Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 24

“Limba Mtima”

“Limba Mtima”

Paulo anapulumuka chiwembu chofuna kumupha komanso analankhula mawu odziteteza pamaso pa Felike

Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 23:11–24:27

1, 2. N’chifukwa chiyani Paulo sanadabwe pamene ankazunzidwa ku Yerusalemu?

 ASILIKALI anapulumutsa Paulo m’manja mwa gulu la anthu achiwawa ku Yerusalemu, ndipo kenako anamutsekeranso m’ndende. Mtumwi wakhamayu sanadabwe kuona kuti ankazunzidwa ku Yerusalemu chifukwa anali atauzidwa kale kuti akuyembekezera “kumangidwa komanso kuzunzidwa” mumzindawu. (Mac. 20:22, 23) Ngakhale kuti sankadziwa zonse zimene zingamuchitikire, Paulo ankadziwa bwino kuti apitiriza kuvutika chifukwa cha dzina la Yesu.​—Mac. 9:16.

2 Aneneri omwe anali Akhristu anali atamuchenjeza kale kuti adzamangidwa “n’kumupereka kwa anthu a mitundu ina.” (Mac. 21:4, 10, 11) M’mbuyomo, gulu la Ayuda linkafuna kumupha kenako, zinaoneka ngati oweruza a m’Khoti Lalikulu la Ayuda “amukhadzulakhadzula” pamene ankatsutsana okhaokha chifukwa cha zimene iye analankhula. Tsopano mtumwiyu anali atamangidwa ndi asilikali a Chiroma ndipo ankamuimba milandu yosiyanasiyana. (Mac. 21:31; 23:10) Apatu n’zoonekeratu kuti iye ankafunika kulimbikitsidwa.

3. Kodi timalimbikitsidwa bwanji kuti tipitirize ntchito yathu yolalikira?

3 Mu nthawi ya mapeto ino, tikudziwa kuti “onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Tim. 3:12) Nthawi zonse ifenso timafunika kulimbikitsidwa kuti tipitirize ntchito yathu yolalikira. Timayamikira kwambiri tikamva mawu olimbikitsa a pa nthawi yake kuchokera m’mabuku athu ndiponso misonkhano imene “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” amatikonzera. (Mat. 24:45) Yehova akutitsimikizira kuti adani a uthenga wabwino sadzapambana. Iwo sangawononge gulu la atumiki ake kapena kuletsa ntchito yawo yolalikira. (Yes. 54:17; Yer. 1:19) Ndiye kodi n’chiyani chinachitikira mtumwi Paulo? Kodi analimbikitsidwa kuti apitirize kuchitira umboni mokwanira ngakhale kuti anthu ankamutsutsa? Ngati ndi choncho, analimbikitsidwa bwanji ndipo iye anatani atalimbikitsidwa?

‘Chiwembu Chochita Kulumbirira’ Chinalephereka (Machitidwe 23:11-34)

4, 5. Kodi Paulo analimbikitsidwa bwanji, ndipo n’chifukwa chiyani tinganene kuti zimenezi zinachitika pa nthawi yabwino?

4 Mtumwi Paulo analimbikitsidwa kwambiri usiku wa tsiku limene anapulumutsidwa m’Khoti Lalikulu la Ayuda. Nkhani youziridwayi imati: “Ambuye anaima pafupi ndi Paulo n’kumuuza kuti: ‘Limba mtima. Chifukwa wandichitira umboni mokwanira ku Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.’” (Mac. 23:11) Mawu olimbikitsa amene Yesu analankhulawa, anatsimikizira Paulo kuti saphedwa. Iye anadziwa kuti apita ku Roma ndipo kumeneko akakhala ndi mwayi wochitira umboni za Yesu.

“Amuna oposa 40 akufuna kudzamudikirira panjira.”​—Machitidwe 23:21

5 Mawu olimbikitsa amene Paulo anauzidwa anali a pa nthawi yake. Tikutero chifukwa tsiku lotsatira, Ayuda oposa 40 “anakonza chiwembu n’kulumbira pochita kudzitemberera kuti saadya kapena kumwa chilichonse mpaka atapha Paulo.” Mfundo yakuti Ayudawo anakonza ‘chiwembu chochita kulumbirira’ ikusonyeza kuti anatsimikiza ndi mtima wonse kuti aphe mtumwiyu. Iwo ankakhulupirira kuti zimene anakonzazo zikalephereka, ndiye kuti akhala otembereredwa kapena chinachake choipa chiwachitikira. (Mac. 23:12-15) Chiwembu chawocho, chimene chinavomerezedwa ndi ansembe aakulu komanso akulu, chinali choti Paulo apitenso ku Khoti Lalikulu la Ayuda kuti akapitirize kumufunsa ngati kuti akufuna kumvetsa bwino nkhani yake. Koma achiwembuwo anakonza zoti amudikirire panjira n’kumupha.

