaphunzitsidwa Zinthu Zosaneneka

Pa nthawi imene dziko la Georgia linali pansi pa ulamuliro wa Soviet Union, abale ndi alongo sankalalikira kunyumba ndi nyumba. M’bale Arno Tüngler ananena kuti: “Abale ndi alongo ambiri ankakonda ulaliki wa mumsewu chifukwa anali asanazolowere kulalikira kunyumba ndi nyumba komanso kupita kwa anthu omwe akufuna kudziwa zambiri.”

M’bale Arno Tüngler ndi mkazi wake Sonja

M’bale Davit Devidze anapita kukatumikira ku ofesi ya m’dzikoli, ofesiyi itangotsegulidwa kumene mu May 1999. M’baleyu anati: “Pa Beteli panali ntchito yochuluka zedi. M’gawo la dziko lathunso munkafunika anthu ambiri olalikira. Popeza ofesi yathu inali itangotsegulidwa kumene, panali malangizo ena omwe tinawawerenga koma sitinkadziwa chochita. Ndimaona kuti abale amene anatumizidwa ndi Bungwe Lolamulira anatithandiza kwambiri chifukwa tinkaphunzira zambiri tikamaona zimene akuchita.”

Kenako, abale a m’dziko la Georgia anayamba kuphunzitsidwa mmene angagwirire ntchito zosiyanasiyana pa ofesi ya nthambi. Abale ochokera m’mayiko ena omwe anabwera kudzathandiza abale a m’dziko la Georgia anathandiza kwambiri kuti zinthu ziziyenda bwino. (Miy. 27:17) Koma kunena zoona, nawonso anaphunzira zambiri kuchokera kwa abale a m’dzikoli.

Abale ndi Alongo Anasonyeza Makhalidwe Abwino

M’bale Arno ndi mkazi wake Sonja saiwala zimene abale ndi alongo anawachitira atafika m’dziko la Georgia. Anawalandira ndi manja awiri ndipo anawathandiza kuti azolowere utumiki wawo watsopano.

Mlongo Sonja ananena kuti abale ndi alongo a m’dzikoli anali owolowa manja. Iye anati: “Banja lina lomwe tinkakhala nalo pafupi linkatibweretsera zakudya zokhetsa dovu. Mlongo wina ankabwera kudzatitenga tikamapita kokalalikira ndipo anatithandiza kuti tidziwane ndi anthu amumpingo umene tinauzidwa kuti tizikasonkhana. Anatiphunzitsanso zinthu zambiri zokhudza chikhalidwe cha anthu a ku Georgia. Mlongo winanso anatiphunzitsa Chijojiya ndipo ankachita nafe zinthu moleza mtima kwambiri.”

M’bale Warren ndi mkazi wake Leslie Shewfelt, anachokera ku Canada ndipo anatumizidwa m’dziko la Georgia. Iwo anati: “Tinagoma kwambiri ndi chikondi chimene abale ndi alongo a m’dziko la Georgia anatisonyeza titangofika m’dzikoli. Anthu onse, ndi ana omwe, ankakondana kwambiri ndipo aliyense sankachita manyazi kuuza munthu wina kuti amamukonda.”

Abale a ku ofesi ya dziko la Georgia anathandizidwa kwambiri ndi abale ochokera m’mayiko ena

N’zoona kuti abale ndi alongo omwe anatumizidwa kuti akatumikire m’dziko la Georgia anakumana ndi mavuto ena. Komabe, mavuto amenewa sanawalepheretse kuona makhalidwe abwino a abale ndi alongo a m’dzikolo. Kudzichepetsa komanso chikondi cha abale ochokera m’mayiko enawa, zinapangitsa kuti azigwirizana kwambiri ndi abale a m’dziko la Georgia.

Anthu Oopa Mulungu Anaphunzira Choonadi

M’zaka za m’ma 1990, anthu ambiri a mitima yabwino anaphunzira choonadi. Mwachitsanzo, m’chaka cha 1998 chokha, anthu amene anabatizidwa analipo 1,724. Koma kodi n’chiyani chimene chinachititsa zimenezi?

M’bale Tamazi Biblaia, yemwe anali woyang’anira dera kwa zaka zambiri, ananena kuti: “Anthu ambiri amamvetsera uthenga wathu tikamawalalikira chifukwa chikhalidwe chathu chimalimbikitsa anthu kuti aziopa Mulungu.”

M’bale Davit Samkharadze, yemwe ndi mlangizi wa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, anafotokoza kuti: “Munthu akayamba kuphunzira Baibulo, achibale komanso anthu ena amabwera kuti adzasokoneze. Amachita zimenezi n’cholinga chofuna kuletsa m’bale wawoyo kuti asiye kuphunzira Baibulo. Koma nthawi zambiri nawonso amakopeka n’kuyamba kuphunzira Baibulo.”

