Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Wokondedwa wathu:

Baibulo limafotokoza za anthu okhulupirika amene ankakumana ndi mavuto ofanana ndi athu. Tingati anali anthu “monga ife tomwe.” (Yakobo 5:17) Ena ankapanikizika ndi mavuto ndiponso ankada nkhawa. Ena anakhumudwitsidwa ndi achibale kapena atumiki anzawo. Ndiye palinso ena amene ankadziimba mlandu kwambiri chifukwa cha zimene analakwitsa.

Koma sikuti anthu amenewa anasiyiratu Yehova. Ambiri anali ndi maganizo ofanana ndi a wamasalimo amene anapemphera kuti: “Ndayendayenda ngati nkhosa yosochera. Ndifunefuneni ine mtumiki wanu, pakuti sindinaiwale malamulo anu.” (Salimo 119:176) Kodi mwina inunso mukumva ngati wamasalimoyu?

Yehova saiwala atumiki ake amene asochera. M’malomwake, amawafufuza ndipo nthawi zambiri amagwiritsa ntchito atumiki ake pochita zimenezi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yobu. Paja iye anakumana ndi mavuto azachuma, anadwala kwambiri ndipo ana ake anaphedwa. Komanso anzake amene anayenera kumuthandiza anamukhumudwitsa. N’zoona kuti Yobu anayamba kukhala ndi maganizo olakwika koma sanasiyiretu Yehova. (Yobu 1:22; 2:10) Kodi Yehova anamuthandiza bwanji?

Iye anagwiritsa ntchito mtumiki wina dzina lake Elihu kuti alimbikitse Yobu. Elihu anamvetsera bwino pamene Yobu ankafotokoza mavuto ake. Chosangalatsa n’chakuti, pamene anayamba kulankhula sanadzudzule Yobu kapena kumuimba mlandu. Sankadziona kuti ndi wapamwamba kuposa Yobuyo. Ndipo mzimu wa Mulungu unalimbikitsa Elihu kunena kuti: “Kwa Mulungu woona, ine ndili ngati inu nomwe. Inenso ndinaumbidwa ndi dongo.” Kenako anakhazika Yobu mtima pansi pomuuza kuti: “Mwa ine mulibe chinthu choti muope, ndipo mawu anga sakulemetsani.” (Yobu 33:6, 7) Elihu sanalemetse Yobu ndi mawu opweteka. M’malomwake anamulimbikitsa n’kumupatsa malangizo oyenera.

Maganizo amene tili nawo pokulemberani kabukuka ndi ofanana ndi a Elihu. Tisanakalembe, tinayamba tamva kaye maganizo a anthu amene anasochera ndipo tinawafunsa mavuto amene amakumana nawo. (Miyambo 18:13) Kenako tinafufuza nkhani za m’Malemba zosonyeza mmene Yehova anathandizira atumiki ake akale amene anakumananso ndi zimenezi. Ndiyeno m’kabukuka talembamo nkhani ngati zimenezo komanso maganizo a anthu ena a masiku ano. Tikukupemphani kuti muwerenge bwinobwino kabukuka. Dziwani kuti timakukondani kwambiri.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova