PHUNZIRO 5
Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso
Paradaiso sadzakhala ngati dziko limene tikukhalamoli. Sichinali chifuniro cha Mulungu kuti dziko lapansi likhale ndi mavuto ochuluka, chisoni, zopweteka ndiponso kuvutika. M’tsogolo muno, Mulungu adzasandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso. Kodi Paradaiso adzakhala wotani? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena:
Anthu abwino. Paradaiso adzakhala mudzi wa mabwenzi a Mulungu. Adzachitirana zinthu zabwino zokhazokha. Adzakhala ndi moyo motsatira njira za Mulungu zolungama.—Miyambo 2:21.
Chakudya chamwana alirenji. M’Paradaisomo njala siidzakhalamo. Baibulo limati: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka [kapena kuti chakudya chambiri].”—Salmo 72:16.
Nyumba zabwino ndi ntchito yosangalatsa. M’dziko lapansi la Paradaiso, banja lililonse lidzakhala ndi nyumba yawoyawo. Aliyense adzagwira ntchito yom’patsa chisangalalo chenicheni.—Yesaya 65:21-23.
Mtendere padziko lonse. Anthu sazidzamenyananso ndi kufa m’nkhondo ayi. Mawu a Mulungu amati: “[Mulungu] aletsa nkhondo.”—Thanzi labwino. Baibulo limalonjeza kuti: “Wokhalamo [m’Paradaiso] sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ndiponso, simudzapezeka wopunduka kapena wakhungu kapena wogontha kapena wosalankhula.—Yesaya 35:5, 6.
Kutha kwa zopweteka, chisoni, ndi imfa. Mawu a Mulungu amati: “Sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
Anthu oipa adzachotsedwa. Yehova walonjeza kuti: “Oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:22.
Anthu adzakondana ndi kulemekezana wina ndi mnzake. Sipadzakhalanso kusoŵa chilungamo, kuponderezana, umbombo, ndi chidani. Anthu adzakhala ogwirizana ndipo adzakhala ndi moyo wotsatira njira za Mulungu zolungama.—Yesaya 26:9.