Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 15

Mabwenzi a Mulungu Amachita Zabwino

Mabwenzi a Mulungu Amachita Zabwino

Pamene muli ndi mnzanu amene mumam’sirira ndi kum’lemekeza, mumayesa kum’tsanzira. Baibulo limanena kuti “Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima.” (Salmo 25:8) Kuti tikhale mabwenzi a Mulungu, tiyenera tikhale abwino ndi owongoka mtima. Baibulo limati: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi.” (Aefeso 5:1, 2) Nazi njira zina zochitira zimenezi:

Khalani wothandiza ena. “Tichitire onse chokoma.”—Agalatiya 6:10.

Gwirani ntchito zolimba. “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake.”—Aefeso 4:28.

Khalani waukhondo m’thupi ndi m’makhalidwe. “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.”—2 Akorinto 7:1.

Sonyezani apabanja panu chikondi ndi ulemu. “Yense payekha, . . . akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa [“azilemekeza kwambiri”, NW] mwamuna. Ananu, mverani akukubalani.”—Aefeso 5:33–6:1.

Sonyezani chikondi kwa ena. “Tikondane wina ndi mnzake; chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu.”—1 Yohane 4:7.

Mverani malamulo a dziko. “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu [boma] . . . Perekani kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho.”—Aroma 13:1, 7.