Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 26

“Palibe Amene Ataye Moyo Wake”

“Palibe Amene Ataye Moyo Wake”

Ngalawa imene Paulo anakwera itasweka, iye anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba komanso ankakonda anthu

Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 27:1–28:10

1, 2. Kodi Paulo ankayembekezera kuyenda ulendo wotani, ndipo mwina ndi zinthu ziti zomwe zinkamudetsa nkhawa?

 PAULO ankaganizirabe mawu amene Bwanamkubwa Fesito ananena akuti, “udzapitadi kwa Kaisara,” chifukwa ankadziwa kuti mawuwa akukhudza zimene zingamuchitikire m’tsogolo. Iye anakhala zaka ziwiri m’ndende, choncho mwina ankaona kuti ulendo wake wautali wopita ku Roma ukanam’patsa mpata woona zinthu zina. (Mac. 25:12) Koma maulendo ambiri amene Paulo anayenda panyanja anali ochititsa mantha, osati osangalatsa, omaona malo okongola n’kumapitidwa kamphepo kayaziyazi. N’kuthekanso kuti Paulo akaganiza za ulendo wokaonana ndi Kaisara, panali zinthu zina zimene zinkamudetsa nkhawa.

2 Paulo anakumanapo ndi ‘zoopsa panyanja’ maulendo ambiri. Katatu konse ngalawa inawaswekera ndipo anakhalapo panyanja masana onse komanso usiku wonse. (2 Akor. 11:25, 26) Kuwonjezera pamenepo, ulendo uwu unali wosiyana kwambiri ndi maulendo amene anayenda pa ntchito yake yaumishonale asanamangidwe. Pa ulendowu, Paulo anali mkaidi komanso ulendo wake unali wautali kwambiri, wa makilomita oposa 3,000 kuchokera ku Kaisareya mpaka ku Roma. Kodi iye akanatha kuyenda ulendo woterewu osakumana ndi mavuto alionse? Ndipo ngakhale akanapanda kukumana ndi vuto lililonse, kodi ku Roma sakanaweruzidwa kuti aphedwe? Pajatu Paulo ankayembekezera kukaweruzidwa ndi wolamulira yemwe anali wamphamvu kwambiri pa nthawiyo m’dziko la Satanali.

3. Kodi Paulo ankafunitsitsa kuchita chiyani, nanga tikambirana chiyani m’mutuwu?

3 Popeza mwawerenga zinthu zambiri zokhudza Paulo pofika pano, kodi mukuganiza kuti iye analibe chiyembekezo ndiponso ankada nkhawa ndi zimene zikanamuchitikira? Ayi. Iye ankadziwa kuti akumana ndi mavuto, koma sankadziwa kuti akhala otani. Choncho ankaona kuti si bwino kuti asiye kusangalala ndi utumiki wake chifukwa choda nkhawa ndi zinthu zimene sangathe kuzisintha. (Mat. 6:27, 34) Paulo ankadziwa kuti cholinga cha Yehova chinali chakuti mtumwiyu agwiritse ntchito mpata uliwonse polalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ngakhale kwa akuluakulu a boma. (Mac. 9:15) Paulo ankafunitsitsa kukwaniritsa ntchito yakeyi, zivute zitani. Kodi nafenso cholinga chathu si chomwechi? Tsopano tiyeni timutsatire pa ulendo wofunikawu, ndipo tione mmene chitsanzo chake chingatithandizire.

‘Mphepo Inkawomba Kuchokera Kutsogolo Kwathu’ (Machitidwe 27:1-7a)

4. Kodi Paulo anakwera ngalawa yotani, ndipo ndi ndani anamuperekeza pa ulendowu?

4 Paulo ndi akaidi ena anaperekedwa m’manja mwa msilikali wina wa Chiroma, dzina lake Yuliyo, kuti aziwayang’anira. Msilikaliyo anaganiza zokwera ngalawa yonyamula katundu imene inafika ku Kaisareya. Ngalawayi inkachokera kudoko la Adiramutiyo limene linali m’dera la m’mbali mwa nyanja kumadzulo kwa Asia Minor. Dokoli linali moyang’anizana ndi mzinda wa Mitilene womwe unali pachilumba cha Lesbos. Ngalawayi inkalowera chakumpoto ndipo kenako inkakhotera chakumadzulo. Pa ulendowu inkaima n’kumatsitsa ndi kukweza katundu. Ngalawa zoterezi sankazipanga kuti muzikwera anthu, makamakanso akaidi. (Onani bokosi lakuti, “ Maulendo Apanyanja Komanso Njira za Amalonda.”) Mwamwayi, si Paulo yekha amene anali Mkhristu m’ngalawamo, momwe munali zigawenga zambiri. Panalinso Akhristu anzake ena awiri amene anamuperekeza omwe ndi Arisitako ndi Luka. Ndipotu Luka ndi amene analemba nkhaniyi. Sitikudziwa ngati Arisitako ndi Luka analipira okha ulendowo, kapena ngati anangokwera nawo ngati atumiki a Paulo.​—Mac. 27:1, 2.

