Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 9

“Mulungu Alibe Tsankho”

“Mulungu Alibe Tsankho”

Akhristu anayamba kulalikira kwa anthu osadulidwa a mitundu ina

Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 10:1–11:30

1-3. Kodi Petulo anaona masomphenya otani, nanga kumvetsa tanthauzo lake n’kofunika bwanji?

 TSIKU lina masana m’nthawi ya chilimwe m’chaka cha 36 C.E., Petulo ankapemphera ali padenga lafulati la nyumba ina imene inali m’mbali mwa nyanja mumzinda wa Yopa. Kwa masiku angapo, iye anali mlendo panyumba imeneyi, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti analibe mtima wa tsankho. Mwiniwake wa nyumbayo anali Simoni ndipo ntchito yake inali yofufuta zikopa. Ayuda ena sakanalola kuti akhale panyumba ya munthu wofufuta zikopa. a Komabe, Petulo anali atatsala pang’ono kuphunzira mfundo yofunika kwambiri pa nkhani yoti Yehova ndi wopanda tsankho.

2 Petulo ali mkati mopemphera, anayamba kuona masomphenya. Zimene anaona m’masomphenyawo zikanasokoneza maganizo Myuda aliyense. Iye anaona chinthu chooneka ngati chinsalu chachikulu chikutsika kumwamba ndipo pachinthu chimenecho panali nyama zimene Chilamulo chinkati ndi zodetsedwa. Petulo atauzidwa kuti aphe ndi kudya nyamazo, anayankha kuti: “Sindinadyepo chinthu chodetsedwa ndiponso chonyansa chilichonse.” Koma iye anauzidwa katatu konse kuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa, usiyiretu kunena kuti n’zodetsedwa.” (Mac. 10:14-16) Petulo anasokonezeka kwambiri maganizo ndi masomphenyawa, koma pasanapite nthawi anadziwa tanthauzo lake.

3 Kodi masomphenya amene Petulo anaonawa ankatanthauza chiyani? Kumvetsa tanthauzo la masomphenyawa n’kofunika kwambiri chifukwa kungatithandize kudziwa mmene Yehova amaonera anthu. Monga Akhristu oona, tingakwanitse kuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu ngati titaphunzira kuona anthu mmene Mulungu amawaonera. Kuti tidziwe tanthauzo la masomphenya amene Petulo anaona, tiyeni tione kaye mmene zinthu zinalili pa nthawiyo.

“Ankapemphera Mochonderera kwa Mulungu Nthawi Zonse” (Machitidwe 10:1-8)

4, 5. Kodi Koneliyo anali ndani, nanga n’chiyani chinachitika pamene ankapemphera?

4 Petulo sanadziwe kuti dzulo lake, Koneliyo yemwe ankakhala ku Kaisareya, dera limene linali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 50 kumpoto kwa mzinda wa Yopa, anaonanso masomphenya ochokera kwa Mulungu. Koneliyo, amene anali mtsogoleri wa asilikali a Chiroma, “ankakonda zopemphera.” b Iye analinso chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosamalira banja chifukwa “ankaopa Mulungu pamodzi ndi banja lake lonse.” Koneliyo anali munthu wosadulidwa wa mtundu wina komanso sanalowe Chiyuda. Komabe, iye ankachitira chifundo Ayuda osauka ndipo ankawapatsa ndalama kapena mphatso zina. Munthu woona mtimayu “ankapemphera mochonderera kwa Mulungu nthawi zonse.”​—Mac. 10:2.

5 Pa nthawi ina Koneliyo akupemphera cha m’ma 3 koloko masana, anaona masomphenya. M’masomphenyawo, mngelo anamuuza kuti: “Mulungu wamva mapemphero ako ndiponso waona mphatso zako zachifundo.” (Mac. 10:4) Atauzidwa ndi mngeloyo, Koneliyo anatumiza anthu kuti akaitane mtumwi Petulo. Koneliyo anali atatsala pang’ono kukhala Mkhristu woyamba wochokera kwa anthu a mitundu ina.

