Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 4 • MACHITIDWE 13:1–14:28

“Anatumizidwa ndi Mzimu Woyera”

“Anatumizidwa ndi Mzimu Woyera”

MACHITIDWE 13:4

M’gawoli, tiyendera limodzi ndi mtumwi Paulo pa ulendo wake woyamba waumishonale. Mtumwiyu anazunzidwa m’mizinda yosiyanasiyana, komabe motsogoleredwa ndi mzimu woyera, iye anapitiriza kuchitira umboni ndi kukhazikitsa mipingo yatsopano. Sitikukayikira kuti nkhani yosangalatsayi itithandiza kuti tizichita utumiki wathu mwakhama.