Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 7 • MACHITIDWE 18:23–21:17

‘Ankaphunzitsa Pagulu Komanso Kunyumba ndi Nyumba’

‘Ankaphunzitsa Pagulu Komanso Kunyumba ndi Nyumba’

MACHITIDWE 20:20

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala odzichepetsa komanso ofunitsitsa kusintha ulaliki wathu kuti ugwirizane ndi anthu amene tikuwalalikira? Kodi njira yaikulu yolalikirira uthenga wabwino ndi iti? Kodi tingasonyeze bwanji kuti kuchita chifuniro cha Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kuchita zofuna zathu? Nkhani yosangalatsa yofotokoza mmene Paulo anayendera pa ulendo wake wachitatu waumishonale umenenso unali womaliza, itithandiza kuyankha mafunso ofunika amenewa.