Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 28

“Mpaka Kumalekezero a Dziko Lapansi.”

“Mpaka Kumalekezero a Dziko Lapansi.”

A Mboni za Yehova akupitiriza ntchito imene otsatira a Yesu Khristu oyambirira ankagwira

1. Kodi Akhristu oyambirira akufanana bwanji ndi a Mboni za Yehova masiku ano?

 AKHRISTU oyambirira ankalalikira mwakhama ndipo ankalola ndi mtima wonse kuti mzimu woyera uziwathandiza ndiponso kuwatsogolera. Iwo anapitirizabe kulalikira ngakhale kuti ankazunzidwa ndipo Mulungu anawadalitsa kwambiri. Masiku anonso, a Mboni za Yehova amachita zimenezi ndipo Mulungu amawadalitsa kwambiri.

2, 3. Kodi n’chiyani kwenikweni chimene chimapangitsa kuti buku la Machitidwe likhale lochititsa chidwi kwambiri?

2 Mosakayikira, mwalimbikitsidwa kwambiri ndi nkhani zochititsa chidwi komanso zolimbitsa chikhulupiriro zopezeka m’buku la m’Baibulo la Machitidwe a Atumwi. Bukuli ndi lapadera kwambiri chifukwa ndi buku lokhali louziridwa ndi Mulungu limene limafotokoza mbiri ya Akhristu oyambirira.

3 Buku la Machitidwe limatchula anthu osiyanasiyana okwana 95 ochokera m’mayiko 32, mizinda 54 ndi zilumba 9. Limafotokozanso nkhani zochititsa chidwi kwambiri zokhudza anthu osiyanasiyana. Ena mwa anthu amenewa anali anthu wamba, achipembedzo odzitukumula, andale onyada ndipo ena ankazunza anzawo mwankhanza. Koma makamaka limafotokoza za abale ndi alongo anu a m’nthawi ya atumwi. Iwo ankakumana ndi mavuto amene anthu onse amakumana nawo tsiku ndi tsiku komanso ankalalikira uthenga wabwino mwakhama.

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti timafanana kwambiri ndi anthu ngati mtumwi Paulo, Tabita ndi mboni zina zokhulupirika zakale?

4 Tsopano papita zaka pafupifupi 2,000 kuchokera m’nthawi ya Akhristu oyambirira. Ena mwa Akhristu amenewa anali mtumwi Petulo ndi mtumwi Paulo, omwe ankagwira ntchito yawo mwakhama, Luka yemwe anali dokotala wokondedwa, Baranaba yemwe anali wopatsa manja, Sitefano yemwe anali wolimba mtima, Tabita yemwe anali wachifundo, Lidiya yemwe anali wochereza alendo ndi mboni zina zambiri zokhulupirika. Ngakhale kuti Akhristu amenewa anakhalapo kalekale, ifeyo timafanana nawo kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa ifenso tikugwira ntchito imene iwowo ankagwira, yothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. (Mat. 28:19, 20) Ndithudi, ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchito imeneyi.

“. . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Machitidwe 1:8

5. Kodi otsatira a Yesu anayambira kuti kugwira ntchito yawo yolalikira?

5 Taganizirani za ntchito imene Yesu anapereka kwa otsatira ake. Iye anawauza kuti: “Mukadzalandira mzimu woyera, mudzakhala ndi mphamvu. Ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Poyamba, mzimu woyera unathandiza ophunzirawo kuti akhale mboni “mu Yerusalemu.” (Mac. 1:1–8:3) Kenako, motsogoleredwa ndi mzimuwo, iwo analalikira “ku Yudeya konse ndi ku Samariya.” (Mac. 8:4–13:3) Kenako iwo anayamba kulalikira kumadera akutali ndipo uthenga wabwinowo unayamba kufika “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Mac. 13:4–28:31.

6, 7. Kodi ifeyo tili ndi zinthu ziti zogwiritsira ntchito polalikira zimene abale ndi alongo athu a m’nthawi ya atumwi analibe?

