Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndi Ndani Anayamba Kuzipanga?

Kodi Ndi Ndani Anayamba Kuzipanga?

M’zaka zaposachedwapa, asayansi ndi mainjiniya aphunzira zambiri pa zomera ndi zinyama. (Yobu 12:7, 8) Masiku ano, akutsanzira zinthu zachilengedwe popanga zinthu zatsopano kapena posintha zinthu zakale kuti zikhale zabwinopo. Mukamawerenga zitsanzo zotsatirazi, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi ndani amene ayenera kulandira ulemu chifukwa chopanga zinthu zimenezi?’

Zimene Anthu Angachite Potsanzira Nangumi

Kodi anthu opanga ndege angapange chiyani potsanzira nangumi wotchedwa Humpback? Nangumi ameneyu amalemera makilogalamu pafupifupi 30,000, ali ndi thupi lolimba ndipo m’mbali mwake ali ndi zinthu zokhala ngati mapiko. Amakhala wamtali mamita 12 koma amayenda mosavutikira m’madzi.

Asayansi anachita chidwi kwambiri ndi mmene nangumiyu amakhotera mosavutikira. Iwo anazindikira kuti chimene chimathandiza kuti azichita zimenezi ndi zinthu zokhala ngati mapiko zimene ali nazo. M’mbali mwa zinthu zimenezi ndi mwa timabampumabampu, osati mosalala ngati mapiko a ndege.

Nangumiyu akamayenda m’madzi, timabamputi timathandiza kuti aziyenda mosavuta. Magazini ina inanena kuti timabampu timeneti timathandiza kuti madzi azidutsa bwinobwino pamwamba pa zinthu zokhala ngati mapikozo popanda kumukankhira m’mbuyo, ngakhale pamene nangumiyo akupita m’mwamba.​—Natural History.10

Kodi ndi ndani anapanga zinthu za m’chilengedwe?

Kodi akatswiri akhoza kugwiritsa ntchito bwanji zimene atulukirazi? Ngati atatsanzira nangumiyu, akhoza kupanga mapiko a ndege popanda kugwiritsa ntchito zitsulo zambiri zothandiza kuti mphepo izidutsa bwinobwino osaikankhira m’mbuyo. Mapiko oterewa angathandize kupewa ngozi komanso sangawonongeke msanga. Katswiri wina dzina lake John Long ananena kuti akukhulupirira zoti posachedwapa “ndege iliyonse izikhala ndi mapiko okhala ndi timabampumabampu ofanana ndi nangumi ameneyu.”11

Zimene Anthu Achita Potsanzira Mapiko a Mbalame

N’zoona kuti kuyambira kale anthu amapanga mapiko a ndege potsanzira mapiko a mbalame. Koma posachedwapa, akatswiri ena atulukira zinthu zina zothandiza pa nkhaniyi. Magazini ina inanena kuti “akatswiri a pa yunivesite ya Florida apanga kandege kouluka mopanda munthu [ka masentimita 61] koyendera limoti komwe kamatha kuima malo amodzimodzi m’mwamba komanso kutsika ndi kukwera mofulumira kwambiri. Achita zimenezi potsanzira mbalame yotchedwa Seagull.”​New Scientist.12

Mbalameyi imauluka modabwitsa chifukwa choti imatha kupinda mapiko ake pachigongono komanso paphewa lake. Magazini ija inanena kuti “kandegeka kali ndi kainjini kakang’ono kamene kamayendetsa tizitsulo tomwe timathandiza kuti mapiko ake aziyenda ngati a mbalameyi.” Izi zimathandiza kuti kazitha kuima malo amodzimodzi m’mwamba komanso kutsika pakati pa nyumba zitalizitali. Asilikali ena akufuna kupanga ndege yoti izitha kuchita zimenezi kuti aziigwiritsa ntchito pofufuza zida zoopsa m’mizinda imene ili ndi nyumba zambiri zitalizitali.

Zimene Anthu Achita Potsanzira Mwendo wa Mbalame

Mbalame yotchedwa Seagull imathanso kuima pa aisi kwa nthawi yaitali koma osafa ndi kuzizira. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Chinthu china chimene chimathandiza mbalameyi komanso nyama zambiri zimene zimakhala kumadera ozizira ndi mmene magazi amayendera m’mitsempha yake.

Zimene zimachitika m’miyendo zimathandiza kuti thupi likhalebe lotentha

Kuti timvetse mmene magazi amayendera m’mitsempha yake, tiganizire za mapaipi awiri a madzi amene amangiriridwa pamodzi. M’paipi imodzi mukuyenda madzi otentha pomwe inayo madzi ozizira. Ngati madzi a m’mapaipi onse awiri akuyenda kupita mbali imodzi, hafu ya kutentha ingapite m’paipi ya madzi ozizira. Koma ngati madziwo akuyenda kupita mbali zosiyana, pafupifupi kutentha konse kungapite m’paipi ya madzi ozizira.

