Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 20

“Anapitiriza kufalikira Ndipo Sankagonjetseka” Ngakhale Kuti Panali Otsutsa

“Anapitiriza kufalikira Ndipo Sankagonjetseka” Ngakhale Kuti Panali Otsutsa

Zimene Apolo ndi Paulo anachita kuti uthenga wabwino ufalikire

Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 18:23–19:41

1, 2. (a) Kodi ndi zinthu zoopsa ziti zimene zinachitikira Paulo ndi anzake ku Efeso? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutuwu?

 MUMZINDA wa Efeso munali chipwirikiti. Anthu ankathamanga m’misewu yamumzindawu ndipo ankafuula kwambiri. Iwo anali atagwira anthu awiri amene ankayenda ndi mtumwi Paulo pamene ankagwira ntchito yake yolalikira. Pasanapite nthawi yayitali, anthu onse amene anali mumsewu umene unadutsa pakati pa mashopu, anathamangira kumene kunali anthuwo ndipo chipwirikiticho chinakula kwambiri. Anthuwo anathamangira kubwalo lina lochitira masewera osiyanasiyana mumzindawo, ndipo bwalolo linali lalikulu kwambiri moti anthu okwana 25,000 ankatha kulowamo n’kumaonerera masewera. Ambiri mwa anthuwo sankadziwa n’komwe chimene chinayambitsa chipwirikiticho, koma ankangoganiza kuti anthu ena aukira kachisi wawo komanso mulungu wawo Atemi, amene ankamukonda kwambiri. Choncho iwo anayamba kufuula mobwerezabwereza kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!”​—Mac. 19:34.

2 Apanso tikuona kuti Satana anayesa kugwiritsa ntchito gulu la anthu achiwawa pofuna kuti uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu usafalikire. Komabe, Satana sagwiritsa ntchito njira yokhayi pofuna kukwaniritsa zolinga zake. M’mutuwu tikambirana njira zingapo zimene Satana anagwiritsa ntchito pofuna kusokoneza ntchito komanso mgwirizano wa Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti tiona kuti njira zonse zimene anagwiritsa ntchito zinalephera chifukwa “mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndipo sankagonjetseka.” (Mac. 19:20) N’chiyani chinathandiza Akhristuwo kuti apambane? Chifukwa chake ndi chofanana ndi chimene chimatithandiza ifeyo kuti tizipambana masiku ano. N’zoona kuti Yehova ndi amene amapambana osati ifeyo. Komabe, monga mmene anachitira Akhristu a m’nthawi ya atumwi, ifenso tiyenera kuchita khama pa ntchito yolalikira. Mzimu wa Yehova ungatithandize kuti tikhale ndi makhalidwe amene angatithandize kuti tikwanitse utumiki wathu. Koma choyamba tiyeni tikambirane chitsanzo cha Apolo.

“Iyeyu Ankadziwanso Bwino Malemba” (Machitidwe 18:24-28)

3, 4. Kodi Akula ndi Purisila anaona kuti Apolo sankadziwa chiyani, nanga anamuthandiza bwanji?

3 Pamene Paulo ankapita ku Efeso pa ulendo wake wachitatu waumishonale, Myuda wina dzina lake Apolo anali atafika kale mumzindawo. Iye anali wochokera mumzinda wotchuka wa Alekizandiriya, m’dziko la Iguputo. Apolo anali ndi luso lapadera lodziwa kulankhula bwino kwambiri. Kuwonjezera pamenepo “iyeyu ankadziwanso bwino Malemba,” komanso “anali ndi mzimu woyera.” Popeza kuti Apolo anali wakhama kwambiri polalikira, iye ankatha kulankhula molimba mtima kwa Ayuda m’sunagoge.​—Mac. 18:24, 25.