6, 7. (a) Fotokozani chitsanzo chosonyeza kuti Mulungu amayankha mapemphero a anthu amene akufuna kudziwa zoona zenizeni zokhudza iyeyo. (b) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zochitika ngati zimenezi?

6 Kodi masiku ano Mulungu amayankha mapemphero a anthu oona mtima amene amafuna kudziwa zoona zenizeni zokhudza iyeyo? Kuti tidziwe yankho la funsoli, tiyeni tione zimene zinachitikira mayi wina wa ku Albania. Tsiku lina a Mboni anafika panyumba ya mayiyu ndipo anamupatsa magazini ya Nsanja ya Olonda imene inali ndi nkhani yokhudza kulera ana. c Atalandira magaziniyo, anauza a Mboniwo kuti: “Simungakhulupirire kuti posachedwapa ndimapemphera kuti Mulungu andithandize kulera bwino ana anga aakazi. Ndikuona kuti Mulungu ndi amene wakutumizani kwa ine. Magazini imene mwandipatsayi ili ndi nkhani yomwe ndimafunikiradi.” Mayiyo pamodzi ndi ana akewo anayamba kuphunzira Baibulo ndipo kenako mwamuna wake nayenso anayamba kuphunzira nawo.

7 Kodi zinthu ngati zimenezi zinangochitikira mayi yekhayu? Ayi. Zinthu ngati zimenezi zakhala zikuchitika kwa anthu osiyanasiyana padziko lonse, ndipo n’zoonekeratu kuti sizichitika mwamwayi. Ndiye kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Choyamba, Yehova amayankha mapemphero a anthu amene amafunitsitsa kuti aphunzire za iye. (1 Maf. 8:41-43; Sal. 65:2) Chachiwiri, angelo amatithandiza tikamagwira ntchito yolalikira.​—Chiv. 14:6, 7.

‘Petulo Anathedwa Nzeru’ (Machitidwe 10:9-23a)

8, 9. Kodi Mulungu anauza chiyani Petulo kudzera mwa mzimu wake woyera, nanga iye anatani?

8 Pamene anthu amene anatumidwa ndi Koneliyo anafika panyumbayo, Petulo anali asanatsike padenga paja ndipo anali “atathedwa nzeru” chifukwa sankadziwa tanthauzo la masomphenyawo. (Mac. 10:17) Kodi Petulo, amene anakana katatu konse kuti sangadye chakudya chodetsedwa malinga ndi Chilamulo, akanalolera kupita ndi anthu amenewa n’kukalowa m’nyumba ya munthu yemwe sanali Myuda? Mwanjira inayake, Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera pothandiza Petulo kudziwa maganizo ake pa nkhaniyi. Iye anauzidwa kuti: “Petulo! Pali anthu atatu amene akukufuna. Ndiye konzeka, tsika upite nawo limodzi. Usakayikire, chifukwa ndawatuma ndine.” (Mac. 10:19, 20) N’zosakayikitsa kuti masomphenya a nyama zodetsedwa amene Petulo anaona anamuthandiza kulolera kuti mzimu woyera umutsogolere.

9 Petulo atadziwa kuti Koneliyo anauzidwa ndi Mulungu kuti atumize anthuwo kukamuitana, analandira anthu a mtundu winawo n’kuwauza kuti alowe m’nyumba, ndipo ‘anawasamalira monga alendo ake.’ (Mac. 10:23a) Mtumwiyu, yemwe anali ndi mtima womvera, anali atayamba kale kusintha maganizo chifukwa cha masomphenyawo kuti agwirizane ndi zimene Mulungu ankafuna.

10. Kodi Yehova amatsogolera bwanji anthu ake, nanga tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

10 Masiku anonso, Yehova amatsogolera anthu ake powaululira zinthu pang’onopang’ono. (Miy. 4:18) Pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera, iye akutsogolera “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru.” (Mat. 24:45) Nthawi zina timalandira mfundo zofotokoza kusintha kwa kayendetsedwe ka gulu kapena kusintha kwa mmene timamvera Mawu a Mulungu. Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimatani ndikamva za kusinthako? Kodi ndimasonyeza kugonjera pololera kutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu pa nkhani ngati zimenezi?’