6. Kodi chiwembu chofuna kupha Paulo chinadziwika bwanji, nanga achinyamata masiku ano angaphunzire chiyani pa nkhaniyi?

6 Koma mwana wa mchemwali wake wa Paulo anamva za chiwembuchi ndipo anakauza Paulo. Kenako Paulo anauza mnyamatayo kuti akauze Kalaudiyo Lusiya, mkulu wa asilikali, za nkhaniyi. (Mac. 23:16-22) N’zoonekeratu kuti Yehova amakonda achinyamata ngati mwana wa mchemwali wake wa Pauloyu, yemwe sanatchulidwe dzina. Achinyamata amenewa amathandiza atumiki ake molimba mtima ndiponso amachita mokhulupirika zonse zomwe angathe kuti athandize pa ntchito ya Ufumu.

7, 8. Kodi Kalaudiyo Lusiya anatani kuti ateteze Paulo?

7 Kalaudiyo Lusiya, amene ankatsogolera asilikali 1,000, atamva za chiwembuchi nthawi yomweyo analamula asilikali okwana 470 kuti achoke ku Yerusalemu usiku womwewo n’kuperekeza Paulo ku Kaisareya. Pagululi panali asilikali oyenda pansi, a mikondo ndiponso okwera mahatchi. Iye anawauza kuti akakafika kumeneko, akapereke Paulo kwa Bwanamkubwa Felike. a Ngakhale kuti mzinda wa Kaisareya unali likulu la Yudeya ndipo chigawochi chinkalamulidwa ndi Aroma, anthu ambiri amene ankakhala mumzindawu sanali Ayuda. Anthu ankakhala mwabata mumzindawu poyerekezera ndi ku Yerusalemu, kumene anthu ambiri ankachita zinthu zachiwawa chifukwa chodana ndi zipembedzo zina. Ku Kaisareya kunalinso likulu la asilikali a Aroma amene ankakhala ku Yudeya.

8 Potsatira malamulo a Aroma, Lusiya anatumiza kalata kwa Felike yofotokoza za mlandu wa Paulo. Iye anafotokoza kuti atadziwa kuti Paulo anali nzika ya Roma, anamulanditsa kwa Ayuda amene “anatsala pang’ono kumupha.” Anafotokozanso kuti Paulo sanapezeke ndi mlandu uliwonse “woyenera kuphedwa kapena kutsekeredwa m’ndende.” Koma popeza kuti Ayuda anamukonzera chiwembu, Lusiya ananena kuti akumupereka kwa Bwanamkubwa Felike kuti amvetsere mlandu wake n’kumuweruza.​—Mac. 23:25-30.

9. (a) Kodi ufulu wa Paulo, yemwe anali nzika ya Roma, unaphwanyidwa bwanji? (b) N’chifukwa chiyani nthawi zina tingagwiritse ntchito ufulu wathu ngati nzika za m’dziko limene tikukhala?

9 Kodi zonse zimene Lusiya analembazi zinali zoona? Ayi. Zikuoneka kuti iye ankafuna kuti bwanamkubwayo amuone ngati munthu wabwino. Si zoona kuti iye analanditsa Paulo chifukwa choti anadziwa kuti mtumwiyu ndi nzika ya Roma. Komanso Lusiya sanafotokoze zoti analamula kuti [Paulo] “amumange ndi maunyolo awiri” ndiponso kuti ‘amufunse mafunso kwinaku akum’kwapula.’ (Mac. 21:30-34; 22:24-29) Polamula zimenezi, Lusiya anaphwanya ufulu wa Paulo chifukwa anali nzika ya Roma. Masiku ano Satana amagwiritsa ntchito anthu okonda kwambiri chipembedzo chawo kuti azitsutsa komanso kuzunza Akhristu oona, ndipo nthawi zina amawaphwanyira ufulu wolambira Mulungu. Koma mofanana ndi Paulo, anthu a Mulungu angagwiritse ntchito malamulo a dziko lawo ndiponso ufulu wawo ngati nzika podziteteza.