5. Kodi Paulo anakumana ndi ndani ku Sidoni, ndipo tikuphunzirapo chiyani?

5 Atayenda kwa tsiku limodzi panyanja pamtunda wa makilomita pafupifupi 110 kulowera kumpoto, ngalawayo inaima ku Sidoni, gombe la ku Siriya. Zikuoneka kuti Yuliyo sankaona Paulo ngati mkaidi wamba, mwina chifukwa choti anali nzika ya Roma ndipo anali asanam’peze ndi mlandu uliwonse. (Mac. 22:27, 28; 26:31, 32) Choncho Yuliyo analola kuti Paulo apite kumtunda kukaona Akhristu anzake. Abale ndi alongo ayenera kuti anasangalala kwambiri kusamalira mtumwiyu, amene anakhala m’ndende kwa nthawi yaitali. Kodi inuyo mukuganiza kuti mungagwiritse ntchito mipata iti kuti muchereze ena n’kulimbitsidwa?​—Mac. 27:3.

6-8. Kodi Paulo anayenda bwanji kuchokera ku Sidoni kukafika ku Kinido, ndipo n’kutheka kuti anapeza mpata wolalikira kwa ndani?

6 Ngalawayo itachoka ku Sidoni, inapitiriza kuyenda m’mbali mwa nyanja ndipo inadutsa mzinda wa Kilikiya, womwe unali pafupi ndi mzinda wa Tariso, kwawo kwa Paulo. Luka sanatchulenso malo ena amene anaima, koma anatchula mfundo ina yochititsa mantha yakuti, ‘mphepo inkawomba kuchokera kutsogolo kwathu.’ (Mac. 27:4, 5) Ngakhale zinali choncho, sitikukayikira kuti Paulo anagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti alalikire uthenga wabwino. Iye ayenera kuti ankalalikira kwa akaidi anzake, anthu ogwira ntchito m’ngalawayo, asilikali ndiponso anthu amene ankakumana nawo m’madoko amene ngalawayo inkaima. Kodi nafenso masiku ano timagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene wapezeka kuti tilalikire kwa anthu ena?

7 Patapita nthawi, ngalawayo inafika kudoko la Mura, lomwe linali kugombe lakum’mwera kwa Asia Minor. Atafika kumeneko, Paulo ndi anthu amene anali nawo ankafunika kukwera ngalawa ina yopita ku Roma, komwe iwo ankapita. (Mac. 27:6) M’masiku amenewo, chakudya chambiri cha anthu a ku Roma chinkachokera ku Iguputo, ndipo ngalawa za ku Iguputo zonyamula tirigu zinkaima ku Mura. Yuliyo anapeza ngalawa imodzi yoteroyo n’kukwera limodzi ndi asilikali komanso akaidi aja. Zikuoneka kuti ngalawa imeneyi inali yokulirapo kuposa yoyamba ija. M’ngalawayo munali tirigu amene anali wamtengo wapatali komanso anthu okwana 276. Pa anthu amenewa panali anthu ogwira ntchito m’ngalawayo, asilikali, akaidi komanso mwina anthu ena amene ankapita ku Roma. Apatu Paulo anapeza anthu ambiri oti awalalikire ndipo ayenera kuti anagwiritsa ntchito bwino mpata umenewu.

8 Atachoka ku Mura anakaima ku Kinido, kum’mwera chakumadzulo kwa Asia Minor. Kukakhala mphepo yabwino, ngalawa inkatha kuyenda ulendo umenewu tsiku limodzi lokha. Koma Luka analemba kuti: “Tinayenda pang’onopang’ono kwa masiku angapo ndipo tinafika ku Kinido movutikira.” (Mac. 27:7a) Anthuwa anavutika kuyenda chifukwa panyanja pankawomba mphepo yamphamvu. (Onani bokosi lakuti, “ Mphepo Zoopsa Zapanyanja ya Mediterranean.”) Taganizirani mmene anthu mungalawayo ankamvera pamene ankalimbana ndi mphepo yamkuntho komanso mafunde.