4 Akula ndi mkazi wake Purisila anamvetsera ulaliki wa Apolo ndipo n’zosakayikitsa kuti anasangalala kwambiri kumva Apolo akuphunzitsa “molondola za Yesu.” Ngakhale kuti Apolo ankaphunzitsa za Yesu molondola, pasanapite nthawi Akula ndi Purisila anazindikira kuti pali mfundo zina zofunika kwambiri zimene iye sankazidziwa. Iye ankangodziwa “za ubatizo wa Yohane wokha.” Banjali, lomwe linkagwira ntchito yopanga matenti, silinachite mantha ndi Apolo amene anali wodziwa kulankhula ndiponso wophunzira kwambiri. Koma iwo “anamutenga n’kumufotokozera njira ya Mulungu molondola.” (Mac. 18:25, 26) Kodi munthu wophunzira ndiponso wodziwa kulankhulayu anatani? N’zoonekeratu kuti anasonyeza khalidwe lofunika kwambiri la kudzichepetsa, limene Mkhristu aliyense ayenera kuyesetsa kuti akhale nalo.

5, 6. N’chifukwa chiyani Yehova anagwiritsa ntchito kwambiri Apolo, nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani pa chitsanzo chake?

5 Apolo anakhala mtumiki wodalirika wa Yehova chifukwa chakuti analola kuthandizidwa ndi Akula ndi Purisila. Iye anapita ku Akaya kumene “anathandiza kwambiri” okhulupirira. Apolo anachitiranso umboni kwa Ayuda am’dera limenelo, amene ankaumirira mfundo yakuti Yesu sanali Mesiya wolonjezedwa. Luka ananena kuti: “Iye anawatsimikizira Ayuda . . . mwamphamvu kuti anali olakwa, ndipo anagwiritsa ntchito Malemba posonyeza kuti Yesu ndiyedi Khristu.” (Mac. 18:27, 28) N’zoonekeratu kuti Apolo anathandiza kwambiri mipingo. Tinganene kuti nayenso anathandiza kuti anthu ambiri amve “mawu a Yehova.” Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Apolo?

6 Akhristu onse ayenera kuyesetsa kuti akhale odzichepetsa. Aliyense wa ife ali ndi mphatso zosiyanasiyana, monga luso lachibadwa kapena anaphunzira kuchita bwino zinthu zinazake. Komabe tiziyesetsa kuti khalidwe lathu lodzichepetsa lizionekera kwambiri kuposa mphatso zimene tili nazo. Kupanda kutero, mphatso zimene tili nazozo zingatipangitse kukhala ndi vuto, monga kudzikuza. (1 Akor. 4:7; Yak. 4:6) Ngati tilidi odzichepetsa tidzayesetsa kuona kuti anthu ena amatiposa. (Afil. 2:3) Sitidzakana malangizo kapena kudana n’zoti ena azitiphunzitsa. Sitidzaumirira maganizo athu modzikonda tikadziwa kuti maganizo athuwo ndi osemphana ndi mfundo zatsopano zimene mzimu woyera watithandiza kuzimvetsa. Tikapitiriza kukhala odzichepetsa, Yehova ndi Mwana wake adzapitiriza kutigwiritsa ntchito.​—Luka 1:51, 52.

7. Kodi Paulo ndi Apolo anasonyeza bwanji chitsanzo cha kudzichepetsa?

7 Kudzichepetsa kumathandizanso kuti anthu apewe mpikisano. Satana ankafunitsitsa kuti agawanitse Akhristu oyambirirawo. N’zodziwikiratu kuti iye akanasangalala kwambiri ngati amuna odalirika ngati Apolo ndi mtumwi Paulo, akanayamba kupikisana ndi kuchitirana nsanje mwina chifukwa chofuna kutchuka m’mipingo. Ndipotu zinali zosavuta kwa iwo kuchita zimenezi chifukwa ku Korinto Akhristu ena anayamba kunena kuti, “Ine ndine wa Paulo,” pomwe ena ankanena kuti, “Ine ndine wa Apolo.” Kodi Paulo ndi Apolo analimbikitsa anthu kuti azinena mawu ogawanitsawo? Ayi. Modzichepetsa Paulo ananena kuti Apolo anathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira ndipo anam’patsa mautumiki ena apadera. Apolo nayenso anatsatira malangizo a Paulo. (1 Akor. 1:10-12; 3:6, 9; Tito 3:12, 13) Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife masiku ano kuti tizichita zinthu mogwirizana komanso modzichepetsa.