6 Abale ndi alongo athu a m’nthawi ya atumwi analibe Baibulo lonse lathunthu loti akanatha kumagwiritsira ntchito polalikira. Mwachitsanzo, kunalibe buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu mpaka cha m’ma 41 C.E. Ndipo makalata ena a Paulo analembedwa cha m’ma 61 C.E., buku la Machitidwe lisanathe kulembedwa. Akhristu oyambirira analibe Mabaibulo awoawo athunthu komanso mabuku osiyanasiyana oti akanatha kumapereka kwa anthu achidwi amene akumana nawo. Akhristu a Chiyuda asanakhale ophunzira a Yesu, ankamva Malemba a Chiheberi akuwerengedwa m’masunagoge. (2 Akor. 3:14-16) Komabe nawonso ankafunika kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama, chifukwa mwina ankafunika kuloweza malemba pamtima n’kumauza anthu ena polalikira.

7 Masiku ano, ambirife tili ndi Baibulo lathulathu komanso mabuku ambirimbiri othandiza pophunzira Baibulo. Tikuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu polengeza uthenga wabwino m’mayiko oposa 240, m’zilankhulo zosiyanasiyana.

Mzimu Woyera Unawapatsa Mphamvu

8, 9. (a) Kodi mzimu woyera unathandiza ophunzira a Yesu kuchita chiyani? (b) Kodi kapolo wokhulupirika akuchita zotani mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu?

8 Pamene Yesu ankauza ophunzira ake kuti azigwira ntchito yolalikira, anawauzanso kuti: “Mukadzalandira mzimu woyera, mudzakhala ndi mphamvu.” Motsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito, otsatira a Yesu akanakwanitsa kuchitira umboni padziko lonse lapansi. Mothandizidwa ndi mzimu woyera, Petulo ndi Paulo ankachiritsa anthu odwala, kutulutsa ziwanda ngakhalenso kuukitsa akufa. Koma cholinga chachikulu cha mphamvu ya mzimu woyera chinali choti iwathandize kugwira ntchito inayake yofunika kwambiri. Mzimu woyera unathandiza atumwi ndi ophunzira ena a Yesu kuti azitha kuphunzitsa molondola mawu a Mulungu, amene amathandiza anthu kuti adzapeze moyo wosatha.​—Yoh. 17:3.

9 Pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E., ophunzira a Yesu analankhula “zilankhulo zosiyanasiyana, mogwirizana ndi mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.” Zimenezi zinawathandiza kuti alalikire “zinthu zazikulu za Mulungu.” (Mac. 2:1-4, 11) Masiku ano sitilankhula zilankhulo zosiyanasiyana mozizwitsa. Komabe mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, kapolo wokhulupirika komanso wanzeru amatulutsa mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’zilankhulo zambiri. Mwachitsanzo, magazini mamiliyoni ambirimbiri a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, amasindikizidwa mwezi uliwonse ndipo pawebusaiti yathu ya jw.org, pamapezeka mabuku ndi mavidiyo othandiza pophunzira Baibulo m’zilankhulo zoposa 1,000. Zimenezi zimatithandiza kuti tizitha kulengeza “zinthu zazikulu za Mulungu” kwa anthu ochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse ndiponso olankhula chilankhulo chilichonse.​—Chiv. 7:9.

10. Kodi n’chiyani chachitika pa ntchito yomasulira Baibulo kuyambira mu 1989?

10 Kuyambira mu 1989, kapolo wokhulupirika anayamba kulimbikitsa kwambiri ntchito yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika n’cholinga choti lizipezeka m’zilankhulo zambiri. Baibuloli lamasuliridwa kale m’zilankhulo zoposa 200 komanso Mabaibulo ambirimbiri asindikizidwa kale ndipo ena ambiri akusindikizidwanso. Ndi Mulungu yekha komanso mzimu wake umene ukuthandiza kuti zimenezi zitheke.

11. Kodi ndi ndani amene amagwira ntchito yomasulira mabuku a Mboni za Yehova?

11 Ntchito yomasulira ikugwiridwa ndi Akhristu ambiri ongodzipereka m’mayiko oposa 150. Sitiyenera kudabwa ndi zimenezi chifukwa palibenso gulu lina padziko lapansi limene likutsogoleredwa ndi mzimu woyera ‘pochitira umboni mokwanira’ za Yehova Mulungu, za Mfumu imenenso ndi Mesiya ndiponso za Ufumu umene wakhazikitsidwa kumwamba.​—Mac. 28:23.

