Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!

Nkhanizi zikuthandizani kudziwa zimene mungachite kuti mukhale bwenzi la Mulungu.

PHUNZIRO 1

Mulungu Akukuitanani Kuti Mukhale Bwenzi Lake

Anthu a padziko lonse anasankha kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Nanunso mukhoza kukhala bwenzi la Mulungu.

PHUNZIRO 2

Mulungu Ndiye Bwenzi Labwino Koposa, Limene Mungakhale Nalo

Mulungu adzakuthandizani kuti muzikhala osangalala.

PHUNZIRO 3

Muyenera Kuphunzira za Mulungu

Zimenezi zidzakuthandizani kudziwa zimene Mulungu amasangalala nazo komanso zimene amadana nazo.

PHUNZIRO 4

Mmene Mungaphunzirire za Mulungu

Mulungu anakonza zoti tidziwe zimene anachita m’mbuyomo, zimene akuchita panopa komanso zimene adzachite m’tsogolo.

PHUNZIRO 5

Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso

Moyo wa m’Paradaiso sudzakhala ngati mmene ulili panopa. Kodi zinthu zidzakhala bwanji m’Paradaiso?

PHUNZIRO 6

Paradaiso Ali Pafupi

Kodi tingatsimikize bwanji kuti paradaiso ali pafupi?

PHUNZIRO 7

Kutengerapo Chenjezo pa Zochitika Zakale

Kodi nkhani ya Nowa ikutiphunzitsa chiyani masiku ano?

PHUNZIRO 8

Kodi Adani a Mulungu Ndani?

N’zotheka kudziwa njira zimene amagwiritsa ntchito n’kuzipewa kuti musapusitsidwe.

PHUNZIRO 9

Nanga Mabwenzi a Mulungu Ndani?

Kodi anthu amafunika kudziwa zotani zokhudza Yehova?

PHUNZIRO 10

Mmene Mungapezere Chipembedzo Choona

Pali zinthu zingapo zomwe mungachite kuti mudziwe chipembedzo choona.

PHUNZIRO 11

Kanani Chipembedzo Chonyenga!

Kodi chipembedzo chonyenga mungachidziwe bwanji? N’chifukwa chiyani chipembedzo choterocho ndi choipa?

PHUNZIRO 12

N’chiyani Chimachitika pa Imfa?

Zimene Baibulo limanena zimatilimbikitsa.

PHUNZIRO 13

Matsenga ndi Ufiti ndi Zoipa

N’chifukwa chiyani Mulungu amadana ndi zamatsenga ndi za ufiti?

PHUNZIRO 14

Mabwenzi a Mulungu Amapeŵa Zoipa

Kodi ndi zinthu ziti zimene Mulungu amadana nazo?

PHUNZIRO 15

Mabwenzi a Mulungu Amachita Zabwino

Kodi ndi zabwino ziti zomwe zingatithandize kuti tikhale mabwenzi a Mulungu?

PHUNZIRO 16

Sonyezani Chikondi Chanu kwa Mulungu

Kuti mupitirize kukhala pa ubwenzi ndi mnzanu, mumafunika kumulankhula, kumumvetsera komanso kuuza anthu ena zinthu zabwino zimene mnzanuyo amachita. N’zimenenso zimafunika kuti munthu akhale bwenzi lenileni la Mulungu.

PHUNZIRO 17

Kuti Musataye Bwenzi, Inunso Khalani Bwenzi

Mukamaphunzira zambiri zokhudza Mulungu, mudzayamba kumukonda kwambiri.

PHUNZIRO 18

Khalani Bwenzi la Mulungu Mpaka Kalekale

Moyo wosatha ndi mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu adzaipereka kwa anthu omwe ndi mabwenzi ake.