‘Mphepo Yamkuntho Inkatikankha Mwamphamvu’ (Machitidwe 27:7b-26)

9, 10. Kodi anthu amene anali m’ngalawa anakumana ndi mavuto otani kufupi ndi Kerete?

9 Woyendetsa ngalawa ankafuna kuti apitirizebe ulendowo n’kumalowera chakumadzulo kwa Kinido, koma Luka analemba kuti analephera kupitirira “chifukwa cha mphepo yomwe inkawomba kuchokera kutsogolo.” (Mac. 27:7b) Pamene ngalawayo inayamba kutalikirana ndi mtunda, inasiya kukankhidwa ndi mphepo yochokera kumtunda. Kenako mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kumpoto chakumadzulo, inayamba kukankhira ngalawayo chakum’mwera mwamphamvu kwambiri. Pa nthawi ina m’mbuyomo chilumba cha Kupuro chinateteza ngalawayo ku mphepo yamkuntho. Apanso chilumba cha Kerete chinateteza ngalawayi. Ngalawayi itadutsa kaphiri kothera m’nyanja kotchedwa Salimone, komwe kanali kumapeto kwa chilumba cha Kerete chakum’mawa, zinthu zinakhalako bwino. Zinali choncho chifukwa ngalawayo inafika kum’mwera kwa chilumbacho, ndipo inatchingidwa ku mphepo yamkuntho imene inkawomba. Anthu amene anali m’ngalawamo mitima yawo inakhalako m’malo. Komabe kwa nthawi yonse imene ngalawayo inali panyanja, anthuwo ayenera kuti ankada nkhawa akakumbukira kuti nyengo yozizira ili pafupi.

10 Luka analemba mwatsatanetsatane kuti: “Titayenda movutikira m’mbali mwa chilumba chimenechi [cha Kerete], tinafika pamalo ena otchedwa Madoko Okoma.” Ngakhale kuti sankavutikanso kwambiri ndi mphepo chifukwa choti anali kufupi ndi kumtunda, zinali zovutabe kuti awongolere ngalawayo. Koma kenako anapeza malo oimika ngalawayo m’dera limene anthu amati lili pafupi ndi pamene gombe la nyanjayo limakhota n’kuyamba kulowera chakumpoto. Kodi anthuwa anakhala kumeneko nthawi yaitali bwanji? Luka ananena kuti anakhalako “nthawi yaitali.” Koma zimenezi zinali zoopsa chifukwa anali atayandikira miyezi ya September ndi October, pamene kuyenda panyanja kunkakhala koopsa.​—Mac. 27:8, 9.

11. Kodi Paulo anapereka malangizo otani kwa anthu amene anali m’ngalawa, koma iwo anachita chiyani?

11 Anthu ena m’ngalawamo mwina anafunsira nzeru kwa Paulo chifukwa chakuti iye anali atayendapo panyanja ya Mediterranean. Iye anawalangiza kuti ngalawayo isapitirize ulendowo. Anawauza kuti ikapitiriza ‘awonongetsa zambiri,’ mwinanso kufa kumene. Koma woyendetsa ndiponso mwiniwake wa ngalawayo ankafuna kupitiriza ulendowo n’cholinga choti akapeze malo abwino oimapo. Iwo anapangitsanso kuti Yuliyo agwirizane ndi maganizo awo oti apitirize ulendowo. Komanso anthu ambiri anavomereza kuti ayenera kukafika kudoko la Finikesi, lomwe linali kutsogolo. Mwina padoko limeneli panali malo aakulu komanso abwino pomwe akanatha kukhalapo m’nyengo yozizira. Choncho ataona kuti kwayamba kuwomba kamphepo kochokera kum’mwera, ngalawayo inanyamuka.​—Mac. 27:10-13.