‘Anawafotokozera Mfundo Zogwira Mtima Zokhudza Ufumu’ (Machitidwe 18:23; 19:1-10)

8. Kodi Paulo anadutsa njira iti pobwerera ku Efeso nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?

8 Paulo analonjeza kuti adzabwerera ku Efeso ndipo anachitadi zimene analonjezazo. a (Mac. 18:20, 21) Komabe taonani njira imene anadutsa pobwererapo. Munkhani yapita, tinaona kuti Paulo anali ku Antiokeya wa ku Siriya. Kuti akafike ku Efeso, iye akanatha kudutsa njira yachidule yopita ku Selukeya, kenako n’kukwera ngalawa yopita kumene ankafuna. M’malomwake iye “anadzera kumadera akumtunda.” Anthu ena amanena kuti ulendo wa Paulo umene watchulidwa pa Machitidwe 18:23 ndi 19:1, unali wa makilomita pafupifupi 1,600. N’chifukwa chiyani Paulo anasankha kudutsa njira yovuta komanso yaitaliyo? Chifukwa ankafuna ‘kulimbikitsa ophunzira onse.’ (Mac. 18:23) Mofanana ndi ulendo wake woyamba ndi wachiwiri, Paulo ankadziwa kuti ulendo wake wachitatu waumishonale ukhalanso wovuta koma ankaona kuti afunikabe kuyenda ulendo umenewo. Masiku ano oyang’anira madera ndi akazi awo amasonyezanso mtima womwewo. Kodi sitikuyenera kuwayamikira chifukwa cha chikondi chawo chololera kuvutikira ena?

9. N’chifukwa chiyani ophunzira ena anafunika kubatizidwanso, ndipo ifeyo tikuphunzirapo chiyani?

9 Atangofika ku Efeso, Paulo anapeza gulu la ophunzira a Yohane M’batizi pafupifupi 12. Iwo anali atabatizidwa kale ndi Yohane koma pa nthawiyi ubatizo umenewo sunkagwiranso ntchito. Komanso zikuoneka kuti ankadziwa zinthu zochepa, kapena sankadziwa chilichonse chokhudza mzimu woyera. Choncho Paulo anawafotokozera kufunika kobatizidwa m’dzina la Yesu ndipo mofanana ndi Apolo, iwo anasonyeza mtima wodzichepetsa ndiponso wofunitsitsa kuphunzira. Ophunzirawo atabatizidwa m’dzina la Yesu, analandira mzimu woyera ndiponso mphatso zina zoti azichitira zinthu zozizwitsa. Apa n’zodziwikiratu kuti Yehova amadalitsa anthu amene ndi ofunitsitsa kutsatira malangizo atsopano amene gulu lake limapereka.​—Mac. 19:1-7.

10. N’chifukwa chiyani Paulo anachoka kusunagoge n’kupita kuholo yapasukulu, nanga tingamutsanzire bwanji tikamalalikira?

10 Pasanapite nthawi, panachitikanso zinthu zina zabwino. Kwa miyezi itatu, Paulo ankalalikira molimba mtima m’sunagoge. Ngakhale kuti iye ‘ankawafotokozera mfundo zogwira mtima zokhudza ufumu wa Mulungu,’ ena anapitiriza kuumitsa mitima yawo ndipo ankamutsutsa kwambiri. M’malo motaya nthawi ndi anthu amene “ankanena zonyoza Njirayo,” Paulo anachoka n’kuyamba kuphunzitsa muholo yapasukulu ina. (Mac. 19:8, 9) Anthu amene ankafuna kupitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu, ankafunika kuchoka kusunagoge n’kupita kuholoyo. Mofanana ndi Paulo, nthawi zina tingafunike kusiya kukambirana ndi anthu amene sakufuna kumvetsera uthenga wathu koma akungofuna kuti tizikangana nawo. Tisaiwale kuti pali anthu ambiri amene ali ngati nkhosa omwe akufuna kumva uthenga wathu wolimbikitsa.

