MUTU 12
Analimbikitsidwa ndi Mulungu Wake
1, 2. Kodi chinachitika n’chiyani pa tsiku lapadera kwambiri pa moyo wa Eliya?
ELIYA anali akuthamanga pa mvula pa ulendo wake wopita ku Yezereeli ndipo pa nthawiyi kunja n’kuti kuli mdima wamvulayo. Panali padakali ulendo wautali kuti akafike ku Yezereeli komanso anali munthu wachikulire. Ngakhale zinali choncho, iye ankathamanga osatopa chifukwa “dzanja la Yehova” linali naye. Pa nthawiyi, anali ndi mphamvu zoti sanakhalepo nazo chiyambire moti anathamanga mpaka kupitirira gulu la mahatchi amene ananyamula Mfumu Ahabu pa galeta lake lachifumu.—Werengani 1 Mafumu 18:46.
2 Yerekezerani kuti mukuona Eliya akuthamanga yekhayekha kwinaku madzi amvula akuyenderera nkhope yake yonse. Pa nthawi yonse imene ankathamangayi ayenera kuti ankangoganizira zinthu zosaiwalika zimene zinachitika pa tsikuli. Tsopano Eliya sakanathanso kuona phiri la Karimeli chifukwa pa nthawiyi n’kuti lili kutali kwambiri ndiponso kunja kunali mitambo ya mvula. N’zosachita kufunsa kuti zimene zinachitika paphiri la Karimeli tsiku limenelo zinachititsa kuti Mulungu wa Eliya atamandidwe komanso zinakweza kulambira koona. Paphiri limeneli ndi pamene Yehova anagwiritsa ntchito Eliya kugonjetsa mwamphamvu komanso mozizwitsa anthu olambira Baala. Aneneri a Baala ambirimbiri anadziwika kuti anali achinyengo komanso oipa ndipo anaphedwa. Kenako Eliya anapemphera kwa Yehova kuti chilala chimene chinachitika kwa zaka zitatu ndi hafu chithe. Mulungu anayankhadi pempheroli moti mvula inayamba kugwa.—1 Maf. 18:18-45.
3, 4. (a) Pa nthawi imene Eliya ankapita ku Yezereeli, n’chifukwa chiyani ankaganiza kuti zinthu zisintha? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
3 Pamene Eliya ankathamanga pa ulendowu, womwe unali wamakilomita 30, kupita ku Yezereeli ayenera kuti ankaganiza zoti mmene zateremu ndiye kuti zinthu zikhala bwino chifukwa Ahabu asintha. Iye ankaganiza kuti zimene Ahabu anaona pa tsikuli zimuchititsa kuti asiye kulambira Baala, aletse mkazi wake kuchita zinthu zoipa komanso kuti asiye kuzunza atumiki a Yehova.
4 Zinthu zikayamba kutiyendera bwino, mwachibadwa timayamba kuganiza kuti ndiye kuti zipitirizabe kuyenda choncho. Mwinanso timayamba kuganiza kuti ngakhale mavuto aakulu amene tinali nawo atha. N’kutheka kuti Eliya anaganizanso choncho chifukwa iye “anali munthu monga ife Yak. 5:17) Koma chimene Eliya sanadziwe n’choti mavuto ake anali akungoyamba kumene. Sanadziwenso kuti pasanapite nthawi yaitali akumana ndi zinthu zochititsa mantha komanso zodetsa nkhawa kwambiri moti alakalaka kufa. Kodi chinachitika n’chiyani? Nanga kodi Yehova anathandiza bwanji mneneri wakeyu kuti akhalenso ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti ayambirenso kuchita zinthu molimba mtima? Tiyeni tione.
tomwe.” (Zinthu Zinasintha Mwadzidzidzi
5. Kodi Ahabu anaphunzira kulemekeza Yehova pa zimene zinachitika kuphiri la Karimeli? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?
5 Kodi Ahabu atafika kunyumba yake yachifumu ku Yezereeli anachita zilizonse zosonyeza kuti wasintha ndipo wayamba kukonda Mulungu? Ayi, chifukwa Baibulo limati: “Ahabu anauza Yezebeli zonse zimene Eliya anachita, ndiponso mmene anaphera aneneri onse ndi lupanga.” (1 Maf. 19:1) Onani kuti pofotokozera mkazi wake zimene zinachitika tsiku limenelo, Ahabu sanatchule Yehova, Mulungu wa Eliya. Iye sankaona zinthu mwauzimu ndipo sankaganiza kuti zodabwitsa zimene zinachitikazo, zachitika ndi mphamvu ya Mulungu. N’chifukwa chake ananena kuti, ‘zimene Eliya wachita.’ Apa n’zoonekeratu kuti Ahabu sanaphunzire kulemekeza Yehova Mulungu. Ndiyeno kodi mkazi wake, yemwe anali ndi mtima wofuna kubwezera, anachita chiyani?