12. Atachoka ku Kerete, kodi ngalawa inakumana ndi zoopsa zotani, nanga anthuwo anatani kuti aipulumutse?

12 Kenako kunayamba kuwomba “mphepo yamkuntho” yochokera kumpoto chakum’mawa. Kwakanthawi, iwo ankatchingidwa ndi “chilumba china chaching’ono chotchedwa Kauda,” chimene chinali pamtunda wa makilomita pafupifupi 65 kuchokera ku Madoko Okoma. Komabe, ngalawayo ikanatha kukankhidwira chakum’mwera mpaka kukafika kumilu ya mchenga, pafupi ndi gombe la ku Africa. Pofuna kupewa zimenezi, nthawi yomweyo oyendetsa anakweza m’ngalawamo bwato laling’ono limene ngalawayo inkakoka. Iwo anavutika kwambiri kuti achite zimenezi chifukwa bwato laling’onolo liyenera kuti linali litadzaza madzi. Kenako anayamba kumanga ngalawayo ndi zingwe kapena matcheni kuti alimbitse matabwa ake. Anthuwo anatsitsanso zingwe zomangira chinsalu cha ngalawa, ndipo anayesetsa kwambiri kuwongolera ngalawayo kuti adutse chimphepo chamkuntho. Zimenezi ziyenera kuti zinali zochititsa mantha kwambiri. Koma ngakhale kuti anachita zonsezi, ‘mphepo yamkuntho inapitirizabe kuwomba ndi kukankha mwamphamvu’ ngalawayo. Tsiku lachitatu, iwo anatayira m’madzi zingwe zokwezera chinsalu cha ngalawayo, mwina pofuna kuti isamire.​—Mac. 27:14-19.

13. Kodi zinthu zinali bwanji m’ngalawa imene Paulo anakwera pa nthawi imene kunali mphepo ya mkuntho?

13 Anthu ambiri m’ngalawamo ayenera kuti ankachita mantha kwambiri. Koma Paulo ndi anzake anali ndi chikhulupiriro kuti apulumuka. Ambuye anali atauza kale Paulo kuti akachitira umboni ku Roma, ndipo kenako mngelo anamutsimikizira kuti zimenezi zichitikadi. (Mac. 19:21; 23:11) Komabe, mphepo yamkunthoyo inapitirizabe kwa milungu iwiri, masana ndi usiku. Chifukwa chakuti kunkagwa mvula yosalekeza komanso kunali mitambo yambiri imene inaphimba dzuwa ndi nyenyezi, woyendetsa ngalawayo sankatha kudziwa pamene ali komanso kumene akulowera. Zinali zovuta kuti anthuwo adye popeza kunkazizira kwambiri, kunali mvula, ena ankasanza ndipo ena ankachita mantha kwambiri.

14, 15. (a) Polankhula ndi anthu amene anali nawo m’ngalawa, n’chifukwa chiyani Paulo anawakumbutsa za chenjezo limene anawapatsa? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa uthenga wolimbikitsa umene Paulo anauza anthuwo?

14 Kenako Paulo anaimirira ndipo anakumbutsa anthuwo chenjezo limene anawapatsa lija, koma sanalankhule mowanyoza, ngati akunena kuti, ‘Pajatu ndinakuuzani.’ Komabe, zimene zinkachitikazo unali umboni wosonyeza kuti zikanakhala bwino akanamvera malangizo ake aja. Ndiyeno anawauza kuti: “Musadandaule chifukwa palibe amene ataye moyo wake, koma ngalawa yokhayi iwonongeka.” (Mac. 27:21, 22) Mawu amenewa ayenera kuti analimbikitsa kwambiri anthuwo. Paulo ayenera kuti anasangalala kwambiri kuti Yehova anamuuza mawu olimbikitsa amenewa kuti auze anthuwo. N’zofunika kwambiri kuti tizikumbukira kuti Yehova amaona kuti moyo wa munthu aliyense ndi wofunika kwa iye. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Yehova . . . sakufuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Choncho n’zofunika kwambiri kuti panopa tiziuza anthu ambiri uthenga wa Yehova wopatsa chiyembekezo, chifukwa moyo wa anthu amenewa, amene Yehova amawaona kuti ndi amtengo wapatali, uli pangozi.