11, 12. (a) Kodi Paulo anatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani yochita khama komanso kusintha njira zolalikirira? (b) Kodi a Mboni za Yehova amayesetsa bwanji kuchita khama ndiponso kusintha akamalalikira?

11 N’kutheka kuti Paulo ankaphunzitsa muholo pasukuluyo tsiku lililonse, kuyambira 11 koloko m’mawa mpaka 4 koloko madzulo. (Mac. 19:9) N’kutheka kuti imeneyi inali nthawi yotentha kwambiri ndipo sikunkakhala phokoso lambiri. Choncho inali nthawi yabwino kwambiri chifukwa anthu ambiri ankasiya kaye kugwira ntchito kuti apume ndi kudya. Ngati Paulo ankachita zimenezi tsiku ndi tsiku kwa zaka ziwiri zathunthu, ndiye kuti anaphunzitsa kwa maola oposa 3,000, ndipo zimenezi zikutanthauza kuti mwezi uliwonse ankaphunzitsa kwa maola 125. b Paulo ankagwira ntchitoyi mwakhama kwambiri ndipo ankasintha ulaliki wake kuti ugwirizane ndi anthu am’deralo komanso mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Kodi zimenezi zinathandiza bwanji? Nkhaniyi imati: “Anthu onse okhala m’chigawo cha Asia, Ayuda ndi Agiriki omwe, anamva mawu a Ambuye.” (Mac. 19:10) Apa zikuonekeratu kuti Paulo anachitira umboni mokwanira.

Timayesetsa kulankhula ndi anthu kulikonse kumene angapezeke

12 Masiku anonso, a Mboni za Yehovafe timachita utumiki wathu mwakhama komanso timasintha njira zolalikirira kuti zigwirizane ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Timayesetsa kufufuza anthu pa nthawi iliyonse komanso kulikonse kumene angapezeke. Timalalikira m’misewu, m’misika ndiponso m’malo oimika magalimoto. Nthawi zina timalalikira anthu powaimbira foni kapena powalembera kalata. Ndipo tikamalalikira kunyumba ndi nyumba, timayesetsa kuti tipite pa nthawi imene anthu angapezeke pakhomo.

Mizimu Yoipa Sinalepheretse Kuti Mawu a Yehova ‘Afalikire Ndipo Sankagonjetseka’ (Machitidwe 19:11-22)

13, 14. (a) Kodi Yehova anathandiza Paulo kuti achite chiyani? (b) Kodi ana a Sikeva anachita zinthu ziti zolakwika, nanga masiku ano anthu ambiri a m’matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu amachitanso zinthu ziti zolakwika zofanana ndi zimenezi?

13 Luka akutiuza kuti panali zinthu zabwino kwambiri zimene zinachitika pa utumiki wa Paulo chifukwa Yehova anamuthandiza “kuchita zinthu zamphamvu komanso zodabwitsa.” Anthu ankatenga ngakhale tinsalu ndi maepuloni amene Paulo ankavala n’kupita nazo kwa anthu odwala ndipo ankachiritsidwa. Komanso anthu ankatulutsa mizimu yoipa pogwiritsa ntchito zinthu zimenezi. c (Mac. 19:11, 12, mawu a m’munsi.) Anthu ambiri anachita chidwi ndi zozizwitsa zimenezi, zomwe zinasonyeza kuti Satana wagonjetsedwa. Koma si onse amene ankasangalala nazo.