12. N’chiyani chinathandiza Paulo ndi Akhristu ena kuti akwanitse kugwira ntchito yolalikira?

12 Pamene Paulo ankalalikira Ayuda ndi anthu a mitundu ina ku Antiokeya wa ku Pisidiya, “onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira.” (Mac. 13:48) Luka anamaliza kulemba buku la Machitidwe ndi nkhani yokhudza Paulo yemwe ‘ankalalikira za Ufumu wa Mulungu . . . ndi ufulu wonse wa kulankhula popanda choletsa.’ (Mac. 28:31) Kodi mtumwiyu ankalalikira kuti? Ku Roma, mzinda umene unali likulu la ufumu wamphamvu kwambiri padziko lonse lapansi pa nthawiyo. Otsatira a Yesu oyambirira ankagwira ntchito yawo yolalikira mothandizidwa ndiponso motsogoleredwa ndi mzimu woyera. Mzimuwo unkawathandiza kuchitira umboni pokamba nkhani komanso pochita zinthu zina.

Anapitirizabe Kulalikira Ngakhale Kuti Ankazunzidwa

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera tikamazunzidwa?

13 Pamene ophunzira a Yesu oyambirira ankazunzidwa, anapempha Yehova kuti awathandize kukhala olimba mtima. Ndiye chinachitika n’chiyani? Anadzazidwa ndi mzimu woyera umene unawathandiza kuti azilankhula mawu a Mulungu molimba mtima. (Mac. 4:18-31) Ifenso timapemphera kwa Mulungu kuti atipatse nzeru ndi mphamvu kuti tipitirize kulalikira ngakhale pamene tikuzunzidwa. (Yak. 1:2-8) Timapitiriza kugwira ntchito yolalikira za Ufumu chifukwa Mulungu amatidalitsa komanso mzimu wake umatithandiza. Palibe chimene chingatiletse kugwira ntchito yolalikira, kaya ndi kutsutsidwa mwamphamvu kapena kuzunzidwa mwankhanza. Tikamazunzidwa, timafunikira kupemphera kuti Mulungu atipatse mzimu woyera, nzeru komanso kuti atithandize kukhala olimba mtima polengeza uthenga wabwino.​—Luka 11:13.

14, 15. (a) Kodi chinachitika n’chiyani chifukwa cha “mavuto amene anayamba chifukwa cha zimene zinachitikira Sitefano”? (b) M’nthawi yathu ino, kodi anthu ambiri ku Siberia anaphunzira bwanji choonadi?

14 Sitefano analalikira molimba mtima asanaphedwe ndi adani ake. (Mac. 6:5; 7:54-60) Akhristu atayamba “kuzunzidwa koopsa” ophunzira onse kupatulapo atumwi, anabalalikira m’zigawo zonse za Yudeya ndi Samariya. Koma zimenezi sizinaimitse ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, Filipo anapita ku Samariya “n’kuyamba kulalikira za Khristu” ndipo zotsatira zake zinali zabwino kwambiri. (Mac. 8:1-8, 14, 15, 25) Komanso Baibulo limatiuza kuti: “Anthu amene anabalalika chifukwa cha mavuto amene anayamba chifukwa cha zimene zinachitikira Sitefano, anakafika mpaka ku Foinike, ku Kupuro ndi ku Antiokeya. Ndipo ankangolalikira kwa Ayuda okha. Koma ena mwa anthuwa anali a ku Kupuro ndi ku Kurene. Iwowa atafika ku Antiokeya anayamba kulengeza uthenga wabwino wa Ambuye Yesu kwa anthu olankhula Chigiriki.” (Mac. 11:19, 20) Pa nthawiyo, kuzunzidwa kwa Akhristu kunachititsa kuti uthenga wa Ufumu ufalikire.

