Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 11

Kanani Chipembedzo Chonyenga!

Kanani Chipembedzo Chonyenga!

Satana ndi ziŵanda zake safuna kuti inu mutumikire Mulungu. Iwo amachita chilichonse chotheka kuti apandutse aliyense kuchoka kwa Mulungu. Kodi amachita motani zimenezo? Njira imodzi ndiyo kudzera m’chipembedzo chonyenga. (2 Akorinto 11:13-15) Chipembedzo chimakhala chonyenga ngati sichiphunzitsa choonadi chochokera m’Baibulo. Chipembedzo chonyenga chili ngati ndalama yachinyengo—ingaoneke ngati yeniyeni, koma ili yopanda pake. Ikhoza kukuloŵetsani m’vuto lalikulu.

Chinyengo cha chipembedzo sichingam’sangalatse Yehova, Mulungu wa choonadi. Pamene Yesu anali padziko lapansi, panali gulu la chipembedzo limene linafuna kumupha. Iwo anaganiza kuti kalambiridwe kawo ndiko kanali kolondola. Iwo anati: “Tili naye atate mmodzi ndiye Mulungu.” Kodi Yesu anavomereza zimenezo? Ayi! Iye anati kwa iwo: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi.” (Yohane 8:41, 44) Lerolino, anthu ambiri amaganiza kuti amalambira Mulungu, koma kwenikweni akulambira Satana ndi ziŵanda zake!—1 Akorinto 10:20.

Monga mtengo wowola ubala zipatso zoipa, chipembedzo chonyenga chimakhalanso ndi anthu ochita zoipa. Dziko ladzaza mavuto chifukwa cha zoipa zomwe anthu amachita. Pali zachiwerewere, kuba, kuponderezana, umbanda, ndi kugwirirana. Ambiri amene amachita zoipa zimenezi ali ndi chipembedzo, koma chipembedzo chawo sichiwalimbikitsa kuchita zabwino. Iwo sangakhale mabwenzi a Mulungu pokhapokha atasiya kuchita zinthu zoipazo.—Mateyu 7:17, 18.

Chiphunzitso chonyenga chimaphunzitsa anthu kupemphera ku mafano. Mulungu amaletsa kupemphera ku mafano. Chimenechi n’chanzeru. Kodi mungakonde ngati munthu wina salankhula ndi inu koma m’malomwake, amangolankhula ndi chithunzi chanu? Kodi munthu woteroyo angakhaledi bwenzi lanu lenileni? Ayi, n’zosatheka. Yehova amafuna kuti anthu azilankhula ndi iye, osati ndi chifanizo kapena chithunzi, chimene chilibe moyo.—Eksodo 20:4, 5.

Chipembedzo chonyenga chimaphunzitsa kuti n’koyenera kupha ena panthaŵi ya nkhondo. Yesu anati mabwenzi a Mulungu azikondana wina ndi mnzake. Ife sitipha anthu omwe timawakonda. (Yohane 13:35) N’kulakwa kwa ife ngakhale kupha anthu oipa. Pamene adani a Yesu anafika kuti am’mange, iye sanalole kuti ophunzira ake amenye nkhondo pofuna kum’teteza iye.—Mateyu 26:51, 52.

Chipembedzo chonyenga chimaphunzitsa kuti oipa adzazunzika m’moto wa helo. Komabe, Baibulo limaphunzitsa kuti uchimo umatengera munthu ku imfa. (Aroma 6:23) Yehova ndi Mulungu wa chikondi. Kodi Mulungu wokonda anthu n’kutheka kuti angazunze anthu kwamuyaya? Ndithudi ayi! M’Paradaiso, mudzakhala chipembedzo chimodzi chokha, chija chimene Yehova amachivomereza. (Chivumbulutso 15:4) Zipembedzo zonse zozikidwa pa mabodza a Satana zidzakhala zitachotsedwa.