GEORGIA
Akhristu Oona Amasonyeza Chikondi Chenicheni
KAMTSIKANA kena dzina lake Sanel kasanabadwe, madokotala anauza makolo ake kuti mwanayo adzabadwa ndi vuto lalikulu. Ananenanso kuti n’zokayikitsa ngati angadzakhale ndi moyo. Mwanayo atangobadwa, ankafunika kupangidwa opaleshoni. Makolo ake ankakhala ku Abkhazia, dziko lomwe linaima palokha kuchoka ku dziko la Georgia. Makolo a Sanel sanapeze dokotala amene akanalola kuchita opaleshoni mwanayu popanda kumuika magazi m’dziko lawolo.
Makolowa anadziwitsa Komiti Yolankhulana ndi Achipatala za nkhaniyi. * Mwamwayi, abale a m’komitiyi anapeza dokotala yemwe akanachita opaleshoni mwanayu kulikulu la dziko la Georgia, ku Tbilisi. Koma pa nthawiyi, mayi a Sanel sankapeza bwino moti sakanakwanitsa kupita nawo ku Tbilisi. Choncho, anakonza zoti agogo ake awiri, amene ndi a Mboni za Yehova, apite ndi mwanayu ku Tbilisi.
Opaleshoni ya Sanel inayenda bwino kwambiri. Pasanapite nthawi yaitali opaleshoniyi itachitika, agogo ake anati: “Tinakhala m’chipatala kwa masiku 20. Pa nthawi imeneyi, abale ndi alongo a m’dziko la Georgia ankabwera kudzationa ndipo anatithandiza kwambiri. Zimenezi zinatikhudza zedi chifukwa tinali titawerengapo zokhudza chikondi chimene abale ndi alongo amachitira anzawo omwe sakuwadziwa. Koma pa nthawiyi tinaona zimenezi zikutichitikira.”
^ ndime 4 Abale omwe ali m’Komiti Yolankhulana ndi Achipatala m’dziko la Georgia anapeza madokotala okwana 250 omwe amalola kuchita opaleshoni popanda kuika magazi.