15 M’nthawi yathu ino, zinthu ngati zimenezi zinachitikanso m’mayiko amene kale ankadziwika kuti Soviet Union. Anthu ambirimbiri a Mboni za Yehova anawathamangitsira ku Siberia, makamaka m’zaka za m’ma 1950. Chifukwa cha kuthamangitsidwako, a Mboni za Yehova ambiri anakakhala kumadera akutali kwambiri ndi kwawo ndipo anamwazikana m’midzi yosiyanasiyana m’dziko lonselo. Zimenezi zinathandiza kuti uthenga wabwino ufalikire m’dziko la Siberia, lomwe ndi lalikulu kwambiri. Choncho a Mboni za Yehova ambiri anakwanitsa kulalikira uthenga wabwino kumadera akutali kwambiri, mpaka mtunda wokwana makilomita 10,000 kuchokera kwawo. Iwo sakanakwanitsa kupeza ndalama zokafikira kumadera amenewa kuti akalalikire. Koma izi zinatheka chifukwa boma linawatumiza lokha kumeneko. M’bale wina anati: “Zimene akuluakulu a boma anachitazi zinathandiza kuti anthu ambirimbiri oona mtima a ku Siberia adziwe choonadi.”

Yehova Anawadalitsa Kwambiri

16, 17. Kodi buku la Machitidwe limasonyeza bwanji kuti Yehova ankadalitsa ntchito yolalikira?

16 N’zochita kuonekeratu kuti Yehova anadalitsa Akhristu oyambirira. Paulo ndi Akhristu ena anadzala komanso kuthirira, “koma Mulungu ndi amene anakulitsa.” (1 Akor. 3:5, 6) Nkhani za m’buku la Machitidwe zikusonyeza mmene ntchito yolalikira inakulira chifukwa chakuti Yehova ankaidalitsa. Mwachitsanzo, “mawu a Mulungu anapitiriza kufalikira. Chiwerengero cha ophunzira chinkawonjezeka kwambiri mu Yerusalemu.” (Mac. 6:7) Pamene ntchito yolalikira inkakula, “mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unayamba kukhala pamtendere ndipo unali wolimba. Chifukwa choti ophunzira ankaopa Yehova komanso ankalimbikitsidwa ndi mzimu woyera, mpingowo unkakulirakulira.”​—Mac. 9:31.

17 Ku Antiokeya wa ku Siriya, Ayuda ndi anthu olankhula Chigiriki anaphunzira choonadi kwa mboni zolimba mtima. Baibulo limati, “dzanja la Yehova linkawathandiza ndipo anthu ambiri anakhulupirira n’kuyamba kutsatira Ambuye.” (Mac. 11:21) Pofotokoza momwe ntchito inakulira mumzinda umenewo, nkhaniyi imati: “Mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndipo anthu ambiri anakhala okhulupirira.” (Mac. 12:24) Ndipo chifukwa chakuti Paulo ndi anthu ena analalikira mokwanira pakati pa anthu a mitundu ina, “mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndipo sankagonjetseka.”​—Mac. 19:20.

18, 19. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti “dzanja la Yehova” lili nafe? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova amathandiza anthu ake.

18 N’zosachita kufunsa kuti “dzanja la Yehova” lilinso ndi ife masiku ano. N’chifukwa chake anthu ambiri akuphunzira choonadi ndipo akubatizidwa posonyeza kuti anadzipereka kwa Mulungu. Ndipo chifukwa chakuti Mulungu akutithandiza komanso kutidalitsa, timatha kupitirizabe kugwira ntchito yathu yolalikira ngakhale pamene tikutsutsidwa kwambiri kapena kuzunzidwa mwankhanza, ngati mmene Paulo ndi Akhristu ena oyambirira ankachitira. (Mac. 14:19-21) Yehova Mulungu amakhala nafe nthawi zonse. ‘Manja ake omwe adzakhalapo mpaka kalekale,’ sadzalephera kutithandiza tikamakumana ndi mayesero alionse. (Deut. 33:27) Tizikumbukiranso kuti chifukwa cha dzina lake lalikulu, Yehova sataya anthu ake.​—1 Sam. 12:22; Sal. 94:14.

