Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 25

“Ndikuchita Apilo Kuti Ndikaonekere kwa Kaisara”

“Ndikuchita Apilo Kuti Ndikaonekere kwa Kaisara”

Paulo anatipatsa chitsanzo cha mmene tingatetezere uthenga wabwino

Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 25:1–26:32

1, 2. (a) Kodi Paulo anakumana ndi zotani? (b) Kodi ndi funso liti limene likubwera chifukwa choti Paulo anachita apilo kuti akaonekere kwa Kaisara?

 ASILIKALI anapitiriza kulondera Paulo ku Kaisareya. Zaka ziwiri m’mbuyomo atabwerera ku Yudeya, Ayuda ankafuna kumupha katatu konse pa masiku ochepa okha. (Mac. 21:27-36; 23:10, 12-15, 27) Pofika pa nthawiyi, adani akewo anali atalephera kukwaniritsa cholinga chawo, koma maganizo ofuna kumuchita chiwembu anali nawobe. Paulo ataona kuti akhoza kumuperekanso kwa adani akewo, anauza Fesito, bwanamkubwa wa Chiroma kuti: “Ndikuchita apilo kuti ndikaonekere kwa Kaisara.”​—Mac. 25:11.

2 Kodi Yehova anagwirizana ndi maganizo a Paulo akuti akaonekere kwa mfumu ya Roma? Yankho la funso limeneli ndi lofunika kwambiri kwa ife, amene tikuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu m’masiku otsiriza ano. M’pofunika kuti tidziwe ngati zimene Paulo anachitazo ndi chitsanzo choti tizitsanzira pa nkhani ‘yoteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito yolengeza uthenga wabwino.’​—Afil. 1:7.

“Ndaima Kutsogolo kwa Mpando Woweruzira Milandu” (Machitidwe 25:1–12)

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Ayuda anapempha kuti Paulo amubweretse ku Yerusalemu, nanga anapulumuka bwanji? (b) Kodi Yehova amathandiza bwanji atumiki ake masiku ano ngati mmene anathandizira Paulo?

3 Fesito anapita ku Yerusalemu patangopita masiku atatu atakhala bwanamkubwa wa Yudeya. a Kumeneko anamvetsera pamene ansembe aakulu ndi amuna olemekezeka pakati pa Ayuda ankaneneza Paulo milandu yoopsa kwambiri. Iwo ankadziwa kuti bwanamkubwa watsopanoyu ankadziwa zoti akuyenera kumakhala mwamtendere ndi iwowo komanso Ayuda onse. Choncho anapempha Fesito kuti awakomere mtima ndipo aitanitse Paulo kuti abwere ku Yerusalemu kuti akamuimbe mlandu kumeneko. Koma adani a Paulowo anali atakonza chiwembu kuti iye akamachoka ku Kaisareya kupita ku Yerusalemu, amudikirire panjira n’kumupha. Fesito anakana pempholi ndipo ananena kuti: “Amene ali ndi maudindo pakati panu, tipitire limodzi [ku Kaisareya] kuti ngati pali chilichonse chimene munthu ameneyu walakwa akamuimbe mlandu.” (Mac. 25:5) Apanso Paulo anapulumuka lokumbakumba.

4 Kudzera mwa Ambuye Yesu Khristu, Yehova anathandiza Paulo pa mayesero onse amene anakumana nawo. Kumbukirani kuti m’masomphenya, Yesu anauza mtumwi wakeyu kuti: “Limba mtima.” (Mac. 23:11) Masiku anonso atumiki a Mulungu amakumana ndi mavuto komanso amazunzidwa. N’zoona kuti Yehova samatiteteza ku mavuto onse, komabe amatipatsa nzeru ndiponso mphamvu kuti tithe kupirira. Choncho nthawi zonse tizidalira “mphamvu yoposa yachibadwa” imene Mulungu wathu wachikondi amapereka.​—2 Akor. 4:7.