Uthenga wabwino unafalikira m’dziko la Georgia ndipo unathandiza anthu ambiri kuti asinthe moyo wawo. Mu April 1999, anthu amene anafika pa Chikumbutso anali 36,669.

“Pali Otsutsa Ambiri”

Paulo ankaona kuti anali ndi mwayi waukulu wolalikira ku Efeso wakale. Iye anati: “Pakuti khomo lalikulu la mwayi wautumiki landitsegukira, koma pali otsutsa ambiri.” (1 Akor. 16:9) Mawu amenewa akugwirizana ndi zimene abale ndi alongo a m’dziko la Georgia anakumana nazo patangotha miyezi ingapo kuchokera pamene Chikumbutso cha chaka cha 1999 chinachitika.

M’mwezi wa August chaka chomwecho, gulu lina la chipembedzo cha Orthodox, lomwe linkatsogoleredwa ndi munthu wina yemwe anachotsedwa pa udindo wa unsembe, dzina lake Vasili Mkalavishvili, anachita zionetsero ku Tbilisi. Pa zionetserozo, gululi linawotcha mabuku athu. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ayambe kuzunza a Mboni ndipo mavutowa anachitika kwa zaka 4.

Kungoyambira m’chaka cha 1999, magulu ena ankachita zionetsero, ankawotcha mabuku athu komanso ankamenya abale ndi alongo

Pa 17 October, 1999, anthu angapo a m’gulu la chipembedzo lija, limodzi ndi anthu enanso 200, anasokoneza misonkhano ya mpingo wa Gldani ku Tbilisi. Gululi linagwiritsa ntchito zibonga komanso zitsulo pomenya abale ndi alongo athu moti ena anavulazidwa kwambiri mpaka kugonekedwa kuchipatala.

Chodabwitsa n’chakuti palibe amene anamangidwa chifukwa cha zimenezi ndipo anthu anapitirizabe kuzunza a Mboni za Yehova. Pulezidenti Shevardnadze komanso akuluakulu angapo a boma, anadzudzula khalidwe limeneli, koma palibe chimene chinachitika. Nthawi zambiri apolisi ankabwera m’mbuyo mwa alendo, abale athu atachitidwa kale zachipongwe.

Pa nthawi yomweyi, phungu wina wa kunyumba ya malamulo, dzina lake Guram Sharadze, analimbikitsa anthu kuti akhaulitse a Mboni za Yehova. Ankauza anthu kuti a Mboni za Yehova ndi anthu oopsa. Zimenezi zinachititsa kuti zinthu zisokonekere kwambiri. “Nthawi yabwino” imene abale ndi alongo a m’dzikoli ankalalikira momasuka inasanduka mbiri yamakedzana.

Gulu la Yehova Linathandiza Pamene Abale Ankatsutsidwa

Gulu la Yehova linathandiza kwambiri pa nthawi imene abale ndi alongo a ku Georgia ankakumana ndi mavuto amenewa. Abale ndi alongo analandira malangizo omwe anawathandiza kudziwa zimene angachite anthu ena akawaukira. Anakumbutsidwanso mfundo ya m’Malemba yakuti Akhristu oona amakumana ndi mavuto ambiri kuphatikizapo kuzunzidwa.2 Tim. 3:12.

Kuwonjezera pamenepa, gulu la Yehova linkasuma kukhoti abale ndi alongo akachitiridwa nkhanza zosiyanasiyana. M’bale wina yemwe ankatumikira m’Dipatimenti ya Zamalamulo ku ofesi ya nthambi ya ku Georgia, anati: “Pa zaka 4 zomwe anthu ankachitira nkhanza a Mboni za Yehova m’dziko la Georgia, tinasuma milandu yoposa 800. Milandu yonseyi inali yokhudza gulu la a Vasili Mkalavishvili. Tinapempha akuluakulu a boma komanso mabungwe oona za ufulu wa anthu kuti atithandize. Abale a kulikulu la dziko lonse la Mboni za Yehova anakonza zoti pagawidwe kapepala kapadera kodziwitsa anthu za nkhanza zomwe anthu ankachitira a Mboni ku Georgia. Komabe, zimenezi sizinaphule kanthu chifukwa palibe chimene chinasintha.” *

^ ndime 30 Kuti mudziwe zambiri zokhudza milandu imene abale ndi alongo anasuma kukhoti chifukwa cha nkhanza zimene ankawachitira, onani Galamukani! yachingelezi ya January 22, 2002, tsamba 18-24.