Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Germany: Akulalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala pamalo omwe pamakhala anthu othawa kwawo

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

Akumalalikira Anthu Ochokera Mayiko Ena

M’dziko la Germany muli anthu ambiri oyankhula zinenero zina chifukwa cha anthu othawa kwawo komanso ena omwe anapita kukagwira ntchito m’dzikoli. Chifukwa cha zimenezi, m’miyezi 9 yapitayi, abale anayambitsa timagulu tokwana 229 ta zinenero za m’mayiko ena. Komanso abale ndi alongo okwana 800 akuphunzira zinenero 13 m’makalasi 30.

Ofalitsa amalalikira pamalo omwe anthu ochokera m’mayiko enawa amafikira. Ofalitsawa amalalikira pogwiritsa ntchito timashelefu tamatayala m’malo okwana 200 ndipo agawira mabuku, magazini komanso zinthu zina zokwana 640,000.

Bungwe Lolamulira linavomereza kuti abale a m’dzikoli agwire ntchito yapadera kuyambira m’mwezi wa May mpaka mu July 2016. Pa nthawiyi abale ndi alongo pafupifupi 700, omwe amayankhula Chiarabu anapita kukalalikira anthu oyankhula chinenerochi m’malo 10 a ku Austria komanso ku Germany.

Amatola Ndalama Zachitsulo Mumsewu

Ofalitsa 50 a mumpingo wa Faber’s Road Kriol ku Belize amayenda pansi akamalalikira. Abale ambiri a mumpingowu ndi osauka koma anapeza njira yopezera ndalama zoti azipereka. Kuyambira zaka zingapo zapitazo, abalewa anagwirizana kuti akamalalikira azitola ndalama zachitsulo zomwe zimapezeka m’misewu yafumbi. Kumapeto kwa chaka chilichonse amakumana n’kutsuka ndalama zimene apeza komanso kuziwerenga.

Ndalama zachitsulo zambiri zimene amatola zimakhala zochepa mphamvu moti sangagulire chinthu chooneka. Koma akazisonkhanitsa zimakhala zambiri ndipo zimatha kukwana madola 225 a ku America. Abalewa amatenga hafu ya ndalamazo n’kupereka kumpingo ndipo zina amazipereka kuti zikathandize pa ntchito ya padziko lonse.

Anthu Okwana 4 Miliyoni Anamvetsera Nkhani Yapadera

Ku Burundi kunachitika zinthu zosaiwalika pamene M’bale Anthony Griffin anapita m’dzikoli monga woimira likulu lathu. Pa 5 March, 2016, nkhani imene m’baleyu anakamba komanso pulogalamu yonse ya pa tsikuli, zinaulutsidwa pawailesi yaikulu ya m’dzikoli kuti abale ndi alongo a m’mipingo yonse amvetsere. Anthu amene anamvetsera pulogalamuyi anakwana 4 miliyoni.

Zimene zinachitikazi zinathandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wathu ndipo ambiri anayamikira. Munthu wina wogwira ntchito kusiteshoni ya wailesiyo anati: “Mupitirize kuchita mapulogalamu ngati amenewa!” Winanso ananena kuti: “Mupitirize kuulutsa mapulogalamu ngati amenewa chifukwa angathandize kuti anthu adzapulumuke.” Pa tsikuli, eni mabasi ambiri komanso magalimoto ahayala anatsegula siteshoni ya wailesi imene inkaulutsa pulogalamuyi.

Phokoso la Kudansi Silinasokoneze Chikumbutso

Ku Nepal, abale ena a m’kagulu kakutali anachita lendi holo ina kuti achitiremo Chikumbutso cha 2016. Koma abalewa anadandaula kwambiri atamva zoti kukhala dansi yaikulu pasukulu ina yapafupi ndi holoyo.

Pamadansi ngati amenewa nyimbo zake zimakhala zaphokoso kwambiri. M’mawa wa tsiku la Chikumbutsolo, abale ndi alongo ankayeretsa muholoyo ndipo munthu amene anakonza dansiyo anawauza kuti: “Simuzimvana chifukwa padansi yathu pakhala phokoso lambiri.”