5. Kodi Fesito anachita chiyani ndi nkhani ya Paulo?

5 Patapita masiku angapo, Fesito “anakhala pampando woweruzira milandu” ku Kaisareya. b Paulo ndi anthu amene ankamuneneza milandu aja anaima pabwalo loweruzira milandulo. Ndiyeno poyankha milandu imene ankamunamizirayo, Paulo anati: “Ine sindinachimwire Chilamulo cha Ayuda kapena kachisi kapenanso Kaisara.” Mtumwiyu analibe mlandu uliwonse ndipo ankayenera kumasulidwa. Ndiye kodi Fesito anatani? Pofuna kuti Ayudawo amukonde, iye anafunsa Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti nkhaniyi ikaweruzidwe kumeneko pamaso panga?” (Mac. 25:6-9) Amenewatu anali maganizo osathandiza chifukwa Paulo akanapita ku Yerusalemu kuti akaweruzidwe kumeneko, ndiye kuti omuimba mlanduwo ndi amene akanamuweruza ndipo mosakayikira akanamupha. Apatu Fesito analephera kuweruza nkhaniyi mwachilungamo chifukwa chofuna kusangalatsa anthu. Pa nthawi ina m’mbuyomo, Bwanamkubwa Pontiyo Pilato anachitanso zofanana ndi zimenezi pa mlandu wa Yesu, munthu wofunika kwambiri. (Yoh. 19:12-16) Masiku anonso oweruza angaweruze mopanda chilungamo pofuna kusangalatsa anthu ena. Choncho tisamadabwe makhoti akaweruza mopanda chilungamo pa milandu yokhudza anthu a Mulungu.

6, 7. N’chifukwa chiyani Paulo anachita apilo kuti akaonekera kwa Kaisara, ndipo pochita zimenezi anapereka chitsanzo chotani kwa Akhristu oona masiku ano?

6 Cholinga cha Fesito chofuna kuti Ayuda azimukonda chikanachititsa kuti Paulo aphedwe. Choncho pofuna kudziteteza, Paulo anagwiritsa ntchito ufulu wake wokhala nzika ya Roma. Iye anauza Fesito kuti: “Ine ndaima kutsogolo kwa mpando woweruzira milandu wa Kaisara, kumene ndiyenera kuweruzidwa. Ayuda sindinawalakwire chilichonse ngati mmene inunso mukuonera. . . . Ndikuchita apilo kuti ndikaonekere kwa Kaisara.” Munthu akapempha kukaonekera kwa Kaisara, nthawi zambiri zinali zosatheka kusintha pempho limeneli. Choncho Fesito anatsimikizira Paulo kuti: “Popeza wachita apilo kuti ukaonekere kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” (Mac. 25:10-12) Pochita apilo kuti akaweruzidwe ndi woweruza waudindo waukulu, Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwa Akhristu oona masiku ano. Anthu otsutsa akamafuna kuyambitsa “mavuto pogwiritsa ntchito malamulo,” a Mboni za Yehova amagwiritsanso ntchito malamulo a m’dziko lawo poteteza uthenga wabwino. c​—Sal. 94:20.

7 Choncho Paulo atasungidwa m’ndende kwa zaka zoposa ziwiri pa milandu yomunamizira, anapatsidwa mwayi wokaonekera kwa Kaisara ku Roma. Koma asananyamuke, wolamulira wina ankafuna kuonana naye.

Ngati mlandu wathu sunaweruzidwe mwachilungamo, timachita apilo kukhoti lalikulu

“Ine Ndinaona Kuti Ndimvere” (Machitidwe 25:13–26:23)

8, 9. N’chifukwa chiyani Mfumu Agiripa inapita ku Kaisareya?

8 Patapita masiku angapo kuchokera pamene Paulo anapempha kuti akaonekere kwa Kaisara, Mfumu Agiripa ndi mchemwali wake Berenike anapita ku Kaisareya “pa ulendo wa boma wokapereka ulemu” kwa bwanamkubwa watsopano Fesito. d Pa nthawi ya ulamuliro wa Roma, unali mwambo wawo kuti akuluakulu a boma ankakachezera bwanamkubwa amene wangoikidwa kumene pa udindowu komanso kumufunira zabwino. N’zosakayikitsa kuti cholinga cha Agiripa pofunira zabwino Fesito pa udindo wakewu, chinali kulimbitsa ubale komanso mgwirizano umene ukanawathandiza m’tsogolo.​—Mac. 25:13.

