Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 7

Kutengerapo Chenjezo pa Zochitika Zakale

Kutengerapo Chenjezo pa Zochitika Zakale

Yehova sadzalola kuti anthu oipa adzawononge Paradaiso. Mabwenzi ake okha ndiwo ati adzakhalemo. Nanga chidzachitika kwa oipa n’chiyani? Kuti tidziŵe yankho, talingalirani nkhani yeniyeni ya Nowa. Nowa anakhalapo ndi moyo zaka zikwi zingapo zapitazo. Iye anali munthu wabwino amene anayesetsa nthaŵi zonse kuchita chifuniro cha Yehova. Koma anthu ena padziko lapansi ankachita zinthu zoipa. Choncho Yehova anauza Nowa kuti Iye akabweretsa chigumula cha madzi kuti chikawononge anthu onse oipa. Kenako anauza Nowa kuti amange chingalawa kotero kuti iye ndi banja lake asafe pofika Chigumulacho.—Genesis 6:9-18.

Nowa ndi banja lake anamanga chingalawa. Nowa anachenjezanso anthu ena kuti kudzabwera Chigumula, koma iwo sanam’mvere. Anapitiriza kuchita zinthu zoipa. Atamaliza chingalawacho, Nowa analoŵetsa nyama zosiyanasiyana m’chingalawamo, komanso iye ndi banja lake analoŵanso mmenemo. Ndiyeno Yehova anadzetsa mvula yaikulu yamkuntho. Mvulayo inagwa masiku 40 usana ndi usiku. Ndipo madziwo anasefukira padziko lonse lapansi.—Genesis 7:7-12.

Anthu oipa anataya miyoyo yawo, koma Nowa ndi banja lake anapulumuka. Yehova anawateteza kufikira Chigumulacho chitatha kenako anawabwezera m’dziko lapansi lopanda choipa chilichonse. (Genesis 7:22, 23) Baibulo limanena kuti nthaŵi idzafika pamene Yehova adzawononganso onse okana kuchita zabwino. Anthu abwino sadzawonongedwa. Adzakhala kwamuyaya m’dziko lapansi la Paradaiso.—2 Petro 2:5, 6, 9.

Lerolinonso anthu ambiri amachita zinthu zoipa. Dziko lapansi ladzaza mavuto okhaokha. Yehova watumiza Mboni zake mobwerezabwereza kuti zikachenjeze anthu, koma ochuluka safuna kumvera mawu a Mulungu. Safuna kusintha njira zawo. Safunanso kulabadira zimene Mulungu amalangiza pa zabwino ndi zoipa. Kodi chidzachitike n’chiyani kwa anthu oterowo? Kodi tsiku lina adzasintha? Ambiri sadzasintha konse. Ikudza nthaŵi pamene anthu oipa adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso.—Salmo 92:7.

Dziko lapansi silidzawonongedwa; adzalikonza kukhala paradaiso. Aja amene akukhala mabwenzi a Mulungu adzakhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi.—Salmo 37:29.