PHUNZIRO 17
Kuti Musataye Bwenzi, Inunso Khalani Bwenzi
Ubwenzi umamangidwa pa chikondi. Pamene muphunzira zambiri ponena za Yehova, chikondi chanunso kwa iye chimakula kwambiri. Pamene chikondi chanu kwa Mulungu chikula, chilakolako chanu chofuna kum’tumikira chimakulanso. Chimenechi chidzakulimbikitsani kukhala wophunzira wa Yesu Kristu. (Mateyu 28:19) Mwa kugwirizana ndi banja lachimwemwe la Mboni za Yehova, mutha kukhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu kwamuyaya. Kodi muyenera kuchita chiyani?
Muyenera kusonyeza chikondi chanu kwa Mulungu mwa kumvera malamulo ake. “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.”—1 Yohane 5:3.
Gwiritsani ntchito zimene mumaphunzira. Yesu anasimba nkhani imene imasonyeza mfundo imeneyi. Munthu wina wanzeru anamanga nyumba yake pathanthwe. Munthu wopusa anamanga nyumba yake pamchenga. Pamene mphepo yaikulu inawomba, nyumba yomangidwa pathanthwe siinagwe, koma nyumba yomangidwa pamchenga inagwa ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu. Yesu anati aja amene amamva ziphunzitso zake ndi kuzichita ali ngati munthu wanzeru uja amene anamanga nyumba yake pathanthwe. Koma aja amene amamva ziphunzitso zake koma osazichita ali ngati munthu wopusa uja amene anamanga nyumba yake pamchenga. Kodi inuyo mukufuna kukhala munthu uti?—Mateyu 7:24-27.
Ubatizo. “Nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.”—Machitidwe 22:16.
Kudzipereka ndi mtima wonse pa kutumikira Mulungu. “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi.”—Akolose 3:23.