9 Fesito anauza Mfumu Agiripa za Paulo, ndipo Agiripa ananena kuti akufuna amve Pauloyo akulankhula. Ndiyeno tsiku lotsatira, olamulira awiriwo anakhala pamipando yoweruzira kuti amvetsere mlandu wa Paulo. Olamulirawa anachita zinthu modzionetsera posonyeza kuti anali ndi mphamvu komanso anali olemekezeka. Koma anthu sanachite chidwi ndi zimenezi, iwo anachita chidwi ndi mawu amene Paulo analankhula.​—Mac. 25:22-27.

10, 11. Kodi Paulo analemekeza bwanji Agiripa, ndipo mtumwiyu ananena chiyani kwa Mfumu Agiripa za moyo wake wakale?

10 Mwaulemu, Paulo anathokoza Mfumu Agiripa pomupatsa mwayi wodziteteza pamaso pake, ndipo anavomereza kuti mfumuyi inali katswiri pa miyambo yonse ya Ayuda komanso pa zonse zimene Ayudawo ankakangana. Kenako Paulo anafotokoza mmene moyo wake unalili poyamba. Iye anati: ‘Ndinali Mfarisi wa m’gulu limene limalambira mokhwimitsa zinthu kwambiri.’ (Mac. 26:5) Monga Mfarisi, Paulo ankayembekezera kubwera kwa Mesiya. Koma pa nthawiyi anali atakhala Mkhristu, ndipo ankalalikira molimba mtima kuti Yesu Khristu ndi Mesiya amene Ayudawo ankamuyembekezera kwa nthawi yaitali. Pa tsikuli, Paulo ankazengedwa mlandu chifukwa cha chikhulupiriro chimene iyeyo komanso anthu amene ankamuneneza mlanduwo anali nacho. Chikhulupirirochi chinali cha chiyembekezo chimene iwo anali nacho choti Mulungu adzakwaniritsa zimene analonjeza makolo awo. Agiripa anachita chidwi ndi zimene Paulo anafotokoza ndipo ankafuna kumva zambiri. e

11 Pofotokoza mmene kale ankazunzira Akhristu, Paulo anati: “Inetu ndinkaganiza kuti ndiyenera kuchita zambiri zotsutsana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti. . . . Popeza ndinali nditakwiya nawo kwambiri [otsatira a Khristu], ndinafika powazunza ngakhale m’mizinda yakunja.” (Mac. 26:9-11) Apatu sikuti Paulo ankakokomeza. Anthu ambiri ankadziwa kuti poyamba iye ankazunza Akhristu mwankhaza. (Agal. 1:13, 23) Ndiye mwina Agiripa ankadzifunsa kuti, ‘N’chiyani chinachititsa kuti munthu ameneyu asinthe?’

12, 13. (a) Kodi Paulo anafotokoza kuti chinachitika n’chiyani kuti akhale Mkhristu? (b) Kodi Paulo ankaponya bwanji ‘miyendo yake n’kumamenya zisonga zotosera’?

12 Mawu a Paulo otsatirawa akupereka yankho. Iye anati: “Ndinanyamuka ulendo wopita ku Damasiko nditapatsidwa mphamvu komanso chilolezo ndi ansembe aakulu. Koma ndili m’njira dzuwa lili pamutu, inu mfumu, ndinaona kuwala kochokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa ndipo kunandizungulira ineyo ndiponso anthu amene ndinali nawo pa ulendowu. Ndiyeno tonse titagwa pansi, ndinamva mawu akundiuza m’Chiheberi kuti, ‘Saulo! Saulo! N’chifukwa chiyani ukundizunza? Ukungovutika popitiriza kuchita ngati nyama imene ikuponya miyendo yake n’kumamenya zisonga zotosera.’ Koma ine ndinati: ‘Ambuye, ndinu ndani kodi?’ Ndipo Ambuye anati: ‘Ndine Yesu amene iwe ukumuzunza.’” f​—Mac. 26:12-15.