“Ndine Wosangalala Kulankhula Podziteteza pa Zimene Akundinenerazi” (Machitidwe 23:35–24:21)

10. Kodi Paulo ananamiziridwa milandu yoopsa iti?

10 Ku Kaisareya, Paulo ‘ankamusunga m’nyumba ya Mfumu Herode n’kumamulondera’ podikira kuti anthu amene ankamuimba mlandu afike kuchokera ku Yerusalemu. (Mac. 23:35) Patatha masiku 5, kunafika Mkulu wa Ansembe Hananiya, munthu wina wodziwa kulankhula dzina lake Teritulo komanso akulu ena. Teritulo anayamba n’kuyamikira Felike chifukwa cha zimene ankachitira Ayuda, mwina pofuna kumukopa kuti awakondere pa mlanduwo. b Kenako polankhula za mlandu wa Paulo, Teritulo ananena kuti: “Munthu uyu ndi wovutitsa kwabasi, ndipo akuyambitsa zoukira boma pakati pa Ayuda padziko lonse. Ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lampatuko la anthu a ku Nazareti. Komanso iyeyu ankafuna kudetsa kachisi ndipo tinamugwira.” Ayuda ena “analowerera ndipo ankanena motsimikiza kuti zimenezo n’zoona.” (Mac. 24:5, 6, 9) Kuyambitsa kuukira boma, kutsogolera gulu loopsa lampatuko ndiponso kudetsa kachisi inali milandu yoopsa kwambiri ndipo anthu opalamula milandu imeneyi ankatha kuphedwa.

11, 12. Kodi Paulo ananena chiyani pokana milandu imene ankamunamizira?

11 Kenako Paulo analoledwa kuti alankhule. Iye anayamba ndi mawu akuti: “Ndine wosangalala kulankhula podziteteza pa zimene akundinenerazi.” Paulo anakanitsitsa milandu yonse imene ankamunamizirayo. Mtumwiyu sanadetse kachisi kapenanso kuyambitsa kuti anthu aukire boma. Ananena kuti kwa “zaka zambiri” sanali ku Yerusalemu ndipo pa nthawiyi anabwera kudzapereka “mphatso zachifundo” kwa Akhristu amene ankavutika chifukwa cha njala komanso kuzunzidwa. Paulo ananena kuti asanalowe m’kachisi ‘anadziyeretsa motsatira mwambo.’ Ananenanso kuti anayesetsa mwakhama ‘kuti akhale ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu ndiponso kwa anthu.’​—Mac. 24:10-13, 16-18.

12 Koma Paulo anavomereza kuti ankatumikira Mulungu wa makolo ake potsatira ‘njira yolambirira imene iwo ankaitchula kuti “gulu lampatuko.”’ Komabe ananena kuti ankakhulupirira “zonse zimene zili m’Chilamulo ndi zimene aneneri analemba.” Ndipo mofanana ndi anthu omwe ankamutsutsawo, iye anali ndi chiyembekezo chakuti “Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe.” Kenako Paulo anauza anthuwo kuti apereke umboni wa zimene ankamunenezazo. Iye anati: “Muwalole anthu ali panowa, afotokoze okha ngati anandipeza ndi mlandu uliwonse pamene ndinaima pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. Mawu amodzi okha amene ine ndinanena, pamene ndinaima pakati pawo ndi akuti, ‘Ine lero ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo chakuti akufa adzauka!’”​—Mac. 24:14, 15, 20, 21.

13-15. N’chifukwa chiyani tiyenera kutengera chitsanzo cha Paulo amene anachitira umboni molimba mtima pamaso pa olamulira?

13 Paulo anatipatsa chitsanzo chabwino cha zimene tiyenera kuchita ngati anthu atatitengera kwa akuluakulu a boma kapena oweruza chifukwa cha chikhulupiriro chathu, n’kutinamizira milandu yoyambitsa chisokonezo, kuukira boma kapena kutinena kuti tili “m’gulu loopsa lampatuko.” Paulo sanalankhule mawu okopa bwanamkubwayo kuti amukonde ngati mmene Teritulo anachitira. Iye ankalankhula modekha komanso mwaulemu. Ankalankhulanso mwaluso ndipo ankafotokoza mfundo zoona komanso zomveka bwino. Paulo ananenanso kuti pa mlanduwu panalibe “Ayuda ena ochokera m’chigawo cha Asia” amene ankamunamizira kuti anadetsa kachisi ndipo mogwirizana ndi malamulo, iwo anayenera kubwera kudzafotokoza zimene ankamunenezazo.​—Mac 24:18, 19.