Petulo “Anawalamula Kuti Abatizidwe” (Machitidwe 10:23b-48)

11, 12. Kodi Petulo anachita chiyani atafika ku Kaisareya, nanga iye anazindikira chiyani?

11 Patapita tsiku limodzi ataona masomphenyawo, Petulo limodzi ndi anthu ena 9 anayamba ulendo wopita ku Kaisareya kuchoka ku Yopa. Atatu mwa anthuwo anali amuna amene anatumidwa ndi Koneliyo, ndipo enawo anali “abale 6” a Chiyuda. (Mac. 11:12) Poyembekezera kuti Petulo afike, Koneliyo anasonkhanitsa “achibale ndi anzake apamtima,” omwe n’kutheka kuti onse sanali Ayuda. (Mac. 10:24) Atafika, Petulo anachita chinthu china chimene anali asanaganizepo kuti angachite. Iye analowa m’nyumba ya munthu wa mtundu wina amene anali wosadulidwa. Petulo ananena kuti: “Inunso mukudziwa bwino kuti si zololeka kuti Myuda azicheza ndi munthu wa mtundu wina kapena kumuyandikira. Koma Mulungu wandionetsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti wodetsedwa kapena wonyansa.” (Mac. 10:28) Pa nthawiyi, Petulo anazindikira kuti masomphenya amene anaonawo sanali chabe okhudza mitundu ya zakudya zimene munthu ayenera kudya. Koma anaona kuti sayenera ‘kutchula munthu aliyense [ngakhale wa mtundu wina] kuti ndi wodetsedwa.’

“Koneliyo ankawayembekezeradi. Iye anali atasonkhanitsa achibale ake ndi anzake apamtima.”​—Machitidwe 10:24

12 Anthu onse amene anasonkhanawo anali ndi chidwi choti amve zimene Petulo anganene. Ndiyeno Koneliyo ananena kuti: “Tonse tili pano pamaso pa Mulungu, kuti timve zonse zimene Yehova wakulamulani kuti mutiuze.” (Mac. 10:33) Tangoganizani mmene mungasangalalire munthu amene akufuna kuphunzira za Yehova atakuuzani mawu amenewa. Poyamba kulankhula, Petulo ananena mawu ogwira mtima akuti: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Mac. 10:34, 35) Petulo anali atazindikira kuti Mulungu sakondera anthu potengera mtundu, fuko kapena maonekedwe awo. Kenako Petulo anapitiriza kuchitira umboni pofotokoza za utumiki wa Yesu, imfa yake ndiponso kuukitsidwa kwake.

13, 14. (a) Kodi Mulungu anasonyeza chiyani chokhudza ubwenzi wake ndi Ayuda atavomereza Koneliyo ndiponso anthu a mitundu ina mu 36 C.E.? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuweruza anthu chifukwa cha maonekedwe awo?

13 Ndiyeno panachitika chinthu china chodabwitsa. Nkhaniyi imati: “Pamene Petulo ankalankhula,” ‘anthu a mitundu inawo’ analandira mzimu woyera. (Mac. 10:44, 45) Awa ndi malo amodzi okha m’Malemba amene amasonyeza kuti anthu analandira mzimu woyera asanabatizidwe. Petulo anazindikira kuti zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu walandira anthu a mitundu inawo kuti azimulambira, choncho iye “anawalamula kuti abatizidwe.” (Mac. 10:48) Mulungu atavomereza anthuwo mu 36 C.E., zinasonyeza kuti wasiya kuona Ayuda ngati mtundu wake wapadera. (Dan. 9:24-27) Potsogolera ntchito yochitira umboni pa tsikuli, Petulo anagwiritsa ntchito kiyi wachitatu yemwenso anali womaliza pa “makiyi a Ufumu.” (Mat. 16:19) Kiyi ameneyu anatsegula mwayi woti anthu osadulidwa a mitundu ina akhale m’gulu la Akhristu odzozedwa ndi mzimu.

