Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kyrgyzstan

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi

Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi

ABALE ndi alongo a m’dziko la Kyrgyzstan komanso ochokera m’mayiko ena anagwira ntchito mwakhama kwa chaka ndi hafu pokonza komanso kuwonjezera ofesi ya nthambi yomwe ili mumzinda wa Bishkek. Mwambo wotsegulira nthambiyi unachitika pa 24 October, 2015, patangotha mwezi umodzi ntchitoyi itatha. Pulogalamuyi inalumikizidwanso m’Nyumba za Ufumu 18 komanso m’malo ena ndipo anthu 3,000 amene anasonkhana m’malowa anamvera mwambowo. M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Muzitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu.” Tsiku lotsatira, kunachitika msonkhano wolimbikitsa ndipo abale ndi alongo ambiri a m’dzikoli anamvetsera msonkhanowu.

Nthambi ya ku Kyrgyzstan

Loweruka pa 14 May, 2016, anthu okwana 6,435 anafika pamwambo wotsegulira nthambi ya ku Armenia. Ofesi ya nthambiyi ndi nsanjika 6 zomwe zili m’chinyumba cha nsanjika 18. Mwambowu unalinso wotsegulira Nyumba ya Msonkhano komanso nyumba zomwe ndi Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Nkhani zomwe zinakambidwa pamwambowu zinafotokoza chiyambi cha a Mboni za Yehova ku Armenia. A Mboni oyambirira anali anthu a ku Armenia amene ankakhala ku United States chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Kenako choonadi chinafika m’dziko la Armenia cha m’ma 1970 dzikoli lidakali pansi pa ulamuliro wa Soviet Union. Chaposachedwapa a Mboni za Yehova analembetsa kuboma n’kukhala chipembedzo chovomerezeka ndipo kenako m’dzikoli munakhazikitsidwa ofesi ya nthambi. Anthu ambiri omwe anafika pamwambowu analipo pa nthawi imene choonadi chinafika m’dzikoli. Pa nthawi imeneyo iwo sankaganiza kuti m’dzikoli mungadzachitike zinthu zapadera ngati zimenezi. Mwambowu unafika pachimake pamene anthu onse omwe analipo anagwirizana ndi zimene M’bale David Splane, wa m’Bungwe Lolamulira, ananena kuti nthambiyo akuipereka kwa Yehova.

Armenia

Pamwamba: Mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi

Pakati: Abale ndi alongo ali pamsonkhano womwe unachitika kumapeto kwa mlunguwo

Pansi: Abale ndi alongo akuvina gule wachikhalidwe chawo