Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Macao

NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Asia ndi Middle East

Asia ndi Middle East
  • MAYIKO 49

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 4,464,374,770

  • OFALITSA 728,989

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 771,272

Anthu Ambiri Anayamba Kuphunzira Baibulo Chifukwa cha Munthu Mmodzi

Tsiku lina a Jonathan, omwe amakhala ku Philippines, anapita kuchipatala ndipo ankadikirira kuti aonane ndi dokotala. Mayi wina dzina lake Laila, yemwe ankagwira ntchito pamalo olandirira alendo, anachita chidwi ndi mmene a Jonathan anavalira moti anawafunsa ngati amagwira ntchito kukampani ya inshulansi. A Jonathan anauza mayiwa kuti ndi a Mboni za Yehova ndipo anapita kuchipatalako kuti akathandize wa Mboni wina yemwe ankadwala. Mayiyo anadabwa kwambiri ndi zimenezi ndipo anauza a Jonathan kuti bambo awo anamwalira, koma ankakonda kuwerenga magazini a Nsanja ya Olonda. A Jonathan atamva izi anawerengera mayiyu lemba la Yohane 5:28, 29 ndipo anamupatsanso kapepala kakuti, Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa?

Philippines: M’bale Jonathan akulalikira mayi wogwira ntchito pamalo olandirira alendo

A Jonathan akamapita kuchipatalaku, ankatengera mayiyu mabuku athu ndipo anamupezera mlongo woti aziphunzira nawo Baibulo. Kenako amuna awo a a Laila, mchemwali wawo komanso mayi awo, omwe ankakhala nawo limodzi, anayambanso kuphunzira Baibulo.

A Rose, omwe ankakhala pafupi ndi a Laila anafunsa a Laila chifukwa chake kunyumba kwawo kunkabwera alendo pafupipafupi. A Laila anawafotokozera kuti anthuwo ndi a Mboni ndipo amabwera kudzawaphunzitsa Baibulo. Zimenezi zinachititsa kuti nawonso a Rose ayambe kuphunzira Baibulo. Kenako a Rose atapita kumudzi kwawo kukaona mchemwali wawo, anafotokozera anthu zimene ankaphunzira. Mchemwali wawoyu, yemwe dzina lake ndi Abigail, anachita chidwi kwambiri moti anapempha kuti nayenso ayambe kuphunzira. Nawonso mayi awo a a Rose anavomera kuti aziphunzira Baibulo.

A Laila anabatizidwa pamsonkhano wina wachigawo. Kenako nawonso amayi awo anabatizidwa. A Rose ndi mchemwali wawo uja anabatizidwa chaka chatha. Amayi awo a a Rose amasonkhana ndipo achibale awo ena a a Laila akupitiriza kuphunzira Baibulo. Zonsezi zatheka chifukwa choti a Jonathan analalikira kuchipatala kuja.

Akugwiritsa Ntchito Zipangizo Zamakono Polalikira Anthu Omwe Ali ndi Vuto Losamva

Anthu olankhula Chinenero Chamanja amene akuphunzira choonadi ku Sri Lanka akuwonjezeka. Mu 2015 abale anali ndi mayina ndi maadiresi a anthu osakwana 80 omwe ali ndi vuto losamva m’dzikoli ndipo mayinawa anangowalemba papepala. Kenako panakhazikitsidwa mpingo woyamba wa Chinenero Chamanja. Panopa abalewa analemba pakompyuta mayina ndiponso maadiresi a anthu 420 omwe ali ndi vuto losamva ndipo amatha kuwapeza mosavuta pogwiritsa ntchito GPS. Abale ndi alongo akwanitsa kulalikira ambiri mwa anthuwa kudzera pavidiyo, meseji kapena pamasom’pamaso. Banja lina lomwe likupanga umishonale m’dzikoli linati: “Poyamba abale ndi alongo ankangolalikira anthu okhawo amene ankawadziwa. Koma panopa tikutha kufikira anthu ambiri. Timauza ofalitsa malo amene angathe kupeza anthu omwe ali ndi vuto losamva kuti akawalalikire.”

Kalata Yoyamikira Yochokera kwa Mkulu wa Boma

Abale ndi alongo a ku Mongolia amalalikira mwakhama pogwiritsa ntchito timashelefu tamatayala ngakhale kunja kukamazizira kwambiri. Tsiku lina bambo wina yemwe ndi mkulu wa boma, anatenga mabuku pakashelefu kena ndipo kenako analemba kalata yothokoza. Bamboyu anati: “Ndine wachipembedzo chachibuda, koma ndimawerenga mabuku a zipembedzo zosiyanasiyana. Ndimachita zimenezi chifukwa ndimakhulupirira kuti ndi bwino kudziwanso zimene zipembedzo zina zimaphunzitsa. Nditawerenga mabuku anu, ndaona kuti ndikulembereni kalata yothokoza. Mabuku anu ndi othandiza kwambiri moti n’zoonekeratu kuti mumachita zambiri kuti mulembe mabuku amenewa. Mabuku anu andithandiza kuzindikira kuti Baibulo ndi buku lomwe aliyense ayenera kuliwerenga chifukwa lili ndi mfundo za choonadi. M’Baibulo muli malangizo omwe angatithandize. Ndikuthokoza onse omwe amagwira ntchito mwakhama kumasulira mabukuwa m’Chimongolia. Ndikuthokozanso onse omwe amagawira mabukuwa kwa anthu ngakhale pamene kunja kukutentha kapena kukuzizira kwambiri.”

Mongolia: Ofalitsa akulalikira ngakhale kuti kunja kukuzizira kwambiri

Pemphero Lake Linayankhidwa

M’bale wina dzina lake Brett amakhala ku Hong Kong ndipo ndi mpainiya. Tsiku lina analalikira mnyamata wina wazaka 20 chakuti, ndipo anamupatsa kapepala kakuti, Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala? Mnyamatayo ataona kapepalako anayamba kulira. Kenako anafotokoza kuti anakulira m’banja la Mboni koma ali ndi zaka 16 anachoka panyumba. Kwa zaka 5 ankangokhala m’misewu ndipo kenako anayamba kumwa mankhwala osokoneza bongo. Patapita nthawi bungwe lina linamutenga n’kumakamusamalira.

Mnyamatayu anauza m’baleyo kuti m’mawa wa tsikuli anali atapemphera kwa Yehova kuti: “Ngati chipembedzo cha makolo anga chili choona, ndipatseni chizindikiro.” Choncho atakumana ndi m’baleyu anaona kuti pemphero lake layankhidwa. Kenako anapita pamalo ena chapafupi ndipo anakambirana mfundo za m’kabuku kakuti, Bwererani kwa Yehova. Popeza mnyamatayu ankafunika kubwerera kwawo ku France, anapatsana manambala a foni ndi zina kuti azitha kulumikizana. Patapita nthawi mnyamatayo analembera M’bale Brett kuti: “M’bale wanga, Yehova wayankha pemphero langa. Lamlungu ndipita ku Nyumba ya Ufumu.” Mnyamatayu anakumana ndi a Mboni a ku France ndipo anayamba kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana.