Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 14

Kodi Apainiya Ali Ndi Mwayi Wochita Maphunziro Otani?

Kodi Apainiya Ali Ndi Mwayi Wochita Maphunziro Otani?

United States

Sukulu ya Giliyadi, ku Patterson, New York

Panama

Kwa nthawi yaitali, gulu la Yehova lakhala likuphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito masukulu osiyanasiyana ophunzitsa Baibulo. Anthu amene amadzipereka kuti azilalikira za Ufumu nthawi zonse, amalowa m’sukulu yapadera yomwe imawathandiza kuti ‘akwaniritse utumiki wawo.’​—2 Timoteyo 4:5.

Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Mpainiya wokhazikika akakwanitsa chaka chimodzi akuchita utumiki wa nthawi zonse, amalowa m’sukulu yomwe imachitika kwa masiku 6 pa Nyumba ya Ufumu ya m’dera lawo. Cholinga cha sukuluyi ndi kuthandiza apainiya kuti azikonda kwambiri Yehova, akhale ndi luso m’mbali zonse za utumiki wawo komanso kuti apitirize kukhala okhulupirika pochita utumikiwo.

Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Sukuluyi, imene imachitika kwa miyezi iwiri, inakonzedwa n’cholinga chothandiza apainiya amene achita utumikiwu kwa kanthawi komanso amene ali ndi mtima wofunitsitsa kukatumikira kumadera ofunikira ofalitsa ambiri. Anthu amene ali ndi mtima umenewu amakhala ngati akunena kuti, “Ine ndilipo! Nditumizeni” ndipo akamachita zimenezi amasonyeza kuti akutsanzira Yesu Khristu yemwe ndi Mlaliki wamkulu kuposa onse amene anagwira ntchito yolalikira padziko lapansi. (Yesaya 6:8; Yohane 7:29) Munthu akasamukira kutali ndi kwawo amafunika kuzolowera kukhala ndi moyo wosafuna zinthu zambiri. Chikhalidwe, nyengo komanso zakudya za m’dera la tsopanolo zikhoza kukhala zosiyana kwambiri ndi zimene anazizolowera. Mwina angafunikenso kuphunzira chinenero china. Sukuluyi imathandiza mabanja, abale osakwatira komanso alongo osakwatiwa, omwe ali ndi zaka za pakati pa 23 ndi 65, kuti akhale ndi makhalidwe amene angawathandize kukwanitsa utumiki wawo komanso kuti akhale ndi luso lomwe lingachititse kuti Yehova komanso gulu lake liwagwiritse ntchito.

Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Mu Chiheberi mawu akuti “Giliyadi” amatanthauza “Mulu wa Umboni.” Kuyambira pamene sukuluyi inayamba mu 1943, anthu oposa 8,000 omwe analowa m’sukuluyi anatumizidwa monga amishonale kuti akachitire umboni “kumalekezero a dziko lapansi” ndipo zinthu zakhala zikuyenda bwino kwambiri. (Machitidwe 13:47) Mwachitsanzo, pamene amishonale anafika ku Peru, anapeza kuti m’dzikomo munalibe mpingo ngakhale umodzi. Koma panopa kuli mipingo yoposa 1,000. Amishonale atafikanso m’dziko la Japan anapeza kuti kuli Mboni zosapitirira 10. Koma panopa kuli Mboni zoposa 200,000. Sukuluyi imatenga miyezi 5 ndipo amaphunzira Mawu a Mulungu mozama kwambiri. Amishonale amene sanaloweko m’sukuluyi, apainiya apadera, amene akutumikira m’maofesi a nthambi kapena oyang’anira dera, amatha kuitanidwa kuti akalowe m’sukuluyi n’cholinga choti azitsogolera komanso kulimbikitsa ntchito yolalikira imene ikuchitika pa dziko lonse.

  • Kodi cholinga cha sukulu ya Utumiki Waupaniya n’chiyani?

  • Kodi ndani angalowe nawo mu Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?