14 Ifenso amene tikulengeza uthenga wa Ufumu masiku ano timadziwa kuti “Mulungu alibe tsankho.” (Aroma 2:11) Iye amafuna kuti “anthu osiyanasiyana apulumuke.” (1 Tim. 2:4) Choncho, tisamaweruze anthu chifukwa cha maonekedwe awo. Ntchito yathu ndi yochitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu ndipo zimenezi zikutanthauza kulalikira kwa anthu onse mosayang’ana mtundu, fuko, maonekedwe kapena chipembedzo chawo.

Iwo “Anasiya Kumutsutsa, Ndipo Anatamanda Mulungu” (Machitidwe 11:1-18)

15, 16. N’chifukwa chiyani Akhristu ena a Chiyuda anayamba kutsutsana ndi Petulo, nanga iye anawauza zifukwa ziti?

15 Petulo ananyamuka kupita ku Yerusalemu chifukwa ankafunitsitsa kuti akafotokoze zimene zinachitikazo. Zikuoneka kuti iye asanafike ku Yerusalemu, anthu anali atamva kale kuti anthu osadulidwa a mitundu ina “alandira mawu a Mulungu.” Petulo atangofika, “anthu olimbikitsa mdulidwe anayamba kumuimba mlandu.” Iwo sanasangalale chifukwa iye anakalowa ‘m’nyumba ya anthu osadulidwa ndipo anadya nawo.’ (Mac. 11:1-3) Sanakhumudwe chifukwa choti anthu a mitundu ina akhala Akhristu, koma ankaumirira kuti anthu a mitundu inawo azitsatiranso Chilamulo kuphatikizapo kudulidwa kuti azilambira Yehova m’njira yovomerezeka. N’zoonekeratu kuti Akhristu ena a Chiyuda anavutika kuvomereza kuti Chilamulo cha Mose sichinkagwiranso ntchito.

16 Kodi Petulo anawafotokozera zifukwa zotani zimene zinam’chititsa kuti abatize anthu a mitundu inawo? Mogwirizana ndi Machitidwe 11:4-16, iye anawauza mfundo 4 zotsimikizira kuti Mulungu ndi amene ankamutsogolera: (1) anafotokoza za masomphenya amene anaona (Vesi 4-10); (2) zimene mzimu unamulamula kuti achite (Vesi 11 ndi 12); (3) anafotokoza kuti mngelo anaonekera kwa Koneliyo (Vesi 13 ndi 14); komanso (4) kuti anthu a mitundu ina analandira mzimu woyera. (Vesi 15 ndi 16) Pomaliza, Petulo anawafunsa funso lamphamvu lakuti: “Choncho ngati Mulungu anawapatsa [anthu a mitundu ina okhulupirira] mphatso yaulere [ya mzimu woyera] yomwenso anatipatsa ifeyo amene tinakhulupirira mwa Ambuye Yesu Khristu, ndine ndani kuti ndiletse Mulungu?”​—Mac. 11:17.

17, 18. (a) Kodi zimene Petulo analankhula zinachititsa Akhristu a Chiyuda kuchita chiyani? (b) N’chifukwa chiyani nthawi zina zingakhale zovuta kuti anthu mumpingo akhalebe ogwirizana, nanga tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

17 Zimene Petulo anafotokozazi zinachititsa Akhristu a Chiyudawo kuti asankhe chochita pa nkhaniyi. Kodi iwo akanachotsa mtima wa tsankho n’kuvomereza anthu a mitundu ina amene anali atangobatizidwa kumene kukhala Akhristu anzawo? Nkhaniyi imati: “Atamva zimenezi, anasiya kumutsutsa, ndipo anatamanda Mulungu kuti: ‘Ndiye kuti Mulungu waperekanso mwayi kwa anthu a mitundu ina kuti nawonso alape n’kudzapeza moyo.’” (Mac. 11:18) Zimenezi zinathandiza kuti mpingo ukhalebe wogwirizana.

