Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 8

Kodi Adani a Mulungu Ndani?

Kodi Adani a Mulungu Ndani?

Mdani wamkulu wa Mulungu ndi Satana Mdyerekezi. Iye ndi cholengedwa chauzimu chimene chinapandukira Yehova. Satana akupitirizabe kulimbana ndi Mulungu ndi kuchititsa mavuto aakulu kwa anthu. Satana ndi woipa. Iye ndi wabodza ndi wambanda.—Yohane 8:44.

Zolengedwa zinanso zauzimu zinagwirizana ndi Satana pa kupandukira kwake Mulungu. Baibulo limazitcha ziŵanda. Monga Satana, ziŵandanso ndi adani a anthu. Zimakonda kuvulaza anthu. (Mateyu 9:32, 33; 12:22) Yehova adzawononga Satana limodzi ndi ziŵanda zake kwamuyaya. Iwo atsala ndi nthaŵi yochepa kwambiri yopitiriza kuvutitsa anthu.—Chivumbulutso 12:12.

Ngati mukufuna kukhala bwenzi la Mulungu, musachite zimene Satana amafuna kuti muchite. Satana ndi ziŵandazo amadana ndi Yehova. Iwo ndi adani a Mulungu, ndipo amafuna kukuchititsani kukhalanso mdani wa Mulungu. Muyenera kusankha amene mukufuna kum’kondweretsa—Satana kapena Yehova. Ngati mukufuna moyo wosatha, sankhani kuchita chifuniro cha Mulungu. Satana ali ndi machenjera ambiri ndi njira zimene amanyenga nazo anthu. Anthu ambiri akupusitsidwa naye.—Chivumbulutso 12:9.