14 Kuwonjezera pamenepo, Paulo sanasiye kunena za chikhulupiriro chake. Molimba mtima, mtumwiyu ananenanso za chikhulupiriro chake chakuti akufa adzauka, ngakhale kuti nkhani imeneyi ndi imene inayambitsa chisokonezo m’Khoti Lalikulu la Ayuda. (Mac. 23:6-10) Podziteteza, Paulo anatsindika za chiyembekezo chakuti akufa adzauka. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa chakuti iye ankachitira umboni za Yesu ndiponso zakuti anaukitsidwa. Koma anthu otsutsawo sakanavomereza zimenezi. (Mac. 26:6-8, 22, 23) Apatu nkhani yaikulu inagona pa kukhulupirira zoti akufa adzauka, makamaka kukhulupirira Yesu ndiponso kuti iye anaukitsidwa.

15 Mofanana ndi Paulo, tingamachitire umboni molimba mtima tikaganizira mawu amene Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa. Koma amene adzapirire mpaka mapeto ndi amene adzapulumuke.” Kodi tiyenera kuda nkhawa kuti tikanena chiyani anthu akamatiimba mlandu? Ayi, chifukwa Yesu anatitsimikizira kuti: “Pamene akupita nanu kukakuperekani, musafulumire kuda nkhawa kuti mukanena chiyani. Zimene mukapatsidwe mu ola lomwelo, mukanene zomwezo chifukwa wolankhula si inu, koma mzimu woyera.”​—Maliko 13:9-13.

“Felike Anachita Mantha” (Machitidwe 24:22-27)

16, 17. (a) Kodi Felike analankhula komanso kuchita chiyani pa mlandu wa Paulo? (b) N’chifukwa chiyani Felike anachita mantha, nanga n’chifukwa chiyani anapitiriza kuonana ndi Paulo?

16 Aka sikanali koyamba kuti Bwanamkubwa Felike amve zokhudza zimene Akhristu amakhulupirira. Baibulo limati: “Popeza Felike ankadziwa bwino nkhani yokhudza Njira imeneyi, [mawu amene ankagwiritsidwa ntchito ponena za Chikhristu choyambirira] anaimitsa mlanduwo n’kunena kuti: ‘Ndidzagamula mlandu wanuwu akadzafika Lusiya mkulu wa asilikali.’ Iye analamula mtsogoleri wa asilikali kuti amusunge m’ndende, koma amupatseko ufulu ndipo azilola anthu a mtundu wake kudzamuthandiza.”​—Mac. 24:22, 23.

17 Patapita masiku angapo, Felike ndi mkazi wake Durusila amene anali Myuda, anaitanitsa Paulo “n’kumamvetsera pamene ankafotokoza za kukhulupirira Khristu Yesu.” (Mac. 24:24) Koma pamene Paulo ankafotokoza za “chilungamo, kudziletsa ndiponso chiweruzo chimene chikubwera, Felike anachita mantha.” Mwina iye anachita mantha chifukwa anayamba kuvutika ndi chikumbumtima chifukwa cha zoipa zimene ankachita. Choncho anauza Paulo kuti: “Basi pita kaye, ndikadzapeza nthawi ndidzakuitananso.” Zitachitika zimenezi, Felike anakumanadi ndi Paulo kambirimbiri, osati chifukwa chofuna kuphunzira choonadi, koma ankaganiza kuti Paulo angamupatse chiphuphu.​—Mac. 24:25, 26.

18. N’chifukwa chiyani Paulo anauza Felike ndi mkazi wake za “chilungamo, kudziletsa ndiponso chiweruzo chimene chikubwera”?