6. Kodi Yezebeli anatumiza uthenga wotani kwa Eliya, nanga ankatanthauza chiyani ponena zimenezi?
6 Yezebeli anakwiya kwambiri. Kenako anatumiza uthenga kwa Eliya wonena kuti: “Milungu yanga indilange mowirikiza, ngati pofika nthawi ino mawa sindidzachititsa moyo wako kukhala ngati moyo wa aliyense wa aneneriwo.” (1 Maf. 19:2) Apatu Yezebeli anaopseza Eliya kuti amupha zivutezitani. Iye analumbira kuti ngati tsiku lingathe asanaphe Eliya, pobwezera imfa ya aneneri a Baala, ndiye kuti iyeyo ayenera kufa. Taganizirani mmene Eliya anamvera atadzutsidwa m’kanyumba kamene anagona ku Yezereeli usiku umenewu mphepo ikuwomba, n’kumva uthenga wochititsa mantha umenewu wochokera kwa mkazi wa mfumu. Kodi iye anatani atamva zimenezi?
Anakhumudwa Kwambiri Ndiponso Anachita Mantha
7. Kodi Eliya anamva bwanji atalandira uthenga wochokera kwa Yezebeli, ndipo anachita chiyani?
7 Ngati Eliya ankanyadira kuti nkhondo yolimbana ndi olambira Baala yatha, ndiye kuti anakhumudwa kwambiri atauzidwa uthenga umenewu. Zimene zinachitikazo sizinapangitse Yezebeli kusintha. Anthu ambiri okhulupirika ngati Eliya anali ataphedwa kale potsatira zimene Yezebeli analamula ndipo tsopano Eliya anaona kuti nayenso aphedwa basi. Kodi Eliya anamva bwanji atalandira uthengawu? Baibulo limanena kuti: “Eliya anachita mantha.” Kodi Eliya ankaona m’maganizo mwake imfa yowawa imene Yezebeli anamukonzera? Ngati iye ankangoganizira zimenezo, 1 Maf. 18:4; 19:3.
n’zosadabwitsa kuti anachita mantha kwambiri. Choncho Eliya ‘anayamba kuthawa kuti apulumutse moyo wake.’—Ngati tikufuna kupitirizabe kuchita zinthu molimba mtima, tiyenera kupewa kumangoganizira zinthu zimene zikutichititsa mantha
8. (a) Kodi zimene zinachitikira Petulo zikufanana bwanji ndi zimene zinachitikira Eliya? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Eliya ndi Petulo?
8 Palinso anthu ena amene anali ndi chikhulupiriro ngati Eliya amene pa nthawi ina anachita mantha. Mwachitsanzo, patapita zaka zambiri kuchokera nthawi ya Eliya, mtumwi Petulo nayenso anachita mantha. Pamene Yesu anamulola Petulo kuti ayende pamadzi, mtumwiyu anayamba kuyang’ana “mphepo yamkuntho.” Kenako anachita mantha ndipo anayamba kumira. (Werengani Mateyu 14:30.) Chitsanzo cha Petulo ndi cha Eliya chikutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri. Ngati tikufuna kupitirizabe kuchita zinthu molimba mtima, tiyenera kupewa kumangoganizira zinthu zimene zikutichititsa mantha. Tiyenera kudalira kwambiri Yehova yemwe amatipatsa mphamvu komanso chiyembekezo.
“Basi Ndatopa Nazo”
9. Fotokozani mmene Eliya anayendera pothawa Yezebeli ndiponso mmene ankamvera.
9 Chifukwa cha mantha, Eliya anayenda ulendo wa makilomita 150 kukafika ku Beere-seba, tauni yomwe inali kum’mwera kwa dziko la Yuda. Atafika kumeneko, anasiya mtumiki wake ndipo anapita yekha kuchipululu. Nkhaniyi imati anayenda “ulendo wa tsiku limodzi,” choncho n’kutheka kuti ananyamuka m’mawa dzuwa litangotuluka kumene. Pa ulendo wakewu ayenera kuti sanatenge chakudya, madzi akumwa ndiponso zinthu zina zofunika. Chifukwa cha mantha, Eliya anadutsa m’malo ovuta monga m’mapiri komanso m’chipululu, ndipo pa nthawiyi n’kuti dzuwa likuswa mtengo. Pomwe dzuwa linkalowa, n’kuti Eliya atatopa kwambiri. Choncho anakhala pansi pa kamtengo kenakake kopanda mthunzi wambiri komwe anakapeza m’chipululumo.—1 Maf. 19:4.
