Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 6

Paradaiso Ali Pafupi

Paradaiso Ali Pafupi

Zoipa zimene zikuchitika padziko lapansi zimasonyeza kuti Paradaiso ali pafupi. Baibulo linanena kuti tidzaona nthaŵi zoipitsitsa pamene Paradaiso wayandikira. Nthaŵi zake ndi zinozi! Nazi zina mwa zimene Baibulo linati zidzachitika:

Nkhondo zazikulu. “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Ulosi umenewu wakwaniritsidwa. Kuchokera m’chaka cha 1914, pachitika nkhondo zapadziko lonse ziŵiri ndi zing’onozing’ono zambiri. Anthu mamiliyoni aphedwa m’nkhondo zimenezo.

Matenda ofalikira. Kudzakhala “miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:11) Kodi zimenezi zachitikadi? Inde. Kansa, matenda a mtima, chifuŵa cha TB, malungo, AIDS, ndi matenda ena apha anthu mamiliyoni ambiri.

Kusoŵa chakudya. Kuzungulira dziko lonse lapansi pali anthu amene sadya mokwanira. Mamiliyoni a anthu amafa ndi njala chaka chilichonse. Chimenechi ndi chizindikiro china chakuti Paradaiso wayandikira. Baibulo limati: “Padzakhala njala.”—Marko 13:8.

Zivomezi. “Kudzakhala . . . zivomezi m’malo akutiakuti.” (Mateyu 24:7) Izinso zachitika m’nthaŵi yathu. Anthu oposa miliyoni imodzi afa m’zivomezi chiyambire 1914.

Anthu oipa. Anthu adzakhala “okonda ndalama” ndi “odzikonda okha.” Adzakhala “okonda zokondweretsa osati okonda Mulungu.” Ana akakhala “osamvera akuwabala.” (2 Timoteo 3:1-5) Kodi simukuvomereza kuti anthu oterowo alipo ambiri lero? Iwo alibiretu ulemu kwa Mulungu, ndipo amavutitsa aja omwe amayesa kuphunzira za Mulungu.

Upandu. Padzakhalanso “kuchuluka kwa kusayeruzika.” (Mateyu 24:12) Mwachionekere inunso mukuvomereza kuti upandu tsopano wafika poipa kusiyana ndi zaka za m’mbuyomu. Anthu kulikonse amakhala pangozi ya kuberedwa, kunamizidwa, kapena kuvulazidwa.

Zinthu zonsezi zimasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira. Baibulo limati: “Pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.” (Luka 21:31) Kodi Ufumu wa Mulungu ndi chiyani? Ndi boma la Mulungu lakumwamba limene lidzabweretsa Paradaiso padziko lapansili. Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo mwa maboma onse a anthu.—Danieli 2:44.