18 N’chifukwa chiyani Paulo anauza Felike ndi mkazi wake za “chilungamo, kudziletsa ndiponso chiweruzo chimene chikubwera”? Kumbukirani kuti iwo ankafuna kudziwa zimene munthu ‘wokhulupirira Khristu Yesu’ ayenera kuchita. Paulo ankadziwa bwino kuti Felike ndi mkazi wake anali ankhanza, opanda chilungamo komanso okonda chiwerewere. Choncho ankawauza momveka bwino zimene munthu aliyense amene akufuna kukhala wotsatira wa Yesu ayenera kuchita. Zimene Paulo ananenazo zinasonyeza kusiyana kwa mfundo zolungama za Mulungu ndi zimene Felike ndi mkazi wake ankachita. Zimene iye anawauzazo zikanawathandiza kudziwa kuti anthu onse adzayankha mlandu kwa Mulungu chifukwa cha zimene amaganiza, kunena ndiponso kuchita. Komanso akanaona kuti anafunika kuganizira kwambiri za chiweruzo chachikulu chimene Mulungu adzawapatse, osati za chiweruzo chimene iwo akanapereka kwa Paulo. Choncho n’zosadabwitsa kuti Felike “anachita mantha.”

19, 20. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati anthu amene tikuwalalikira akuoneka ngati ali ndi chidwi ndi uthenga wathu, koma sakufuna kuti asinthe moyo wawo? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti Felike sanali mnzake wa Paulo?

19 Pamene tikugwira ntchito yolalikira, tingapeze anthu amene ali ngati Felike. Poyamba iwo angaoneke ngati akufuna kudziwa choonadi, koma safuna kumvera Mulungu n’kusintha moyo wawo. Tiyenera kukhala osamala pothandiza anthu ngati amenewa. Komabe mofanana ndi Paulo, tingawauze mwaulemu zimene ayenera kuchita kuti asangalatse Mulungu. Mwina choonadi chikhoza kuwathandiza kusintha khalidwe lawo. Koma tikaona kuti sakufuna kusiya zoipa zimene amachita, timawasiya n’kupita kukafufuza anthu amene akufunadi kudziwa choonadi.

20 Pa nkhani ya Felike, zolinga zake zenizeni zinadziwika chifukwa Baibulo limati: “Patatha zaka ziwiri, Felike analowedwa m’malo ndi Porikiyo Fesito. Koma popeza Felike ankafuna kuti Ayuda azimukonda, anangomusiya Paulo m’ndende.” (Mac. 24:27) Apa n’zoonekeratu kuti Felike sanali mnzake wa Paulo. Iye ankadziwa kuti anthu otsatira “Njira ya Ambuye” sanali oukira boma kapena oyesa kusintha malamulo a boma. (Mac. 19:23) Ankadziwanso kuti Paulo sanaphwanye lamulo lililonse la Aroma. Koma Felike anasungabe mtumwiyu m’ndende pofuna kuti “Ayuda azimukonda.”

21. Kodi n’chiyani chinachitikira Paulo, Porikiyo Fesito atakhala bwanamkubwa, nanga sitikukayikira kuti n’chiyani chinamuthandiza kuti akhalebe wolimba?

21 Mogwirizana ndi zimene taona pavesi lomaliza la Machitidwe chaputala 24, Paulo anali adakali m’ndende pamene Porikiyo Fesito anakhala bwanamkubwa m’malo mwa Felike. Choncho Paulo anayamba kuonekera kwa olamulira osiyanasiyana kuti iwo amve mlandu umene Ayuda ankamuneneza. Apatu mtumwi wolimba mtimayu ‘anamupititsa kwa mafumu ndi abwanamkubwa.’ (Luka 21:12) Kutsogoloku tiona kuti iye anachitiranso umboni pamaso pa wolamulira amene anali wamphamvu kwambiri pa nthawiyo. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto onsewa, Paulo anakhalabe ndi chikhulupiriro cholimba. Sitikukayikira kuti iye anakhalabe wolimba chifukwa ankakumbukira mawu a Yesu akuti: “Limba mtima.”

a Onani bokosi lakuti “ Felike Anali Bwanamkubwa wa Yudeya.”

b Teritulo anayamikira Felike kuti anabweretsa “mtendere wambiri” m’dziko lawo. Koma zoona zake zinali zakuti pa nthawi imene Felike anali bwanamkubwa, ku Yudeya kunalibe mtendere poyerekezera ndi nthawi imene abwanamkubwa ena ankalamulira derali. Ndipo mtendere unapitirizabe kusokonekera mpaka pamene Ayuda anagalukira boma la Roma. Komanso iye ananama kwambiri ponena kuti Ayuda ‘ankayamikira kwambiri’ Felike chifukwa anasintha zinthu. Zoona zake zinali zakuti Ayuda ambiri ankadana naye chifukwa chowapondereza komanso chifukwa chopha mwankhanza Ayuda amene anaukira boma.​—Mac. 24:2, 3.