Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Warwick, NY: Likulu la Mboni za Yehova Lapadziko Lonse

Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi

Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi

NGAKHALE kuti zinthu m’dziko la Satanali zikuipiraipira, atumiki a Yehova ali ndi ‘zochita zambiri mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Malipoti otsatirawa akusonyeza zimene a Mboni za Yehova akhala akuchita posonyeza kuti ‘amakhulupirira Yehova, amachita zabwino komanso amayesetsa kukhala okhulupirika m’zochita zawo zonse.’Sal. 37:3.

Ntchito Yosamutsa Likulu la Mboni za Yehova Komanso Ofesi ya Nthambi

Ntchito yomanga maofesi atsopano mumzinda wa Wallkill ku New York inatha pa 1 February, 2016. Choncho Komiti ya Nthambi ya ku United States, Dipatimenti ya Utumiki komanso madipatimenti ena anasamukira kumalowa. Ntchito yomanga likulu la Mboni za Yehova lapadziko lonse inatha ku Warwick moti anthu a m’banja la Beteli ya ku Brooklyn ayamba kusamukira kumalo atsopanowa.

Kuyambira Lolemba pa 3 April, 2017, anthu azidzatha kupita kukaona malo atsopanowa. Poona mbali zitatu, anthu azidzayenda okha, koma poona mbali ina ya 4, azidzayenda ndi munthu wowasonyeza malo.

  1. Mbali ya “Dzina la Mulungu M’Baibulo” ili ndi Mabaibulo akale kwambiri omwe sapezeka masiku ano. Mbaliyi ilinso ndi umboni wosonyeza kuti dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Baibulo.

  2. Mbali ya “Anthu Odziwika ndi Dzina la Yehova” ili ndi zithunzi zosonyeza mbiri ya Mboni za Yehova. Mbaliyi ikusonyezanso kuti Yehova wakhala akutsogolera, kuphunzitsa komanso kuthandiza anthu ake kuti azichita chifuniro chake mwadongosolo.

  3. Mbali ya “Likulu Lapadziko Lonse—Anasonyeza Chikhulupiriro” ili ndi mavidiyo osonyeza mmene makomiti a Bungwe Lolamulira amathandizira kuti atumiki a Yehova azisonkhana, azilalikira, aziphunzira Mawu a Mulungu komanso azikondana.

Mbali zimenezi zizidzakhala zotsegula kuchokera Lolemba mpaka Lachisanu, kuyambira 8:00 koloko m’mawa mpaka 4:00 koloko madzulo. Mbali yomwe anthu azidzayenda ndi munthu wowasonyeza malo ija, izidzakhala ya maminitsi 20. Anthu azidzaona maofesi komanso panja pa Beteli. Azidzaona malo amenewa kuchokera Lolemba mpaka Lachisanu, kuyambira 8:00 koloko m’mawa mpaka 11:00 koloko komanso 1:00 koloko masana mpaka 4:00 koloko madzulo.

Musanapite kukaona malo, pitani pa jw.org. Onani pamene palembedwa kuti ZOKHUDZA IFEYO > MAOFESI NDI KUONA MALO > United States.

M'CHIGAWO ICHI

Tikuyesetsa Kuti Ntchito Yolalikira Padziko Lonse Izikhala Pamalo Oyamba

Kodi anthu amene poyamba ankatumikira pa Beteli achita chiyani kuti azikwanitsa utumiki wawo watsopano?

“Ndinu Aneba Abwino”

Pa May 7 ndi 8, 2016, anthu anaona malo ku Brooklyn Heights, New York ndipo izi zinathandiza kuti anthuwa adziwe zokhudza Beteli ya ku Brooklyn.

Msonkhano Watsopano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Kuyambira January 2016, misonkhano ya mkati mwa mlungu inasintha.

Mapulogalamu a pa JW Broadcasting ‘Ndi Othandiza Komanso Olimbikitsa Kwambiri’

Mapulogalamu a JW Broadcasting anakhazikitsidwa mu 2014 ndipo tsopano akupezeka m’zilankhulo 90. Kodi amene amaonera mapulogalamuwa anena zotani?

Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi

Mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Kyrgyzstan ndi ku Armenia unali wosangalatsa kwambiri.

Lipoti la Milandu la 2016

Kodi a panali milandu yotani yokhudza a Mboni za Yehova mu 2016?

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

Nkhani za posachedwapa zonena za zimene a Mboni za Yehova achita ku Germany, Belize, Burundi, Nepal, Italy, Argentina, Uganda, Congo (Kinshasa) ndi ku Papua New Guinea.