Dansiyo inayambika masana ndipo pamalopo panalidi chiphokoso. Abalewo anabwereka sipika yaikulu kuposa imene ankafuna kugwiritsa ntchito. Koma pamene ankayesa sipikayo, mawu sankamveka m’pang’ono pomwe chifukwa cha phokoso la kudansiko. Abale ataona zimenezi anakhumudwa kwambiri ndipo anaganiza zopempherera nkhaniyo. Kenako abale ndi alongo anayamba kufika pamalowa ndipo itangotsala 30 minitsi kuti mwambowu uyambe, nyimbo zija zinangosiya mwadzidzidzi. Apolisi anali ataimitsa dansiyo chifukwa choti anthu ena oledzera ankamenyana. Zimenezi zinachititsa kuti abale achite mwambo wa Chikumbutso popanda chosokoneza chilichonse.

Anayamikira Webusaiti Yathu ya jw.org

M’bale Giuseppe amakhala ku Italy ndipo ndi mpainiya wokhazikika. M’baleyu amagwira ntchito pakampani ina yokonza mawebusaiti. M’mwezi wa May, bwana wamkulu wapakampanipo anachititsa msonkhano ndipo panapezeka ogwira ntchito 70, kuphatikizapo m’baleyu. Pamsonkhanowu ankakambirana zinthu zina zomwe zingawathandize pa ntchito yawoyi. Bwanayo ananena kuti pali mawebusaiti amene angawathandize kuti azipanga mawebusaiti abwino. Kenako anawaonetsa chitsanzo cha webusaiti imodzi pasikilini. M’bale Giuseppe anadabwa kwambiri ataona kuti bwana akewo atsegula webusaiti ya jw.org. Bwanayo anati: “Palibenso webusaiti yabwino ngati imeneyi!” Ndiyeno anayamba kuwafotokozera zinthu zina zochititsa chidwi zomwe zimapezeka pawebusaitiyi. Iye ananena kuti webusaitiyi ili ndi malinki osavuta komanso zithunzi zokongola kwambiri.

M’bale Giuseppe anati: “Anzangawo anadabwa atazindikira kuti pawebusaitiyi pali zinenero zambirimbiri. Chakumapeto kwa msonkhanowu, bwana wanga wina anauza abwana aja komanso anthu ena onse kuti: ‘Giuseppe ndi wa Mboni za Yehova.’ Atangonena zimenezi abwana aja anandiuza kuti: ‘Gulu lanuli ndimalitayira kamtengo. Munapanga webusaiti yabwino kwambiri imene makampani komanso mabungwe ambiri amaisirira. Ndikuona kuti pamakhala ntchito yaikulu kwambiri kuti muike zinthu komanso kuti anthu asamavutike kugwiritsa ntchito webusaitiyi.’ Ndinachita manyazi kwambiri chifukwa bwanayu ankatamanda ineyo ngakhale kuti sindinagwire nawo ntchito yokonza webusaitiyi. Komabe ndinasangalala kwambiri chifukwa anthu ena omwe anali pamsonkhanowu, anamva koyamba za Mboni za Yehova. Panopa ndimacheza ndi ena mwa anthuwa ndipo anthu atatu ndinayamba kuphunzira nawo Baibulo.” Kampaniyi ikupitirizabe kuphunzira zambiri pawebusaiti ya jw.org ndipo nayenso M’bale Giuseppe akupitirizabe kukambirana za mfundo za m’Baibulo ndi anzakewo.

Anakana Kukasewera Mpira Kunja

Argentina: Jorge akusewera mpira ndi abale

Chakumayambiriro kwa chaka cha 2010, mnyamata wina wa ku Argentina dzina lake Jorge analalikidwa ndi mnzake wina wam’kalasi. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Pa nthawiyi Jorge ankasewera mpira. Iye anakhala katswiri wa masewerawa ndipo anasankhidwa kuti akasewere nawo mu kalabu ina yaikulu. Mu April 2014, anapeza mwayi woti akasewere mu timu ina ya ku Germany. Jorge anasangalala kwambiri ndi zimenezi ndipo anavomera kuti apita. Koma kutangotsala masiku ochepa kuti anyamuke, akochi ake anamuuza kuti: “Ndiwe wa Mboni za Yehova eti? Usapite kunja chifukwa zisokoneza moyo wako. Ine ndili mnyamata ndinalinso wa Mboni. Kenako ndinaitanidwa kuti ndizikasewera m’timu ya m’dziko lina la ku Asia. Anandilonjeza zinthu zambiri zabwino ndipo ndinatengeka nazo. Ine ndi banja langa tinasamuka n’kupitadi m’dzikolo. Koma ndinabwerako nditakhumudwa kwambiri.” Jorge anati: “Nditaganizira zimene akochi ananenazi, ndinaona kuti ndisapite ku Germany. Mu 2015 ndinakhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo kenako ndinabatizidwa.”

