Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 8 • MACHITIDWE 21:18–28:31

“Ankawalalikira za Ufumu wa Mulungu . . . Popanda Choletsa”

“Ankawalalikira za Ufumu wa Mulungu . . . Popanda Choletsa”

MACHITIDWE 28:31

M’gawoli tiyendera limodzi ndi Paulo kuchokera pamene anakumana ndi anthu achiwawa, anatsekeredwa m’ndende ndiponso pamene anaonekera kwa akuluakulu osiyanasiyana a Chiroma. Pa nthawi yonse imene ankakumana ndi mavutowa, mtumwiyu anapitiriza kulalikira za Ufumu wa Mulungu. Pamene mukuphunzira nkhani zosangalatsa zomaliza m’buku la Machitidwe, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatsanzire bwanji Paulo yemwe ankalalikira molimba mtima ndiponso mwakhama?’