15 N’zodziwikiratu kuti Paulo anali atalalikira kwa anthu ambiri m’ngalawamo zokhudza “chiyembekezo cha zimene Mulungu analonjeza.” (Mac. 26:6; Akol. 1:5) Tsopano poona kuti nthawi iliyonse ngalawayo ikhoza kusweka, Paulo anathandiza anthuwo kukhala ndi chiyembekezo choti apulumuka. Iye anati: “Usiku wapitawu mngelo wa Mulungu wanga . . . anaima pafupi ndi ine n’kunena kuti: ‘Usaope Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Kaisara. Ndipo dziwa kuti chifukwa cha iwe, Mulungu apulumutsa anthu onse amene uli nawo pa ulendowu.’” Kenako Paulo anawalimbikitsa kuti: “Choncho limbani mtima anthu inu, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu achita zonse zimene wandiuza. Komabe, ngalawa yathuyi iwonongeka pafupi ndi chilumba chinachake.”​—Mac. 27:23-26.

“Onse Anafika Kumtunda Ali Bwinobwino” (Machitidwe 27:27-44)

“Anayamika kwa Mulungu pamaso pa onse.”​—Machitidwe 27:35

16, 17. (a) Kodi Paulo anapemphera pa nthawi iti, ndipo zimenezi zinakhudza bwanji anthu omwe anali naye? (b) Kodi mawu ochenjeza a Paulo anakwaniritsidwa bwanji?

16 Zinthu zochititsa manthazi zinachitika kwa milungu iwiri. Pa nthawi imeneyi, ngalawayo inakankhidwa kwa mtunda wa makilomita pafupifupi 870. Kenako oyendetsawo anazindikira kuti chinachake chasintha, mwina atayamba kumva phokoso la mafunde pagombe. Iwo anaponya anangula kumbuyo kwa ngalawayo kuti isatengeke ndi mafunde komanso kuti athe kuiwongolera mpaka kukafika bwinobwino m’mbali mwa nyanja. Atatero anthu ena ankafuna kutuluka m’ngalawayo, koma asilikali aja anawaletsa. Paulo anauza mkulu wa asilikali komanso asilikaliwo kuti: “Anthu awa akachoka m’ngalawa muno, simupulumuka.” Chifukwa choti tsopano ngalawa ija sinkakankhikakankhika kwambiri, Paulo analimbikitsa anthu onsewo kuti adye chakudya ndipo anawatsimikiziranso kuti apulumuka. Kenako Paulo “anayamika Mulungu pamaso pa onse.” (Mac. 27:31, 35) Popereka pemphero loyamikira limeneli, Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwa Luka, Arisitako ndi Akhristu masiku ano. Kodi mapemphero amene mumapereka pagulu amalimbikitsa ndiponso kutonthoza ena?

17 Paulo atamaliza kupemphera, “onse analimba mtima n’kuyamba kudya.” (Mac. 27:36) Kenako anatayanso tirigu amene ngalawayo inanyamula n’cholinga choti ipepukidwe kuti ithe kuyandama ikamayandikira kumtunda. Kutacha, oyendetsa ngalawayo anadula anangula, anamasulanso zingwe zomangira nkhafi zowongolera ndipo anakweza m’mwamba nsalu ya ngalawa yakutsogolo, kuti athe kuwongolera ngalawayo n’kukaiimitsa kugombe. Kenako kutsogolo kwa ngalawayo kunatitimira, mwina pachimulu chamchenga kapena m’matope, ndipo inayamba kusweka kumbuyo chifukwa cha mafunde amphamvu amene ankaiwomba. Asilikali ena ankafuna kupha akaidiwo kuti asathawe, koma Yuliyo anawaletsa. Iye anauza anthuwo kuti asambire kapena akwere pazidutswa za ngalawayo mpaka kukafika kugombe. Zimene Paulo ananena zija zinachitikadi. Anthu onse okwana 276 anapulumuka ndipo “onse anafika kumtunda ali bwinobwino.” Koma kodi pa nthawiyi iwo anali ali kuti?​—Mac. 27:44.

“Kukoma Mtima Kwapadera” (Machitidwe 28:1-10)

18-20. Kodi anthu a ku Melita anasonyeza bwanji “kukoma mtima kwapadera,” nanga Mulungu anachita chinthu chodabwitsa chiti kudzera mwa Paulo?

18 Anthu amene anapulumukawo anapezeka ali pachilumba cha Melita, kum’mwera kwa Sisile. (Onani bokosi lakuti, “ Kodi ku Melita Kunali Kuti?”) Anthu apachilumbacho, amene ankalankhula chilankhulo chachilendo, anawasonyeza “kukoma mtima kwapadera.” (Mac. 28:2) Iwo anawasonkhera moto alendowo, amene anafika atanyoweratu komanso akunjenjemera chifukwa chozizidwa. Motowo unawathandiza kuti amve kutenthera chifukwa kunkazizira komanso kunkagwa mvula. Koma kenako panachitika chinthu china chodabwitsa.