10, 11. (a) Kodi Eliya ankadziona bwanji pamene ankapemphera kwa Yehova? (b) Pogwiritsa ntchito malemba amene ali kumapeto kwa ndime 11, fotokozani mmene atumiki ena a Mulungu anamvera atakumana ndi mavuto.
10 Ali pamenepo, Eliya anapemphera mosonyeza kuti wapanikizika kwambiri ndipo anapempha Mulungu kuti angofa. Iye anati: “Sindine woposa makolo anga.” Iye ankadziwa kuti makolo ake amene anamwalira sangathe kuchita chilichonse. (Mlal. 9:10) Choncho Eliya ankadziona kuti ndi wosafunika ndipo panalibe chifukwa choti azikhalabe ndi moyo. N’chifukwa chake ananena kuti: “Basi ndatopa nazo.”
11 Kodi n’zodabwitsa kuti munthu wa Mulungu anada nkhawa ndiponso kukhumudwa kwambiri chonchi? Ayi, chifukwa Baibulo limanena za atumiki a Yehova ena amene nthawi ina anavutika maganizo kwambiri moti analakalaka atangofa. Ena mwa anthu amenewa ndi Rabeka, Yakobo, Mose ndi Yobu.—Gen. 25:22; 37:35; Num. 11:13-15; Yobu 14:13.
12. Mukavutika maganizo kwambiri, kodi mungatsanzire bwanji Eliya?
2 Tim. 3:1) Zoterezi zikakuchitikirani, tsanzirani zimene Eliya anachita. Pempherani kwa Mulungu ndi kumuuza nkhawa zanu zonse. Musaiwale kuti Yehova ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Kodi Yehova anatonthoza, kapena kuti kulimbikitsa Eliya?
12 Tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” Choncho n’zosadabwitsa kuona kuti anthu ambiri, ngakhale atumiki a Mulungu, nthawi zina amavutika maganizo kwambiri chifukwa cha zimene akumana nazo pa moyo wawo. (Yehova Anathandiza Mneneri Wake
13, 14. (a) Kudzera mwa mngelo, kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankadera nkhawa mneneri wake? (b) N’chifukwa chiyani n’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amadziwa bwino munthu aliyense moti amadziwanso zimene sitingakwanitse?
13 Kodi mukuganiza kuti Yehova anamva bwanji pamene anayang’ana ali kumwambako n’kuona mneneri wake wokondedwa atagona m’chipululu pansi pa kamtengo akupempha kuti angofa? Kuti tidziwe mmene Yehova anamvera, tiyeni tione zimene zinachitika. Eliya ali mtulo, Yehova anatumiza mngelo. Mngeloyo anamugwedeza Eliya pang’onopang’ono ndipo anamuuza kuti: “Dzuka udye.” Eliya anadzukadi ndipo anadya mkate wotentha ndiponso anamwa madzi amene mngeloyo anamubweretsera. Sitikudziwa ngati Eliya anathokoza mngeloyo chifukwa nkhaniyi imangofotokoza kuti mneneriyu anadya ndi kumwa kenako n’kugonanso. N’kutheka kuti Eliya sanathokoze chifukwa chakuti anali atakhumudwa kwambiri moti sankafuna kulankhula. Komabe patapita nthawi mngeloyo anadzutsanso Eliya ndipo mwina tsopano unali m’bandakucha. Apanso mngeloyo anauza Eliya kuti: “Dzuka udye,” ndipo anawonjezeranso kuti: “Popeza ulendowu wakukulira.”—1 Maf. 19:5-7.
14 Yehova anathandiza mngeloyo kudziwa kumene Eliya ankapita. Mngeloyu anadziwanso kuti Eliya sakanatha kuyenda ulendowu mwa mphamvu zake zokha chifukwa unali wautali. Ndiyetu n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu amene timamutumikira amadziwa bwino maganizo athu komanso zimene sitingakwanitse. (Werengani Salimo 103:13, 14.) Kodi chakudyachi chinamuthandiza bwanji Eliya?
