PHUNZIRO 9
Nanga Mabwenzi a Mulungu Ndani?
Yesu Kristu ndi Mwana wa Yehova, komanso ndiye bwenzi lake lenileni lapamtima. Asanadzakhale pano padziko lapansi monga munthu, Yesu anali kumwamba monga cholengedwa champhamvu chauzimu. (Yohane 17:5) Kenako anabwera padziko lapansi kudzaphunzitsa anthu choonadi chonena za Mulungu. (Yohane 18:37) Iye anaperekanso moyo wake kuti apulumutse anthu omvera ku uchimo ndi imfa. (Aroma 6:23) Yesu tsopano ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, boma lakumwamba limene lidzabweretsa Paradaiso padziko lapansili.—Chivumbulutso 19:16.
Angelo Alinso mabwenzi a Mulungu. Angelo sanayambe akhalapo anthu padziko lapansi. Mulungu anawalenga iwo kumwambako asanalenge dziko lapansi. (Yobu 38:4-7) Angelo alipo mamiliyoni ambiri. (Danieli 7:10) Mabwenzi a Mulungu akumwamba ameneŵa amafuna kuti anthu aphunzire choonadi chonena za Yehova.—Chivumbulutso 14:6, 7.
Mulungu alinso ndi mabwenzi padziko lapansi; amawatcha Mboni zake. Mboni m’bwalo la milandu imanena zimene imadziŵa ponena za munthu wina kapena chinthu china. Mboni za Yehova zimauza ena zimene zimadziŵa ponena za Yehova ndi chifuno chake. (Yesaya 43:10) Mofanana ndi angelo, Mbonizo zimafuna kukuthandizani kuphunzira choonadi chonena za Yehova. Zimafuna kuti inunso mukhale bwenzi la Mulungu.