Analandira Madalitso Kwaulere

Mu September 2015, mumzinda wa Kampala ku Uganda munachitika Msonkhano Wachigawo wakuti, “Tsanzirani Yesu.” Anthu amene anabwera pamsonkhanowu anasangalala kwambiri M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira, atatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lachiluganda.

Mayi wina amene akuphunzira Baibulo, yemwenso analandira Baibulo pamsonkhanowo, anati: “Ndinasangalala kwambiri kulandira Baibulo lokongola. Pa nthawi imeneyo anthu ankakonzekera kubwera kwa papa. Pofuna kupeza ndalama zapamwambowu, pankagulitsidwa makolona pamtengo wa madola 30 (a ku America). Ankati makolona amenewa angathandize munthu kupeza madalitso. Anthu ambiri ankafuna madalitso koma analibe ndalama zogulira makolonawo. Koma ine ndinalandira Baibulo kwaulere ndipo ndinaona kuti amenewo ndiye madalitso enieni. Yehova anapereka madalitsowa kwa onse amene anapita kumsonkhanowu. Zinali kwa munthu kupereka mochokera pansi pa mtima ndalama iliyonse imene angafune. Ndimawerenga Baibuloli tsiku lililonse ndipo popeza ndi lachinenero changa, ndimamvetsa bwino zimene ndikuwerengazo. Izi zikundithandiza kuti ndimudziwe bwino Yehova. Ndikumuthokoza kwambiri pondipatsa Baibulo langalanga.”

Ankanama Kuti Mabuku Athu Amasindikizidwa Kudziko la Mizimu

Pofuna kunyozetsa webusaiti yathu ya www.pr418.com, atsogoleri a zipembedzo zina ku Congo (Kinshasa) ankaphunzitsa otsatira awo kuti mabuku ndi zinthu zina zimene a Mboni za Yehova amafalitsa zimasindikizidwa kudziko la mizimu. Kuti anthu akhulupirire bodzali, atsogoleri azipembedzowa ankati zilembo za “www” zimafanana ndi nambala ya 666 yomwe imapezeka m’buku la Chivumbulutso. (Chiv. 13:18) Izi zinachititsa kuti anthu ena amene poyamba ankaphunzira Baibulo, ayambe kukana kuphunzira.

M’bale wina ndi mkazi wake, omwenso ndi apainiya, anaipempherera nkhaniyi. Kenako anaitana anthu amene ankaphunzira nawo Baibulo. Anawapempha kuti abwere limodzi ndi amuna kapena akazi awo, kuti adzacheze kunyumba kwawo. Mabanja atatu anabweradi ndipo atamaliza kudya, m’bale ndi mkazi wakeyu anawaonetsa vidiyo yakuti, Mboni za YehovaGulu Limene Likulalikira Uthenga Wabwino. Zimene anthuwa anaona muvidiyoyi zinawathandiza kudziwa kuti zimene atsogoleri azipembedzo aja ankanena n’zabodza. Mlungu wotsatira mwamuna wa mmodzi mwa amayi amene anabwera, anapereka ndalama zokwana madola 100 a ku America kwa banjalo. Anati ndalamazo akazipereke kuti zikathandize pa ntchito yolalikira yapadziko lonse. Iye anachita zimenezi ngakhale kuti anali asanayambe kuphunzira Baibulo.

Amayesetsa Kuti Aphunzire Nyimbo Zatsopano

Abale ndi alongo amene amakhala m’madera akumidzi m’dziko la Papua New Guinea akuyesetsa kuphunzira nyimbo zathu zatsopano ngakhale kuti kumaderawa kulibe intaneti. Mwachitsanzo, abale a mpingo wa Mundip amatumiza m’bale kuti apite kutauni ina yapafupi kuti akapeze mawu a nyimbozi. M’baleyo amayenda wapansi kwa maola awiri kuti akafike kokwerera basi ndipo akakwera, amayendanso kwa maola ena awiri kuti akafika kutauniyo. Kumeneko amatha kugwiritsa ntchito intaneti ndipo amakopera mawu a nyimbozi m’kope. Akafika ku Nyumba ya Ufumu, amalemba mawu a nyimbozo pabolodi kuti aliyense azitha kuona. Ndiyeno abale ndi alongo onse amakopera mawu a nyimbowa m’makope awo kuti aziimba pamisonkhano. Iwo amaona kuti n’zofunika kwambiri kuti nawonso aziimba nyimbo zatsopanozi pamisonkhano ngati mmene akuchitira abale ndi alongo a mipingo yonse padziko lapansi.