15, 16. (a) Kodi chakudya chimene Eliya anapatsidwa ndi Yehova chinamuthandiza bwanji? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira mmene Yehova akuthandizira atumiki ake masiku ano?
15 Baibulo limati: “Anadzuka ndipo anadya ndi kumwa. Atatero, anapeza mphamvu zokwanira moti anatha kuyenda masiku 40, usana ndi usiku, mpaka kukafika kuphiri la Mulungu woona la Horebe.” (1 Maf. 19:8) Eliya anasala kudya kwa masiku 40, usana ndi usiku. Zimenezi ndi zofanana ndi zimenenso Mose anachita zaka pafupifupi 600 m’mbuyomo. N’zofanananso ndi zimene Yesu anachita patatha zaka pafupifupi 1,000 kuchokera pamene Eliya anamwalira. (Eks. 34:28; Luka 4:1, 2) Sikuti chakudya chimene Eliya anadya tsiku limeneli chinathetsa mavuto ake onse, komabe chinamuthandiza mozizwitsa. Tangoganizani, munthu wachikulire ngati ameneyu anayenda movutikira m’chipululumo kwa pafupifupi mwezi ndi hafu.
Mat. 4:4) Tikamaphunzira Mawu a Mulungu ndiponso mabuku othandiza kumvetsa Baibulo, timapeza chakudya chauzimu. Ngakhale kuti zimene timaphunzirazo sizingachititse kuti mavuto athu onse athe, zingatithandize kupirira mavuto amene patokha sitikanatha kuwapirira. Zingatithandizenso kuti tidzapeze “moyo wosatha.”—Yoh. 17:3.
16 Masiku anonso Yehova amathandiza atumiki ake, osati powapatsa chakudya mozizwitsa, koma mwa njira ina yofunika kwambiri kuposa imeneyi. Iye amathandiza atumiki ake powapatsa chakudya chauzimu. (17. Kodi Eliya anapita kuti ndipo n’chifukwa chiyani malo amenewa anali ofunika?
17 Eliya anayenda makilomita pafupifupi 320 mpaka kukafika kuphiri la Horebe. Kuphiri limeneli ndi kumene zaka zambiri m’mbuyomo Yehova Mulungu, kudzera mwa mngelo, anaonekera kwa Mose m’chitsamba choyaka moto. N’kumenenso Yehova anachita pangano la Chilamulo ndi Aisiraeli. Atafika kuphiri limeneli, Eliya analowa kuphanga.
Mmene Yehova Analimbikitsira Mneneri Wake
18, 19. (a) Kodi mngelo wa Yehova anamufunsa Eliya funso lotani, ndipo iye anayankha bwanji? (b) Kodi Eliya anasonyeza kuti ankada nkhawa pa zifukwa zitatu ziti?
18 Ndiyeno Eliya anamva “mawu” a Yehova, mwina kudzera mwa mngelo, akumufunsa kuti: “Ukufuna chiyani kuno Eliya?” N’zachidziwikire kuti funsoli linafunsidwa mokoma mtima chifukwa linachititsa kuti Eliya afotokoze zakukhosi kwake. Iye anati: “Ndachitira nsanje kwambiri inu Yehova Mulungu wa makamu, chifukwa ana a Isiraeli asiya pangano lanu. Agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti achotse moyo wanga.” (1 Maf. 19:9, 10) Mawu a Eliya amenewa akusonyeza zinthu zitatu zomwe zinamuchititsa kuti ade nkhawa kwambiri.
19 Choyamba, Eliya ankaona kuti ntchito yonse imene anagwira inangopita pachabe. Iye ‘anachita nsanje kwambiri’ potumikira Yehova kutanthauza kuti anayesetsa kukweza dzina lopatulika la Mulungu ndiponso anayesetsa kuti anthu adziwe kuti Yehova ndiye Mulungu woyenera kumulambira. Koma ngakhale kuti anachita zonsezi, ankaona kuti zinthu zikungoipiraipira. Anthu anapitirizabe kukhala osakhulupirika komanso osamvera ndipo kulambira konyenga kunali ponseponse. Chachiwiri, Eliya ankaona kuti watsala yekhayekha. Iye ananena kuti: “Ine ndatsala ndekhandekha,” ngati kuti mu Aisiraeli monse ndi iye yekha amene anatsala akulambirabe Yehova. Chachitatu, Eliya anali ndi mantha kwambiri chifukwa aneneri anzake anali ataphedwa ndipo ankangoona kuti nayenso aphedwa basi. Eliya sanalole kuti kunyada kapena manyazi zimulepheretse kufotokoza mmene ankamvera. Iye anapemphera kwa Mulungu kuchokera pansi pa mtima ndipo chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwa atumiki onse okhulupirika a Yehova.—Sal. 62:8.