14 “Ayuda ena amene ankayendayenda n’kumatulutsa ziwanda,” anayesa kutsanzira zozizwitsa zimene Paulo ankachita. Ena mwa Ayuda amenewo ankayesa kutulutsa ziwanda potchula dzina la Yesu ndiponso Paulo. Luka anapereka chitsanzo cha ana aamuna 7 a Sikeva a m’banja la ansembe, omwe anayesa kuchita zimenezi. Koma chiwandacho chinawauza kuti: “Ine Yesu ndikumudziwa ndipo Paulo ndikumudziwanso bwino. Nanga inuyo ndinu ndani?” Kenako munthu amene anagwidwa ndi chiwandayo anawalumphira ngati chilombo cholusa n’kuyamba kulimbana nawo, ndipo iwo anayamba kuthawa ali maliseche komanso atavulala. (Mac. 19:13-16) Pamenepa zikuonekeratu kuti “mawu a Yehova” anapambana makamaka tikaona mphamvu zimene Paulo anapatsidwa komanso zimene zinachitikira ana a Sikeva amene kulambira kwawo kunali kwabodza. Masiku anonso pali anthu ambiri amene amaganiza kuti kungotchula dzina la Yesu, kapena kungodzitchula kuti ndi “Akhristu,” n’kokwanira. Komabe, zimene Yesu ananena zikusonyeza kuti anthu okhawo amene amachitadi zimene Atate wake amafuna ndi amene akuyembekezera kudzapeza moyo wosatha.​—Mat. 7:21-23.

15. Kodi tingatsanzire bwanji zimene anthu a ku Efeso anachita pa nkhani ya kukhulupirira mizimu ndiponso chinthu chilichonse chokhudzana ndi zamizimu?

15 Zinthu zochititsa manyazi zimene zinachitikira ana a Sikeva zinachititsa kuti anthu ambiri ayambe kuopa Mulungu, moti ambiri anasiya kukhulupirira mizimu ndipo anakhala Akhristu. Anthu a ku Efeso ankakhulupirira kwambiri zamatsenga ndipo zinthu monga maula, zithumwa komanso mabuku a zamatsenga zinali zofala kwambiri. Koma izi zitachitika anthu ambiri a ku Efeso anabweretsa mabuku awo a zamatsenga n’kuwawotcha anthu onse akuona. Iwo anachita zimenezi ngakhale kuti mabukuwo anali okwera mtengo kwambiri. d Luka analemba kuti: “Choncho mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndipo sankagonjetseka.” (Mac. 19:17-20) Umenewu ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti choonadi chinagonjetsa chinyengo ndiponso ziwanda. Zimene anthu okhulupirikawo anachita zikutipatsa chitsanzo chabwino kwambiri masiku ano. Ifenso tikukhala m’dziko limene anthu ambiri amakhulupirira zamizimu. Ngati tadziwa kuti tili ndi chinachake chimene chikukhudzana ndi zamizimu, tiyenera kuchiwotcha mwamsanga ngati mmene anachitira anthu a ku Efeso. Tisayese n’komwe kukhala ndi chilichonse chokhudzana ndi zamizimu, ngakhale chinthucho chitakhala cha ndalama zambiri.

“Panayambika Chisokonezo Chachikulu” (Machitidwe 19:23-41)

“Anthu inu, mukudziwa kuti timapeza chuma kuchokera mu ntchito imeneyi.”​—Machitidwe 19:25

16, 17. (a) Fotokozani mmene Demetiriyo anayambitsira chipwirikiti ku Efeso. (b) Kodi anthu a ku Efeso anasonyeza bwanji mtima wokonda kwambiri chipembedzo chawo?