19 Mwachitsanzo, popeza M’bale Harald Abt sanasiye kulalikira, akuluakulu a chipani cha Nazi anamutumiza kundende yozunzirako anthu ya Sachsenhausen pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. M’mwezi wa May m’chaka cha 1942, apolisi a Gestapo anapita kunyumba kwa Elsa, mkazi wa m’baleyu, kukamumanga ndipo anamulanda mwana wawo wamkazi wamng’ono. Elsa anatumizidwa kundende zosiyanasiyana zozunzirako anthu. Kenako Mlongo Abt anafotokoza kuti: “Pa zaka zimene ndinakhala m’ndende zozunzirako anthu ku Germany, ndinaphunzira kanthu kenakake kapadera kwambiri. Ndinaphunzira kuti mzimu wa Yehova umatha kulimbikitsa munthu kwambiri pamene ali pa mayesero oopsa. Ndisanamangidwe, ndinawerenga kalata imene mlongo winawake analemba, imene inanena kuti munthu akakhala pa mayesero oopsa, mzimu wa Yehova umamuthandiza kuti asachite mantha. Ndinkaganiza kuti mlongoyu akungokokomeza. Koma ineyo nditakumana ndi mayesero, ndinazindikira kuti zimene ankanenazo zinali zoona ndipo ndi mmenedi zimakhalira. Ngati munthu sunakumanepo nazo, n’zovuta kuti uzikhulupirire. Koma n’zimene zinandichitikira ineyo.”

Pitirizani Kuchitira Umboni Mokwanira

20. Kodi Paulo ankachita chiyani pamene anali mkaidi wosachoka panyumba, nanga zimenezi zingalimbikitse bwanji abale ndi alongo athu ena?

20 Nkhani ya m’buku la Machitidwe inathera poti Paulo ‘ankalalikira za Ufumu wa Mulungu’ mwakhama. (Mac. 28:31) Popeza Paulo anali mkaidi wosachoka panyumba, analibe mwayi woti akanatha kumalalikira kunyumba ndi nyumba ku Roma. Ngakhale zinali choncho, iye anapitiriza kulalikira kwa anthu onse amene ankabwera kwa iye. Masiku ano, chifukwa cha ukalamba kapena matenda, abale ndi alongo athu ena sangathe kuchoka panyumba, ndipo ena sangathe kudzuka pabedi, pamene ena akukhala m’nyumba zosungirako anthu odwala ndi okalamba. Koma abale ndi alongo amenewa amakondabe Mulungu ndiponso kulalikira. Choncho timawapempherera kuti Atate wathu wakumwamba awathandize kukumana ndi anthu amene akulakalaka kuphunzira za iye ndiponso kudziwa zinthu zosangalatsa kwambiri zimene Mulungu adzachite m’tsogolomu.

21. N’chifukwa chiyani tiyenera kulalikira mwachangu?

21 Koma ambiri a ife tikhoza kukwanitsa kulalikira kunyumba ndi nyumba ndiponso m’njira zina zosiyanasiyana pa ntchito yathu yothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Choncho tiyeni tonsefe tiyesetse kuchita zonse zimene tingathe kuti tikwanitse udindo wathu wolalikira za Ufumu ndi kuchitira umboni “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” Tiyenera kugwira ntchito imeneyi mwachangu, ndipo tiyenera kugwiritsira ntchito bwino nthawi yathu chifukwa “chizindikiro” cha kukhalapo kwa Khristu tsopano chikuonekera bwino kwambiri. (Mat. 24:3-14) Panopa, tili ndi “zochita zambiri pa ntchito ya Ambuye.”​—1 Akor. 15:58.

22. Kodi tiyenera kupitiriza kuchita chiyani pamene tikudikira tsiku la Yehova?

22 Pamene tikudikira kufika kwa “tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova,” tiyeni tipitirize kuchitira umboni molimba mtima ndiponso mokhulupirika. (Yow. 2:31) Tipitirizabe kupeza anthu ambiri ofanana ndi anthu a ku Bereya, amene “analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri.” (Mac. 17:10, 11) Choncho tiyeni tipitirize kuchitira umboni mpaka pamapeto ndipo Yehova adzasangalala nafe kwambiri, moti adzakhala ngati akutiuza kuti: “Wachita bwino kwambiri, ndiwe kapolo wabwino komanso wokhulupirika!” (Mat. 25:23) Tikamagwira mwakhama ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu ndiponso tikapitiriza kukhala okhulupirika kwa Yehova, tidzasangalala kwamuyaya kuti tinagwira nawo ntchito ‘yochitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu.’