19 Paulo ankafuna kuthandiza nawo, choncho anatola nkhuni kuti aziike pamoto. Pamene ankaziponya pamotopo, munkhunimo munatuluka njoka ya mphiri yapoizoni ndipo inamuluma n’kukanirira kudzanja lake. Anthu apachilumbacho ankaganiza kuti chimenechi ndi chilango chochokera kwa milungu. a

20 Anthu apachilumbapo amene anaona kuti Paulo walumidwa ndi njoka ankaganiza kuti iye “atupa.” Buku lina linafotokoza kuti mawu a chilankhulo choyambirira amene anagwiritsidwa ntchito palembali ndi “azachipatala.” N’zosadabwitsa kuti mawu amenewa ndi amene anabwera msanga m’maganizo mwa “Luka, dokotala wokondedwa.” (Mac. 28:6; Akol. 4:14) Koma Paulo anangoikutumulira pamoto njoka yapoizoniyo ndipo sinamuvulaze.

21. (a) Kodi munkhani ya m’Baibulo imeneyi muli zitsanzo ziti zosonyeza kuti Luka anafotokoza zinthu molondola? (b) Kodi Paulo anachita zinthu zodabwitsa ziti, nanga anthu a ku Melita anakhudzidwa bwanji?

21 M’deralo munkakhala munthu wina wolemera amene anali ndi malo, dzina lake Papuliyo. Mwina iyeyu anali msilikali wamkulu wa Aroma pachilumba cha Melita. Luka anafotokoza kuti Papuliyo anali “munthu woyang’anira chilumbacho.” Mawu onena za udindo amenewa ndi olondola ndipo anapezekanso m’zolembedwa zinazake ziwiri za ku Melita. Iye analandira bwino kwambiri Paulo ndi anzake aja ndipo anawachereza kwa masiku atatu. Koma bambo ake a Papuliyo ankadwala. Apanso Luka anafotokoza molondola kwambiri za matenda awo pogwiritsa ntchito mawu azachipatala. Iye analemba kuti bambowo “ankadwala malungo komanso kamwazi ndipo anali chigonere.” Paulo anapemphera n’kusanjika manja ake pa bambowo ndipo anachira. Anthu apachilumbacho anachita chidwi kwambiri ataona zimenezi ndipo anayamba kubweretsa odwala ena kuti adzachiritsidwe. Iwo anabweretsanso mphatso zoti zithandize Paulo ndi anzake aja pa ulendo wawo.​—Mac. 28:7-10.

22. (a) Kodi pulofesa wina ananena chiyani poyamikira zimene Luka analemba zokhudza ulendo wawo wopita ku Roma? (b) Kodi m’mutu wotsatira tikambirana chiyani?

22 Mbali ya ulendo wa Paulo imene takambirana kufika pano ikusonyeza kuti inalembedwa molondola kwambiri komanso nkhani zake ndi zoona. Pulofesa wina anati: “Nkhani imene Luka analemba . . . ndi imodzi mwa nkhani zofotokozedwa mwatsatanetsatane kwambiri m’Baibulo lonse. Iye anafotokoza molondola kwambiri zinthu zokhudzana ndi maulendo apanyanja a pa nthawiyo komanso mmene nyengo inkakhalira kum’mawa kwa nyanja ya Mediterranean,” moti ayenera kuti anagwiritsa ntchito zimene ankalemba yekha m’buku lake la zochitika za tsiku ndi tsiku. Mwina Luka ankalemba zimenezi pamene ankayenda ndi mtumwi Paulo pa ulendowu. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti iye anapeza zambiri zolemba pamene ankapitiriza ulendo wawo. Kodi Paulo anakumana ndi zotani atafika ku Roma? Tiyeni tione.

a Popeza anthuwa anaizindikira njokayo, zikusonyeza kuti njoka za mphiri zinkapezeka pachilumbacho pa nthawiyo. Koma masiku ano ku Melita sikupezeka mphiri. Mwina n’chifukwa chakuti pofika pano nyengo ndi nthaka zinasintha kwambiri pachilumbapo. Mwinanso kuchuluka kwa anthu kunachititsa kuti njoka za mphiri zithe.