13 Paulo asanaone masomphenya odabwitsawa, mophiphiritsa iye ‘ankaponya miyendo yake n’kumamenya zisonga zotosera.’ Nyama yonyamula katundu imadzivulaza ikamaponya miyendo yake n’kumamenya zisonga zakuthwa zotosera. Mofanana ndi zimenezi, Paulo ankadzivulaza mwauzimu pochita zinthu zotsutsana ndi chifuniro cha Mulungu. Choncho Yesu amene anali ataukitsidwa anaonekera kwa Paulo pamsewu wopita ku Damasiko ndipo anathandiza munthu woona mtimayu amene anali atasocheretsedwa kuti asinthe maganizo.​—Yoh. 16:1, 2.

14, 15. Kodi Paulo ananena kuti moyo wake unasintha bwanji?

14 Paulo anasinthadi kwambiri pa moyo wake. Polankhula ndi Agiripa, iye anati: “Ine ndinaona kuti ndimvere zimene ndinaona m’masomphenya akumwambawo. Kuyambira kwa anthu a ku Damasiko, kenako a ku Yerusalemu ndipo kenako m’dziko lonse la Yudeya ndi anthu a mitundu ina, ndinafikitsa uthenga wakuti alape n’kuyamba kulambira Mulungu pochita zinthu zosonyeza kulapa.” (Mac. 26:19, 20) Kwa zaka zambiri, Paulo anakhala akukwaniritsa ntchito imene anapatsidwa ndi Yesu Khristu m’masomphenya amene anaona dzuwa lili pamutu aja. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Ena mwa anthu amene anamvetsera uthenga wabwino umene Paulo ankalalikira, analapa n’kusiya zachiwerewere ndiponso zachinyengo ndipo anayamba kutumikira Mulungu. Anthu amenewo anakhala nzika zabwino ndipo ankamvera malamulo n’kumathandiza kuti m’dziko mukhale mtendere.

15 Koma Ayuda amene ankatsutsa Paulo analibe nazo ntchito zimenezi. Paulo ananena kuti: “N’chifukwa chake Ayuda anandigwira m’kachisi n’kumafuna kundipha. Komabe, popeza ndinaona Mulungu akundithandiza, ndikuchitirabe umboni kwa anthu otchuka ndiponso anthu wamba mpaka lero.”​—Mac. 26:21, 22.

16. Kodi tingatsanzire bwanji Paulo tikamafotokoza zimene timakhulupirira kwa oweruza komanso olamulira?

16 Akhristu oonafe, ‘nthawi zonse tizikhala okonzeka kuyankha’ zokhudza chikhulupiriro chathu. (1 Pet. 3:15) Tikamafotokoza zimene timakhulupirira kwa oweruza ndiponso olamulira, tingachite bwino kutsatira njira imene Paulo anagwiritsa ntchito polankhula ndi Agiripa komanso Fesito. N’kutheka kuti anthu audindo angafewetse mitima yawo ngati titawauza mwaulemu mmene choonadi cha m’Baibulo chatisinthira ifeyo komanso anthu amene amamvetsera uthenga wathu.

“Ukhoza Kundikopa Kuti Ndikhale Mkhristu” (Machitidwe 26:24–32)

17. Kodi Fesito ananena chiyani atamva zimene Paulo ankalankhula, ndipo anthu masiku ano amakhala ndi maganizo ati ofanana ndi a Fesito?

17 Olamulira awiriwo anakhudzidwa kwambiri atamvetsera umboni wosatsutsika wa Paulo. Tamvani zimene zinachitika: “Pamene Paulo ankanena zimenezi podziteteza, Fesito ananena mokweza mawu kuti: ‘Wachita misala iwe Paulo! Kuphunzira kwambiri kwakupengetsa!’” (Mac. 26:24) Zimene Fesito ananenazo zikusonyezanso mmene anthu ena amaganizira masiku ano. Anthu ambiri amaona kuti anthu amene amaphunzitsa zimene Baibulo limanena amaumirira mfundo za chipembedzo chawo. Nthawi zambiri anthu amene amaonedwa kuti ndi anzeru m’dzikoli savomereza mfundo ya m’Baibulo yakuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa.