16 Tsopano tiyeni tione njira ina imene Satana amagwiritsa ntchito pofuna kusokoneza atumiki a Mulungu. Luka ankanena za njira imeneyi pamene analemba kuti “panayambika chisokonezo chachikulu chokhudza Njira ya Ambuye.” Pamenepa, sikuti iye ankangokokomeza zinthu. e (Mac. 19:23) Munthu wina wosula siliva dzina lake Demetiriyo anayambitsa mavuto. Iye anakopa amisiri anzake powakumbutsa kuti amapeza ndalama chifukwa chogulitsa mafano. Kenako iye ananena kuti uthenga umene Paulo ankalalikira ukanachititsa kuti malonda awo asamayende bwino chifukwa Akhristu salambira mafano. Demetiriyo anakopanso anthu a ku Efeso chifukwa chakuti iwo ankanyada kwambiri kuti ndi nzika za mzindawo komanso ankakonda kwambiri dziko lawo. Iye anawachenjeza kuti ulemerero wa mulungu wawo wamkazi Atemi ndiponso kachisi wake amene anali wotchuka kwambiri padziko lonse, ‘azidzaonedwa ngati wopanda pake.’​—Mac. 19:24-27.

17 Zimene Demetiriyo ankafuna zinachitikadi. Amisiri osula silivawo anayamba kufuula kuti, “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!” Kenako mumzindawo munayambika chipwirikiti chimene tachitchula kumayambiriro kwa nkhaniyi. f Chifukwa choti anali wodzipereka, Paulo ankafuna kulowa m’bwalo la masewera kuti akalankhule ndi gulu la anthulo, koma ophunzira anamuchonderera kuti asaike dala moyo wake pachiswe. Munthu wina dzina lake Alekizanda anaimirira kutsogolo kwa gulu la anthulo ndipo anayesa kuti alankhule. Popeza kuti iye anali Myuda, ayenera kuti ankafunitsitsa kuti afotokoze kusiyana kwa Ayuda ndi Akhristuwo. Komabe zimene iye ankafuna kufotokozazo sizikanaphula kanthu. Anthuwo atazindikira kuti iye ndi Myuda, anayamba kufuula mobwerezabwereza kwa maola pafupifupi awiri kuti, “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!” Masiku anonso, anthu amene ali ndi mtima wokonda kwambiri chipembedzo chawo adakalipo ndipo mtima umenewu umawachititsa kuti azichita zinthu mosaganiza bwino.​—Mac. 19:28-34.

18, 19. (a) Kodi woyang’anira mzinda anatani kuti aletse chipwirikiti ku Efeso? (b) Kodi nthawi zina anthu a Yehova amatetezedwa bwanji ndi akuluakulu aboma, ndipo ifeyo tingatani kuti zinthu zizitiyendera bwino?

18 Kenako woyang’anira mzindawo anauza gulu la anthulo kuti likhale chete. Woyang’anira mzindayu anali wanzeru ndipo anatsimikizira anthuwo kuti Akhristuwo sanachite chinthu chilichonse choukira kachisi komanso mulungu wawo wamkazi. Iye anawauzanso kuti Paulo ndi anzakewo sanachite chilichonse chotsutsana ndi kachisi wa Atemi komanso anawauza kuti pali njira yoyenerera yothetsera milandu ngati imeneyi. Mwina iye ananena mfundo yogwira mtima kwambiri pamene anakumbutsa gulu la anthuwo kuti Aroma akanatha kuwaimba mlandu chifukwa cha chipwirikiti chimene anayambitsacho. Atanena zimenezi, anthuwo anachoka pamalopo. Chifukwa cha mawu anzeru amene woyang’anira kachisi uja analankhula, chipwirikiticho chinatha mofulumira kwambiri ngati mmene chinayambira.​—Mac. 19:35-41.