18 Masiku ano, nthawi zina zingakhale zovuta kuti anthu mumpingo akhalebe ogwirizana chifukwa olambira oona akuchokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chilankhulo chilichonse.” (Chiv. 7:9) M’mipingo yambiri muli anthu ochokera m’mitundu, m’zikhalidwe ndi m’mayiko osiyanasiyana. Choncho, tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndinachotsa maganizo a tsankho aliwonse mumtima mwanga? Popeza kuti anthu ambiri m’dzikoli amachita zinthu zogawanitsa anthu, monga kukonda kwambiri dziko lawo, mtundu wawo, chikhalidwe chawo ndiponso kusankhana mitundu, kodi ineyo ndinatsimikiza ndi mtima wonse kuti sindidzalola zinthu zimenezi kundipangitsa kuchitira abale anga a Chikhristu zinthu zosayenera?’ Kumbukirani zimene Petulo (Kefa) anachita patapita zaka zingapo kuchokera pamene anthu a mitundu ina anayamba kukhala otsatira a Khristu. Chifukwa choopa anthu ena atsankho, iye “anadzipatula” pakati pa Akhristu a mitundu ina moti anachita kudzudzulidwa ndi Paulo. (Agal. 2:11-14) Choncho, tiyeni nthawi zonse tizikhala osamala kuti tisayambe kuchita zinthu mwatsankho.

“Anthu Ambiri Anakhulupirira” (Machitidwe 11:19-26a)

19. Kodi Akhristu a Chiyuda a ku Antiokeya anayamba kulalikira kwa ndani, nanga zotsatira zake zinali zotani?

19 Kodi otsatira a Yesu anayamba kulalikira kwa anthu osadulidwa a mitundu ina? Taonani zimene zinachitika pa nthawi ina mumzinda wa Antiokeya wa ku Siriya. d Mumzinda umenewu munkakhala Ayuda ambiri, koma ankayesetsa kukhala bwino ndi anthu a mitundu ina. Zimenezi zinachititsa kuti Akhristu a ku Antiokeya asamavutike kulalikira kwa anthu a mitundu ina. Akhristu ena a Chiyuda anayambira mumzinda umenewu kulalikira uthenga wabwino “kwa anthu olankhula Chigiriki.” (Mac. 11:20) Iwo sankangolalikira kwa Ayuda olankhula Chigiriki okha, koma ankalalikiranso kwa anthu osadulidwa a mitundu ina. Yehova anadalitsa ntchitoyo ndipo anthu “ambiri anakhulupirira.”​—Mac. 11:21.

20, 21. Kodi Baranaba anasonyeza bwanji kudzichepetsa, nanga ifeyo tingam’tsanzire bwanji pochita utumiki wathu?

20 Pofuna kulalikira anthu achidwiwo, mpingo wa ku Yerusalemu unatumiza Baranaba ku Antiokeya. Anthu ambiri mumzindawu anali ndi chidwi ndi uthenga wabwino moti munthu mmodzi sakanakwanitsa kuwalalikira. Choncho, Baranaba anagwira ntchitoyi limodzi ndi Saulo amene anasankhidwa kuti akhale mtumwi wa anthu a mitundu ina. (Mac. 9:15; Aroma 1:5) Kodi Baranaba anaopa kuti Saulo achita zambiri pa ntchitoyi kuposa iyeyo? Ayi. Baranaba anasonyeza kudzichepetsa. Iye anachita kupita ku Tariso kukafunafuna Saulo, ndipo atam’peza anabwera naye ku Antiokeya kuti athandizane kugwira ntchito yolalikira. Iwo anakhala mumzindawo kwa chaka chathunthu akulimbikitsa ophunzira a mumpingo wa kumeneko.​—Mac. 11:22-26a.

21 Kodi ifeyo tingasonyeze bwanji kudzichepetsa tikamachita utumiki wathu? Munthu wodzichepetsa amazindikira zinthu zimene sangakwanitse kuchita. Tonsefe tili ndi maluso osiyanasiyana. Mwachitsanzo, ena angakhale aluso kwambiri polalikira mwamwayi kapena kunyumba ndi nyumba koma angamavutike kupanga maulendo obwereza kapena kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Ngati mukufuna kuphunzira luso linalake pochita utumiki, mungapemphe ena kuti akuthandizeni. Mutachita zimenezi, mungakhale mphunzitsi wogwira mtima ndipo mungamasangalale kwambiri mu utumiki wanu.​—1 Akor. 9:26.

