PHUNZIRO 3
Muyenera Kuphunzira za Mulungu
Kuti mukhale bwenzi la Mulungu, muyenera kuphunzira za iye. Kodi mabwenzi anu amalidziŵa dzina lanu ndipo amalitchula? Inde amatero. Mulungunso amafuna kuti dzina lake mulidziŵe ndi kumalitchula. Dzina la Mulungu ndi Yehova. (Salmo 83:18; Mateyu 6:9) Muyenera kudziŵanso zimene amafuna ndi zimene safuna. Mufunikiranso kudziŵa mabwenzi ake ndi adani ake. Komatu kudziŵa munthu kumatenga nthaŵi. Baibulo limanena kuti n’kwanzeru kupatula nthaŵi yophunzira za Yehova.—Aefeso 5:15, 16.
Mabwenzi a Mulungu amachita zimene zimam’kondweretsa. Taganizirani za mabwenzi anu. Ngati inuyo muwachitira zoipa ndiponso kuchita zinthu zimene iwo amadana nazo, kodi adzapitiriza kukhala mabwenzi anu? Ndithudi ayi! Mofananamo, ngati mukufuna kukhala bwenzi la Mulungu, muyenera kuchita zimene zimam’kondweretsa.—Yohane 4:24.
Si zipembedzo zonse zimene zimapezetsa ubwenzi ndi Mulungu. Yesu, amene ndiye bwenzi lenileni lapamtima la Mulungu, analankhula za njira ziŵiri. Njira ina n’njotakata ndipo ili ndi anthu ambiri. Njira imeneyo imatsogolera ku chiwonongeko. Njira inayo n’njopapatiza ndipo ili ndi anthu oyendamo oŵerengeka. Njira imeneyo imatsogolera ku moyo wosatha. Izi zimatanthauza kuti ngati mufuna kukhala paubwenzi ndi Mulungu, muyenera kuphunzira njira yolondola yom’lambirira.—Mateyu 7:13, 14.