Mlozera wa Zithunzi
Potengera Masamba a M’bukuli
Pazikuto: Paulo, Tabita, Galiyo, Luka, msilikali wapakachisi ali ndi atumwi, Msaduki, Paulo akumuperekeza ku Kaisareya, kulalikira masiku ano, galimoto yokhala ndi zokuzira mawu ndiponso galamafoni.
Tsamba 1 Paulo atamangidwa maunyolo ali ndi Luka m’ngalawa yonyamula katundu yopita ku Roma.
Masamba 2, 3 M’bale J. E. Barr ndi M’bale T. Jaracz a m’Bungwe Lolamulira, akuyang’ana mapu a dziko lapansi.
Tsamba 11 Yesu akupereka ntchito kwa atumwi 11 okhulupirika ndi otsatira ake ena paphiri ku Galileya.
Tsamba 14 Yesu akukwera kumwamba. Atumwi akumuyang’anitsitsa.
Tsamba 20 Pa Pentekosite, ophunzira akulankhula ndi alendo m’zilankhulo za alendowo.
Tsamba 36 Atumwi aimirira pamaso pa Kayafa amene wakwiya kwambiri. Asilikali apakachisi ndi okonzeka kumanga atumwiwo ngati atauzidwa ndi oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda.
Tsamba 44 M’munsi: Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, khoti lina la ku East Germany linagamula molakwa kuti Mboni za Yehova ndi akazitape a dziko la America.—Neue Berliner Illustrierte, October 3, 1950.
Tsamba 46 Sitefano akuimbidwa mlandu m’Khoti Lalikulu la Ayuda. Asaduki olemera ali chakumbuyo ndipo Afarisi otsatira miyambo ya chipembedzo chawo monyanyira ali kutsogolo.
Tsamba 54 Petulo waika dzanja lake pa wophunzira watsopano. Simoni wanyamula kathumba ka ndalama.
Tsamba 75 Petulo ndi anzake amene ankayenda naye akulowa m’nyumba ya Koneliyo. Koneliyo wapachika chinsalu paphewa lake lakumanzere chosonyeza udindo wake monga kapitawo wa asilikali a Chiroma.
Tsamba 83 Petulo akutulutsidwa m’ndende ndi mngelo. N’kutheka kuti ndendeyi inali mu Nsanja ya Antoniya.
Tsamba 84 M’munsi: Anthu achiwawa pafupi ndi ku Montreal, ku Quebec, mu 1945.—Weekend Magazine, July 1956.
Tsamba 91 Paulo ndi Baranaba awaponya kunja kwa mzinda wa Antiokeya wa ku Pisidiya. Chakumbuyo, kuli ngalande zatsopano za madzi. Mwina ngalandezi zinamangidwa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 100 C.E.
Tsamba 94 Paulo ndi Baranaba akuletsa anthu kuti asawalambire ku Lusitara. Anthu akamapereka nsembe, kawirikawiri ankavala zovala zokongola n’kumaimba nyimbo mokweza kwambiri.
Tsamba 100 Pamwamba: Sila ndi Yudasi akulimbikitsa mpingo ku Antiokeya wa ku Siriya. (Machitidwe 15:30-32) M’munsi: Woyang’anira dera akukamba nkhani pampingo ku Uganda.
Tsamba 107 Mpingo wa ku Yerusalemu wasonkhana m’nyumba ya Mkhristu wina.
Tsamba 124 Paulo ndi Timoteyo ali m’ngalawa ya ku Roma yonyamula katundu. Chakutsogoloko kukuoneka nsanja yokhala ndi nyale yotsogolera oyendetsa ngalawa.
Tsamba 139 Paulo ndi Sila ali m’bwalo lotchingidwa ndi geti, ndipo akuthawa anthu achiwawa.
Tsamba 155 Galiyo akukalipira anthu amene akuimba Paulo mlandu. Iye wavala zovala zogwirizana ndi udindo wake. Wavala mkanjo woyera wachifumu wokhala ndi mpendero wofiirira ndi nsapato yooneka ngati jombo.
Tsamba 158 Demetiriyo akulankhula ndi amisiri osula siliva m’malo awo ogwirira ntchito ku Efeso. Amisiriwa amagulitsa tiakachisi tasiliva ta Atemi kwa alendo.
Tsamba 171 Paulo ndi anzake akukwera ngalawa. Chakumbuyo kukuoneka chipilala chotchedwa Great Harbor, chimene chinamangidwa m’zaka za m’ma 100 B.C.E.
Tsamba 180 M’munsi: Mabuku a Mboni za Yehova ataletsedwa ku Canada m’ma 1940, wa Mboni wachinyamata wabweretsa mozemba mabuku ofotokoza za m’Baibulo. (Zongoyerekezera.)
Tsamba 182 Paulo wamvera zimene akulu amupempha. Luka ndi Timoteyo akhala pansi chakumbuyoko, ndipo akukonzekera kukagawa zopereka.
Tsamba 190 Mwana wa mlongo wake wa Paulo akulankhula ndi Kalaudiyo Lusiya mu Nsanja ya Antoniya kumene mwina Paulo anaikidwa m’ndende. Kachisi wa Herode akuoneka chakumbuyoko.
Tsamba 206 Paulo akupempherera anthu otopa apaulendo amene anakwera ngalawa yonyamula katundu.
Tsamba 222 Paulo ali mkaidi ndipo amumangirira kwa msilikali wachiroma. Iwo akuyang’ana mbali ina ya mzinda wa Roma.