‘Anatumiza Thandizo’ (Machitidwe 11:26b-30)

22, 23. Kodi abale a ku Antiokeya anachita chiyani posonyeza chikondi chenicheni, nanga masiku ano anthu a Mulungu amachita zinthu zotani zofanana ndi zimenezi?

22 Ku Antiokeya n’kumene “ophunzirawo anayamba kutchedwa Akhristu, motsogoleredwa ndi Mulungu.” (Mac. 11:26b) Dzina lovomerezedwa ndi Mulunguli, ndi loyenereradi kwa anthu amene amatsatira Khristu. Anthu a mitundu ina atayamba kukhala Akhristu, kodi Akhristu a Chiyuda ankakondana nawo? Taonani zimene zinachitika m’chaka cha 46 C.E. kutagwa njala yaikulu kwambiri. e Kale anthu osauka, amene analibe ndalama kapena chakudya chapadera, ndi amene ankavutika kwambiri kukagwa njala. Pamene kunagwa njala yaikuluyi, Akhristu a Chiyuda a ku Yudeya, amene mwina ambiri mwa iwo anali osauka, ndi omwe ankafunikira thandizo. Atamva zimenezi, abale a ku Antiokeya, omwe ena mwa iwo anali Akhristu a mitundu ina, anatumiza “thandizo kwa abale a ku Yudeya.” (Mac. 11:29) Zimenezitu zinasonyeza kuti Akhristuwo ankakondana kwambiri.

23 Masiku anonso, anthu a Mulungu timachita chimodzimodzi. Tikamva kuti abale athu m’dziko lina kapena m’dziko lathu lomweli akuvutika, timayesetsa kuwathandiza mofunitsitsa. Mofulumira, Makomiti a Nthambi amakonza zoti pakhale Makomiti Othandiza pa Ngozi za Mwadzidzidzi n’cholinga chothandiza abale athu amene akhudzidwa ndi ngozi zam’chilengedwe monga mphepo zamkuntho, zivomerezi komanso kusefukira kwa madzi. Zonsezi zimasonyeza kuti Akhristu oona ali ndi chikondi chenicheni.​—Yoh. 13:34, 35; 1 Yoh. 3:17.

24. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona kuti tanthauzo la masomphenya amene Petulo anaona ndi lofunika kwambiri?

24 Akhristu oonafe masiku ano timaona kuti tanthauzo la masomphenya amene Petulo anaona ali padenga ku Yopa ndi lofunika kwambiri. Timalambira Mulungu wopanda tsankho amene akufuna kuti tichitire umboni mokwanira za Ufumu wake. Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tiyenera kulalikira anthu ena mosayang’ana ngati ali ndi chuma kapena ayi, mtundu kapena fuko lawo. Choncho, tiyeni tizigwira ndi mtima wonse ntchito yolalikira kuti anthu onse amene akufuna kuphunzira za Mulungu akhale ndi mwayi womva nawo uthenga wabwino.​—Aroma 10:11-13.

Abale athu akakhala pa mavuto timayesetsa kuwathandiza

a Ayuda ena ankadana ndi anthu ofufuta zikopa chifukwa ntchitoyi inkawachititsa kuti azigwira zikopa, nyama zakufa komanso ankagwiritsa ntchito zinthu zina zonyansa pogwira ntchitoyi. Anthu ofufuta zikopa ankaonedwa kuti ndi osayenera kufika pakachisi, ndipo malo awo ogwirira ntchito ankafunika kukhala kunja kwa mzinda pa mtunda pafupifupi mamita 20. Mwina chimenechi chinali chimodzi mwa zifukwa zimene zinachititsa kuti nyumba ya Simoni ikhale “m’mbali mwa nyanja.”​—Mac. 10:6.

b Onani bokosi lakuti “ Koneliyo Ndiponso Gulu la Asilikali a Roma.”

d Onani bokosi lakuti “ Antiokeya wa ku Siriya,” patsamba 73.

e Myuda wina dzina lake Josephus, yemwe anali katswiri wa mbiri yakale ananena kuti “njala yaikulu” imeneyi inachitika mu ulamuliro wa Mfumu Kalaudiyo (41-54 C.E.).