Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 18

Khalani Bwenzi la Mulungu Mpaka Kalekale

Khalani Bwenzi la Mulungu Mpaka Kalekale

Kupeza bwenzi kumalira khama; kusunga bwenzi kumaliranso khama. Khama lanu pakupalana ubwenzi ndi Mulungu ndi kukhalabe bwenzi lake lidzadalitsidwa kwambiri. Yesu anati kwa aja amene anakhulupirira iye: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Kodi zimenezo zimatanthauzanji?

Mukhoza kupeza ufulu tsopano lino. Mukhoza kumasuka ku ziphunzitso zonyenga ndi mabodza amene afalitsidwa ndi Satana. Mukhoza kumasuka pa kuthedwa nzeru kumene kuli ndi mamiliyoni a anthu amene sadziŵa Yehova. (Aroma 8:22) Mabwenzi a Mulungu ali omasuka ngakhale pa “kuopa imfa.”—Ahebri 2:14, 15.

Mutha kudzasangalala ndi ufulu m’dziko latsopano la Mulungu. Inde, mukhoza kudzapeza ufulu wodabwitsa m’tsogolo muno! M’dziko lapansi laparadaiso, mudzakhala ufulu ku nkhondo, matenda, ndi upandu. Ufulu ku umphaŵi ndi njala. Ufulu ku ukalamba ndi imfa. Ufulu ku mantha, kuponderezedwa, ndi chisalungamo. Baibulo limati ponena za Mulungu: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.”—Salmo 145:16.

Mabwenzi a Mulungu adzakhala ndi moyo kosatha. Moyo wosatha ndi mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu adzapatsa onse opalana naye ubwenzi. (Aroma 6:23) Tangoganizani zimene moyo wosatha ungatanthauze kwa inu!

Mudzakhala ndi nthaŵi yochita zinthu zambiri. Mwinamwake mungafune kudzaphunzira kuimba chida choimbira. Kapena mungadzafune kuphunzira kujambula zithunzi kapena kukhala kalipentala. Mwinanso mungadzafune kuphunzira zinyama ndi zomera. Mwachidziŵikire mudzafuna kudzayenda ndi kuona malo ndi anthu osiyanasiyana. Zonsezi zidzatheka mutangopeza moyo wosatha basi!

Mudzakhala ndi nthaŵi yopeza mabwenzi ambiri. Kukhala ndi moyo kosatha kudzatheketsa kudziŵa anthu ambiri amenenso akhala mabwenzi a Mulungu. Mudzadziŵa maluso awo ndi mikhalidwe yawo yabwino, ndipo iwonso adzakhala mabwenzi anu. Mudzawakonda, ndipo adzakukondani. (1 Akorinto 13:8) Kukhala ndi moyo wosatha kudzakupatsani mpata wopalana ubwenzi ndi wina aliyense padziko lapansi! Choposa zonse, ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimbiralimbirabe m’kupita kwa zaka zikwizikwi. Khalanitu bwenzi la Mulungu mpaka kalekale!