19 Imeneyi sinali nthawi yoyamba kapena yomaliza kuti munthu wanzeru ndiponso waudindo waukulu m’boma ateteze otsatira a Yesu. Ndipotu mtumwi Yohane anaona masomphenya osonyeza kuti m’masiku otsiriza ano, anthu a maudindo akuluakulu m’dzikoli, omwe atchulidwa kuti dziko lapansi, adzameza mtsinje wamadzi ambiri wa Satana, umene ukuimira kuzunzidwa kwa anthu otsatira Khristu. (Chiv. 12:15, 16) Zimenezi n’zimene zikuchitikadi masiku ano. Nthawi zambiri, anthu oweruza milandu amene ali ndi maganizo abwino, amateteza Mboni za Yehova kuti zikhale ndi ufulu wolambira ndiponso wolalikira uthenga wabwino. Ndipotu khalidwe lathu labwino lingathandize kuti oweruzawo aziteteza ufulu wathuwu. Zikuoneka kuti akuluakulu ena aboma ku Efeso ankalemekeza Paulo chifukwa cha khalidwe lake labwino ndipo anayesetsa kuti iye asavulazidwe. (Mac. 19:31) Ifenso tiziyesetsa kukhala oona mtima komanso aulemu kuti anthu amene timawalalikira azikopeka ndi uthenga wathu, chifukwa sitikudziwa zinthu zabwino zimene zingachitike chifukwa chakuti tikusonyeza makhalidwe abwino.

20. (a) Kodi mumamva bwanji mukaganizira kuti mawu a Yehova sankagonjetseka m’nthawi ya atumwi komanso kuti sakugonjetseka masiku ano? (b) Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani mukaona mmene Yehova akuthandizira gulu lake masiku ano?

20 N’zosangalatsa kwambiri tikaona kuti m’nthawi ya atumwi, “mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndipo sankagonjetseka.” N’zosangalatsanso kuona mmene Yehova akuthandizira atumiki ake masiku ano kuti zinthu ziziwayendera bwino. Kodi inuyo simungayesetse kuchita zimene mungathe kuti mukhale ndi mwayi wothandiza nawo anthu a Mulungu kuti zinthu ziziwayendera bwino? Ngati ndi choncho, tsanzirani zitsanzo zimene takambirana munkhaniyi. Khalani wodzichepetsa, muzichita zinthu zogwirizana ndi gulu la Yehova limene likupita patsogolo, pitirizani kugwira ntchito mwakhama, muzipewa zinthu zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu ndiponso muzichita chilichonse chotheka kuti muzitha kuchitira umboni chifukwa cha khalidwe lanu la kuona mtima ndi laulemu.

a Onani bokosi lakuti “ Mzinda wa Efeso Unali Likulu la Asia.”

b Paulo analembanso buku la 1 Akorinto ali ku Efeso.

c N’kutheka kuti timeneti tinali tinsalu timene Paulo ankamanga pachipumi kuti thukuta lisamayenderere n’kulowa m’maso. Komanso mfundo yakuti Paulo ankavala maepuloni ikusonyeza kuti iye ankagwira ntchito yake yokonza matenti pa nthawi yake yopuma, mwina m’mawa kwambiri.​—Mac. 20:34, 35.

d Luka ananena kuti mabukuwo anali a ndalama zasiliva zokwana 50,000. Ngati ndalama zake zinali madinari, ndiye kuti munthu ankafunika kugwira ntchito tsiku lililonse kwa masiku 50,000, zomwe ndi zaka pafupifupi 137, kuti apeze ndalama zimenezo.

e Anthu ena amati Paulo ankanena zimene zinamuchitikira pa nthawiyi pamene anauza anthu a ku Korinto kuti: “Tinalibe chiyembekezo choti tikhala ndi moyo.” (2 Akor. 1:8) Komabe, n’kutheka kuti ankatanthauza zinthu zina zoopsa zimene zinamuchitikira pa nthawi ina. Pamene Paulo analemba kuti “ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso,” ayenera kuti ankatanthauza kuti anamenyanadi ndi zilombo zolusa m’bwalo la masewera, kapenanso ankatanthauza anthu amene ankamutsutsa. (1 Akor. 15:32) N’kutheka kuti mawu amenewa angatanthauze zilombo zenizeni kapena zophiphiritsa.

f Magulu a anthu ngati amenewa anali amphamvu kwambiri. Mwachitsanzo, patapita zaka pafupifupi 100, gulu la anthu ophika buledi linayambitsa chipolowe changati chimenechi ku Efeso.