Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GEORGIA

Mwamuna Wanga Sankafuna Kusiya Kuwerenga

Marina Kopaliani

Mwamuna Wanga Sankafuna Kusiya Kuwerenga
  • CHAKA CHOBADWA 1957

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1990

  • MBIRI YAKE Marina ndi mwamuna wake Badri, ankachita khama kwambiri pogwira ntchito yolalikira. Ankachita zimenezi ngakhale kuti anali ndi ana awiri. M’kupita kwa nthawi, Badri anatumikira m’Komiti ya Dziko ndipo anakhalabe wokhulupirika mpaka pamene anamwalira mu 2010.

MU 1989, ine ndi mwamuna wanga tinakumana ndi a Mboni za Yehova kunyumba kwa munthu wina yemwe tinayandikana naye nyumba. M’bale Givi Barnadze, yemwe ankaphunzira Baibulo ndi munthuyu, analibe Baibulo lakelake chifukwa pa nthawiyo kukhala ndi Baibulo kunali kovuta kwambiri.

Tinasangalala kwambiri ndi zimene tinamva moti tinaganiza zopeza Baibulo lathulathu. Mwamuna wanga atakumana ndi mchimwene wake anamuuza kuti tikufunitsitsa titapeza Baibulo. Iye anadabwa kwambiri mchimwene wakeyo atamuuza kuti anali atangogula kumene Baibulo latsopano lachijojiya. Anamuuzanso kuti amupatsa Baibulolo ngati mphatso.

Mwamuna wanga atafika kunyumba, anakhala pampando n’kuyamba kuwerenga Baibulo mpaka dzuwa linalowa. Tsiku lotsatira, anapitiriza kuwerenga Baibulo lija. Ndiye madzulo pamene ndinkafika kuchokera kuntchito, ndinamupeza akuwerengabe. Mwamuna wanga sankafuna kusiya kuwerenga. Choncho ndinamuuza kuti atenge tchuthi cha masiku angapo kuti amalize kuwerenga Baibulolo. Anachitadi zimenezi, moti pasanapite nthawi anamaliza kuliwerenga.

Pamene tinayamba kuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya ndi M’bale Barnadze, tinasangalala kwambiri chifukwa tinali ndi Baibulo lathulathu. Zinthu zinayenda bwino, chifukwa ife tinalibe buku la Coonadi, pomwe M’bale Barnadze anali ndi bukuli koma analibe Baibulo. Ndiye ndinganene kuti tinali ndi zinthu zonse zofunika pophunzira Baibulo. Patadutsa pafupifupi chaka, ine ndi mwamuna wanga tinabatizidwa.