18. Kodi Paulo anamuyankha bwanji Fesito, nanga Agiripa atamva yankho limeneli anati chiyani?

18 Koma Paulo anayankha bwanamkubwayo kuti: “Wolemekezeka a Fesito, inetu sindinachite misala, koma ndikulankhula mawu a choonadi ndipo ndili bwinobwino. Kunena zoona, ndikulankhula momasuka chifukwa mfumu imene ndikulankhula nayo ikudziwa bwino zimenezi . . . Kodi inuyo, Mfumu Agiripa, mumakhulupirira zimene aneneri analemba? Ndikudziwa kuti mumazikhulupirira.” Koma Agiripa anayankha kuti: “Pa nthawi yochepa ukhoza kundikopa kuti ndikhale Mkhristu.” (Mac. 26:25-28) Kaya Agiripa ananena mawu amenewa moona mtima kapena ayi, n’zoonekeratu kuti mfumuyi inakhudzidwa mtima ndi zimene Paulo ananena.

19. Kodi Fesito ndi Agiripa anadziwa kuti Paulo anali munthu wotani?

19 Kenako Agiripa ndi Fesito anaimirira posonyeza kuti msonkhanowo watha. “Koma pochoka anayamba kukambirana kuti: ‘Munthu uyu sanachite chilichonse choyenera kuphedwa kapena kumangidwa.’ Ndipo Agiripa anauza Fesito kuti: ‘Akanakhala kuti sanapemphe kukaonekera kwa Kaisara, munthu ameneyu akanamasulidwa.’” (Mac. 26:31, 32) Olamulirawa anadziwa kuti Paulo anali wosalakwa. Mwina zimenezi zinawathandiza kuti asamadanenso kwambiri ndi Akhristu.

20. Kodi panali zotsatira zotani Paulo atalalikira akuluakulu a boma?

20 Zikuoneka kuti olamulira amphamvu awiriwa sanakhale Akhristu ngakhale kuti Paulo anawalalikira. Ndiye kodi mtumwi Paulo anachita bwino kukaonekera kwa olamulirawa? Inde. Tikutero chifukwa zimene zinachitikira Paulo ‘pomupititsa kwa mafumu ndi abwanamkubwa’ ku Yudeya, zinathandiza kuti akuluakulu a boma la Roma amve uthenga wabwino. Zimenezi sizikanatheka pa nthawiyo Paulo akanapanda kukaonekera kwa olamulirawo. (Luka 21:12, 13) Ndipo zimene zinamuchitikirazo komanso kukhulupirika kwake pa nthawi ya mavuto zinalimbikitsa abale ndi alongo ake.​—Afil. 1:12-14.

21. Kodi chingachitike n’chiyani ngati tikupitiriza kulalikira za Ufumu pamene tikukumana ndi mayesero?

21 N’chimodzimodzinso masiku ano. Tikamapitiriza kugwira ntchito yolalikira za Ufumu ngakhale pamene tikukumana ndi mayesero komanso kutsutsidwa, pangakhale zotsatira zabwino. Mwachitsanzo, tingachitire umboni kwa akuluakulu a boma amene sizikanatheka kuwalalikira. Komanso tikamapirira mokhulupirika, tingalimbikitse Akhristu anzathu ndipo tingawathandize kukhala olimba mtima kwambiri pa ntchito yolalikira za Ufumu wa Mulungu.

a Onani bokosi lakuti “ Porikiyo Fesito Anali Bwanamkubwa wa Chiroma.”

b “Mpando woweruzira milandu” ankauika pamalo okwera. Zimenezi zinkasonyeza kuti palibe amene akanasintha zimene woweruza wagamula ndipo zinkayenera kulemekezedwa. Pilato anakhala pampando woweruzira milandu pamene ankamvetsera milandu imene Ayuda ankaneneza Yesu.

d Onani bokosi lakuti “ Mfumu Herode Agiripa Wachiwiri.”

e Paulo atakhala Mkhristu, ankavomereza kuti Yesu ndi Mesiya. Koma Ayuda amene sankavomereza zimenezi, ankaona kuti Paulo ndi wampatuko.​—Mac. 21:21, 27, 28.

f Polankhulapo pa mawu a Paulo akuti ankayenda “dzuwa lili pamutu,” katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Munthu amene anali pa ulendo ankafunikira kupuma nthawi ya masana chifukwa kunkatentha kwambiri. Koma ngati sanapume, zinkasonyeza kuti akufulumira kwambiri. Choncho apa tikuona kuti Paulo ankadzipereka kwambiri pa ntchito yozunza Akhristu.”