Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 3

Kukhumudwa—Tikakhala ndi “Chifukwa Chodandaulira”

Kukhumudwa—Tikakhala ndi “Chifukwa Chodandaulira”

Mlongo wina dzina lake Linda anati: “Mumpingo wathu, mlongo wina anandinamizira kuti ndamubera ndalama. Ndipo abale ndi alongo ena anakhulupirira zimenezi. Kenako mlongoyo anandiuza kuti wazindikira zoti sindinabe ndalamazo. Ngakhale kuti anapepesa, mumtimamu ndinkaona kuti sindingathe kumukhululukira.”

KODI inunso munakhumudwitsidwapo ndi m’bale kapena mlongo wina? N’zomvetsa chisoni kuti ena zimawasokoneza maganizo kwambiri moti amafika posiya kutumikira Mulungu mwakhama. Kodi inunso munasiya kuchita zinthu zina chifukwa chokhumudwa?

Palibe “Angatilekanitse ndi Chikondi cha Mulungu”

Kunena zoona, zimakhala zovuta kukhululukira m’bale kapena mlongo amene watikhumudwitsa. Timadziwa kuti Akhristu ayenera kukondana. (Yohane 13:34, 35) Choncho Mkhristu mnzathu akatikhumudwitsa zimapweteka kwambiri.—Salimo 55:12.

Baibulo limasonyeza kuti nthawi zina Mkhristu wina angachititse kuti mnzake akhale ndi “chifukwa chodandaulira.” (Akolose 3:13) Komabe zikatichitikira, timakhumudwa kwambiri. Ndiyeno kodi n’chiyani chingatithandize? Tiyeni tikambirane mfundo zitatu za m’Baibulo.

Atate wathu wakumwamba amadziwa zonse. Yehova amadziwa zonse ngakhale zinthu zopanda chilungamo zimene zatichitikira. Amadziwanso mmene zinthuzo zatikhudzira. (Aheberi 4:13) Yehova amatimvera chisoni tikamavutika. (Yesaya 63:9) Iye sangalole ‘chisautso, zowawa,’ zochita za Akhristu anzathu kapena chinthu chilichonse ‘kutilekanitsa ndi chikondi chake.’ (Aroma 8:35, 38, 39) Nafenso tisalole chilichonse kapena aliyense kutilekanitsa ndi Yehova.

Kukhululuka si kulekerera. Tikakhululukira anthu sikuti tikulekerera kapena kupeputsa zimene anatilakwira. Tizikumbukira kuti Yehova salekerera zoipa koma amakhululukira anthu olapa. (Salimo 103:12, 13; Habakuku 1:13) Choncho akamatiuza kuti tizikhululukira ena, amakhala akutipempha kuti tizimutsanzira. Baibulo limanena kuti iye “sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse.”—Salimo 103:9; Mateyu 6:14.

Kukhululuka kumatithandiza. N’chifukwa chiyani tikunena kuti kukhululuka kumatithandiza? Kuti timvetse, tiyerekezere kuti mwanyamula mwala wopepuka n’kutambasula mkono umene mwanyamulirawo. Mwina poyamba simungavutike kuunyamula. Koma bwanji patapita maminitsi angapo kapena ola? N’zosachita kufunsa kuti mkono wanu udzatopa kwambiri. N’zoona kuti mwalawu susintha, koma mukaugwira kwa nthawi yaitali umayamba kulemera kwambiri. Tikasungiranso munthu zifukwa, ngakhale pa zinthu zazing’ono koma kwa nthawi yaitali, timadzipweteka tokha. M’pake kuti Yehova amatiuza kuti tisamasungire ena zifukwa. Kunena zoona, kukhululuka kumatithandiza.—Miyambo 11:17.

Kukhululuka kumatithandiza

Anamva Ngati Yehova Akulankhula ndi Iyeyo

N’chiyani chinathandiza Linda amene tamutchula kumayambiriro uja kuti akhululukire mlongo amene anamulakwira? Chinthu chimodzi n’chakuti, anaganizira kwambiri zifukwa zimene Baibulo limatiuzira kuti tizikhululukira anzathu. (Salimo 130:3, 4) Mfundo imene inamuthandiza kwambiri ndi yoti Yehova amatikhululukira ngati ifenso timakhululukira anzathu. (Aefeso 4:32–5:2) Linda ananena kuti atawerenga zifukwa za m’Malembazo, anamva ngati Yehova akulankhula ndi iyeyo.

Kenako Linda anasiya kusungira zifukwa mlongo winayo. Iye anamukhululukira ndi mtima wonse ndipo panopa amagwirizana kwambiri. Tsopano Linda akutumikira Yehova mwakhama. Dziwani kuti Yehova amafunitsitsa kukuthandizani ngati mmene anathandizira Linda.