20, 21. (a) Fotokozani zimene Eliya anaona ataima pakhomo la phanga paphiri la Horebe. (b) Kodi zimene Yehova anasonyeza Eliya zinamuthandiza bwanji?
20 Eliya atafotokoza zinthu zimene zinkamuchititsa mantha ndiponso kumudetsa nkhawa, kodi Yehova anamuthandiza bwanji? Mngelo uja anauza Eliya kuti aimirire pakhomo la phanga limene anabisalako. Eliya anachitadi zimenezi ngakhale kuti sankadziwa kuti chichitike n’chiyani. 1 Maf. 19:11, 12.
Mwadzidzidzi pamalopo panawomba chimphepo. Payenera kuti panamveka chiphokoso chifukwa chimphepocho chinali champhamvu kwambiri moti chinang’amba mapiri ndi matanthwe. Ndiyeno yerekezerani kuti mukuona Eliya akuyesetsa kuphimba nkhope yake kwinaku atagwira mwamphamvu chovala chake chokhuthala chaubweya chomwe chinkauluzika ndi chimphepocho. Iye akuyesetsanso kuti aime bwinobwino n’cholinga chakuti asagwe chifukwa pamalo amene waimawo nthaka ikugwedezeka chifukwa cha chivomezi. Koma chimphepo ndiponso chivomezi chija chitangotha, pakubuka moto ndipo izi zikuchititsa Eliya kubwerera kuphanga pothawa kutentha kwa motowo.—21 Nkhaniyi imafotokoza kuti Yehova sanali mu zinthu zachilengedwe monga mphepo, chivomezi ndiponso moto zimene Eliya anaonazi. Eliya ankadziwa kuti Yehova si mulungu wongoganiziridwa kuti alipo ngati mmene zinalili ndi Baala amene anthu omwe ankamulambira ankamutamanda kuti ndi woyendetsa mitambo, kapena kuti wobweretsa mvula. Mphamvu zochititsa mantha zimene zili m’zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe, zinachokera kwa Yehova. Koma iye ndi wamkulu kwambiri kuposa chilichonse chimene analenga. Ndipo ngakhale kumwamba kumene timaonaku, Yehova sangakwaneko. (1 Maf. 8:27) Ndiyeno kodi zimene Eliya anaonazi zinamuthandiza bwanji? Kumbukirani kuti Eliya anapezeka pamalo amenewa chifukwa chochita mantha. Popeza kuti Yehova Mulungu, yemwe ali ndi mphamvu zimenezi, anali kumbali ya Eliya, panalibe chifukwa chakuti iye aziopa Ahabu ndi Yezebeli.—Werengani Salimo 118:6.
22. (a) Kodi “mawu achifatse apansipansi” anatsimikizira bwanji Eliya kuti ndi munthu wofunika? (b) Kodi “mawu achifatse apansipansi” ayenera kuti anali a ndani? (Onani mawu a m’munsi.)
22 Moto uja utapita, pamalopo panakhala bata ndipo Eliya anamva “mawu achifatse apansipansi.” Mawuwo anali omupempha kuti anenenso zakukhosi kwake ndipo zimenezi zinachititsa kuti kachiwirinso Eliya afotokoze zinthu zomwe zinkamudetsa nkhawa. * Zimenezi ziyenera kuti zinamulimbikitsanso kwambiri. Komanso mosakayikira, Eliya analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene “mawu achifatse apansipansi” aja anamuuza. Yehova anatsimikizira Eliya kuti ndi munthu wofunika. Kodi anachita bwanji zimenezi? Mulungu anamuuza kuti nkhondo yothetsa kulambira Baala mu Isiraeli ipitirizabe. Ndiyetu apa n’zoonekeratu kuti ntchito imene Eliya anagwira sinapite m’madzi chifukwa Mulungu anali akuyendetsabe zinthu kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. Komanso, Yehova anali akugwiritsabe ntchito Eliya popeza anamupatsa malangizo omveka bwino n’kumuuza kuti abwerere akagwire ntchito yomweyi.—1 Maf. 19:12-17.
