Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Mungathe Kuthetsa Vuto Loseweretsa Maliseche

Mungathe Kuthetsa Vuto Loseweretsa Maliseche

A Kuseweretsa maliseche pofuna kukhutiritsa chilakolako chogonana ndi chizolowezi chimene Mulungu amadana nacho, ndipo chimapangitsa munthu kumangofuna kudzisangalatsa yekha komanso kumangoganizira zoipa. Munthu amene amadziseweretsa maliseche, amayamba kuona anthu ena ngati pongothetsera chilakolako chogonana basi. Iye amaganiza kuti kugonana si njira yosonyezerana chikondi, koma pongothetsera chilakolako chogonana kuti asangalale kwa kanthawi kochepa. Komatu, sikuti chilakolako chogonanacho chimatheratu. Zoona zake n’zakuti, m’malo mochititsa ziwalo za thupi kukhala zakufa “ku dama, zinthu zodetsa, [ndi] chilakolako cha kugonana [chosayenera],” kuseweretsa maliseche kumadzutsa zilakolakozo.​—Akolose 3:5.

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Okondedwanu, . . . tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Ngati zikukuvutani kutsatira mawu amenewa, musataye mtima. Yehova nthawi zonse ndi wokonzeka ‘kukhululuka’ komanso kukuthandizani (Salimo 86:5; Luka 11:​9-13) Kunena zoona, ngati mumadziimba mlandu ndipo mukuyesetsa kusiya chizolowezichi ngakhale kuti nthawi zina mumabwerezanso khalidweli, ndiye kuti muli ndi mtima wabwino. Kumbukiraninso kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yohane 3:20) Mulungu amadziwa zonse zokhudza munthu aliyense, osati zochimwa zathu zokha. Chifukwa chodziwa zimenezi, iye amatimvetsera tikamalimbikira kupemphera ndipo amatichitira chifundo. Choncho, musatope kuthawira kwa Yehova modzichepetsa ndi kulimbikira kupemphera monga mmene mwana amathawira kwa bambo ake akakumana ndi mavuto. Yehova angakuthandizeni kuti mukhale ndi chikumbumtima choyera. (Salimo 51:​1-12, 17; Yesaya 1:18) Komabe, muyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero anu. Mwachitsanzo, muzipewa zinthu zilizonse zolaula komanso kucheza ndi anthu oipa. *

Ngati mukulepherabe kuthetsa vuto loseweretsa maliseche, tikukupemphani kuti mufotokozere kholo lanu lachikhristu kapena mnzanu wapamtima wachikulire mwauzimu. *​—Miyambo 1:​8, 9; 1 Atesalonika 5:14; Tito 2:​3-5.

^ ndime 2 Pofuna kupewa kugwiritsa ntchito kompyuta molakwika, mabanja ambiri amaiika pamalo oonekera. Komanso ena amagula mapulogalamu otetezera kuti zinthu zosayenera zisalowe mu kompyuta yawo. Komabe, palibe pulogalamu imene ingatetezeretu kompyuta yanu ku zinthu zosayenera.

^ ndime 1 Kuti mudziwe zinthu zina zimene mungachite kuti muthetse vuto loseweretsa maliseche, onani nkhani yakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Ndingathetse Bwanji Chizolowezi Chimenechi?” mu Galamukani! ya November 2006, ndiponso buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba, patsamba 178 mpaka 182.