Choncho mbalameyi ikaima pa aisi magazi amene amabwerera kuchokera m’mapazi ake amatenthedwa akamadutsana ndi magazi otentha amene akuchokera m’thupi lake. Izi zimathandiza kuti mbalameyo isazizidwe kwambiri. Katswiri wina dzina lake Arthur P. Fraas ananena kuti “zimene zimachitika m’miyendo ya mbalameyi n’zochititsa chidwi kwambiri.”13 M’pake kuti anthu akuzitsanzira popanga zinthu zina.

Kodi Ndi Ndani Ayenera Kupatsidwa Ulemu?

Galimoto imene anaipanga potsanzira nsomba yooneka ngati bokosi

Panopa bungwe lina (National Aeronautics and Space Administration) likupanga mashini okhala ndi miyendo yambiri amene amayenda ngati chinkhanira. Ndipo ku Finland mainjiniya apanga kale thilakitala yamiyendo 6 imene imatha kukwera zinthu ngati mmene tizilombo tingachitire. Asayansi ena apanga nsalu yokhala ndi tinthu tangati mamba, potsanzira mmene zibalobalo za mtengo wa paini zimatsegukira ndi kutsekekera. Nsalu zoterezi zimasintha mogwirizana ndi kutentha kapena kuzizira kwa thupi la munthu amene wavala. Kampani ina yopanga magalimoto ikupanga galimoto potsanzira nsomba inayake imene imaoneka ngati bokosi ndipo imatha kuyenda mofulumira m’madzi. Anthu ena akufufuza za zigoba za nkhono zinazake zomwe sizisweka msanga. Akuchita zimenezi n’cholinga choti apange zida zopepuka koma zolimba zimene munthu angavale podziteteza.

Anthu amayesetsa kutsanzira mmene nsomba zotchedwa dolphin zimamvera zinthu zikakhala m’madzi

Pali zinthu zambiri zimene anthu angatsanzire m’chilengedwechi ndipo asayansi apanga pulogalamu yapakompyuta imene analembamo zinthu zimene angatsanzirezi. Magazini ina inanena kuti asayansi akhoza kufufuza zinthu pogwiritsa ntchito pulogalamuyi kuti apeze “njira yopangira zinthu zina potsanzira zinthu zachilengedwe.” (The Economist) Zinthu zimene zimapezeka mupulogalamuyi amazitchula kuti “zopangidwa m’chilengedwe.” Nthawi zambiri anthu kapena makampani akapanga chinthu chatsopano amalembetsa kuti ndi iwowo amene anachipanga. Ndiyeno magazini ija inanenanso kuti dzina limene anapereka ku zinthu zopezeka mupulogalamuyi likusonyeza kuti “nthawi zambiri luso limayambira ku zinthu zachilengedwe.”14

Asayansi akufufuza zimene zimathandiza kuti zigoba zinazake zisamasweke msanga

Koma kodi zinatheka bwanji kuti m’chilengedwe muzipezeka zinthu zogometsa chonchi? Asayansi ambiri amanena kuti izi zinachitika chifukwa choti zinthu zakhala zikusintha pazokha kwa zaka zambirimbiri. Koma pali asayansi ena amene amaganiza mosiyana ndi zimenezi. Mwachitsanzo, wasayansi wina dzina lake Michael J. Behe analemba munyuzipepala ina kuti: “Kuchuluka kwa zinthu zomwe zimaoneka kuti zinapangidwa mwaluso kwambiri [m’chilengedwe] kumatifikitsa pa mfundo yosavuta koma yomveka bwino yakuti: Ngati chinthu chikuoneka ngati bakha, kuyenda ngati bakha komanso kulira ngati bakha, ndiye kuti chinthucho ndi bakha, ngati palibe umboni wina wotsutsa zimenezo.” (The New York Times ya pa February 7, 2005) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Iye anapitiriza kuti: “Ngati chinthu chikuonekeratu kuti chinachita kupangidwa ndi winawake, palibe chifukwa chilichonse chotsutsira zimenezo.”15

Nalimata ali ndi zinthu zomuthandiza kuti asamagwe pakhoma kapena pamalo ena osalala kwambiri

Munthu amene wapanga mapiko a ndege otetezeka komanso ouluka bwino ayenera kupatsidwa ulemu. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene wapanga zovala zabwino kapena injini yabwino ya galimoto. Ndipo munthu amene amapanga zinthu zina motsanzira zimene mnzake wapanga kale popanda kuvomereza kuti pali wina amene anapanga kale zinthuzo akhoza kuimbidwa mlandu.

Ndiye taganizirani izi: Akatswiri ambiri amayesa kutsanzira zinthu za m’chilengedwe pofuna kupanga zinthu zovuta. Koma ena amanena kuti zinthu za m’chilengedwezo zinangokhalako zokha. Kodi zimenezi n’zomveka? Ngati kutsanzira chinthu china kumafuna nzeru za munthu, kuli bwanji kupanga chinthu choyambiriracho? Ndipo kodi ndi ndani ayenera kupatsidwa ulemu waukulu, amene anayamba kupanga zinthu kapena amene anangozitsanzira?

Mfundo Imene Ena Azindikira

Anthu ambiri akaona umboni wakuti zinthu za m’chilengedwe zinachita kupangidwa ndi winawake, amagwirizana ndi mawu a m’Baibulo amene Paulo analemba akuti: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.”​—Aroma 1:19, 20.