Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 2

Mulungu Ndiye Bwenzi Labwino Koposa, Limene Mungakhale Nalo

Mulungu Ndiye Bwenzi Labwino Koposa, Limene Mungakhale Nalo

Kukhala bwenzi la Mulungu ndiko chinthu chabwino koposa m’moyo wanu. Mulungu adzakuphunzitsani mmene mungakhalire wachimwemwe ndi wotetezeka; adzakumasulani ku ziphunzitso zonyenga zambiri ndi zochita zina zowononga munthu. Adzamvetsera mapemphero anu. Adzakuthandizani kupeza mtendere wa m’maganizo ndi chidaliro mumtima. (Salmo 71:5; 73:28) Mulungu adzakuchirikizani m’nthaŵi yamavuto. (Salmo 18:18) Ndipo Mulungu akupereka kwa inu mphatso yake ya moyo wosatha.—Aroma 6:23.

Pamene muyandikira kwa Mulungu, mudzayandikiranso mabwenzi a Mulungu. Iwonso adzakhala mabwenzi anu. Ndipotu adzakhala ngati abale ndi alongo kwa inu. Iwo adzakonda kukuphunzitsani za Mulungu ndipo adzakuthandizani ndi kukulimbikitsani.

Ife sitili olingana ndi Mulungu. Pamene mukufuna ubwenzi ndi Mulungu, pali mfundo ina yofunika yoti muidziŵe. Ubwenzi ndi Mulungu si ubwenzi wapakati pa anthu olingana. Iye ndi wamkulu ndiponso wanzeru komanso wamphamvu kutiposa ife. Ndiye Wolamulira wathu woyenera. Choncho, ngati tikufuna kukhala bwenzi lake, tiyenera kumvetsera kwa iye ndi kuchita zimene amatiuza kuchita. Kuchita motero kudzatipindulitsa nthaŵi zonse.—Yesaya 48:18.