23. Kodi Yehova anathandiza bwanji Eliya pa vuto lake loona kuti watsala yekhayekha?
23 Kodi Yehova anathandiza bwanji Eliya pa vuto lake loona kuti watsala yekhayekha? Iye anachita zinthu ziwiri. Choyamba, anauza Eliya kuti akadzoze Elisa kukhala mneneri amene adzalowe m’malo mwake. Elisa, yemwe pa nthawiyo anali wachinyamata, anali kudzakhala mnzake wa Eliya komanso womuthandiza kwa zaka zambiri. Pamenepatu Yehova anamulimbikitsa kwambiri. Chachiwiri, Yehova anauza Eliya nkhani yabwino kwambiri. Iye anati: “Ine ndasiya anthu 7,000 mu Isiraeli, amene mawondo awo sanagwadirepo Baala, ndiponso pakamwa pawo sipanapsompsonepo Baala.” (1 Maf. 19:18) Choncho, Eliya sanatsale yekha. Eliya ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kumva kuti panalinso anthu ena okhulupirika masauzande ambiri amene anakana kulambira Baala. Iye anafunika kupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika kuti apereke chitsanzo kwa anthuwo makamaka pa nthawi imeneyi pamene zinthu sizinali bwino. Choncho, Eliya ayenera kuti analimbikitsidwadi kwambiri kumva “mawu achifatse apansipansi” amenewa ochokera kwa Mulungu wake.
Baibulo likhoza kukhala “mawu achifatse apansipansi” ngati titamaligwiritsa ntchito kuti lizititsogolera pa moyo wathu
24, 25. (a) Kodi masiku ano tingamvetsere bwanji “mawu achifatse apansipansi” a Yehova? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti Eliya analimbikitsidwa ndi zimene Yehova anamuuza komanso kumuonetsa?
24 Mofanana ndi Eliya, ifenso nthawi zina tingachite mantha chifukwa cha mphamvu zoopsa zimene zili m’chilengedwechi, ndipo mpake kumva choncho. Mphamvu zimene chilengedwechi chimasonyeza ndi umboni wakuti Mlengi ndi wamphamvu kwambiri. (Aroma 1:20) Masiku ano Yehova amagwiritsirabe ntchito mphamvu zake zopanda malirezo pothandiza atumiki ake okhulupirika. (2 Mbiri 16:9) Komabe njira yaikulu imene Mulungu amalankhulira ndi anthu ake ndi mwa kudzera m’Mawu ake, Baibulo. (Werengani Yesaya 30:21.) Choncho, Baibulo likhoza kukhala “mawu achifatse apansipansi” ngati titamaligwiritsa ntchito kuti lizititsogolera pa moyo wathu. Pogwiritsa ntchito Baibulo, Yehova amatilangiza, kutilimbikitsa komanso kutitsimikizira kuti amatikonda kwambiri.
25 Kodi Eliya anaonadi kuti Yehova wamulimbikitsa ndi zimene anamuuza ndiponso zimene anamusonyeza paphiri la Horebe? Inde, chifukwa pasanapite nthawi yaitali, mneneriyu anayambiranso kugwira ntchito yake yolimbana ndi kulambira konyenga ndipo anachita zimenezi molimba mtima ndiponso mokhulupirika ngati mmene ankachitira poyamba. Ifenso tikamatsatira Mawu ouziridwa a Mulungu, kapena kuti ‘malemba amene amatilimbikitsa,’ tidzatha kutsanzira chikhulupiriro cha Eliya.—Aroma 15:4.
^ ndime 22 “Mawu achifatse apansipansi” amenewa ayenera kuti anali a mngelo amene anagwiritsidwanso ntchito kunena “mawu a Yehova” amene ali palemba la 1 Mafumu 19:9. Pa vesi 15 mngelo ameneyu anangotchulidwa kuti “Yehova.” Zimenezi zingatikumbutse mngelo yemwe Yehova anamugwiritsira ntchito kutsogolera Aisiraeli m’chipululu. Ponena za mngelo ameneyu, Mulungu anati: “Dzina langa lili mwa iye.” (Eks. 23:21) Ngakhale kuti Baibulo silinena mwatchutchutchu kuti mngelo amene analankhula ndi Eliya anali Yesu, mfundo yofunika kuidziwa ndi yakuti Yesu asanabwere padziko lapansi, Yehova ankamugwiritsa ntchito monga “Mawu,” kapena kuti Womulankhulira.—Yoh. 1:1.