Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 3

“Anadzazidwa ndi Mzimu Woyera”

“Anadzazidwa ndi Mzimu Woyera”

Zimene zinachitika ophunzira a Yesu atalandira mzimu woyera pa Pentekosite

Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 2:1-47

1. Fotokozani mmene zinthu zinkakhalira pa Chikondwerero cha Pentekosite.

 TSIKU lina, anthu anali akuyendayenda m’misewu ya ku Yerusalemu, uku akusangalala. a Kukachisi kunkaoneka utsi wochokera paguwa lansembe ndipo Alevi ankaimba nyimbo zotamanda Mulungu. (Salimo 113 mpaka 118 ) Poimba nyimbozi, mwina munthu mmodzi kapena angapo ankatsogolera ndipo ena onse ankayankhira. M’misewu imeneyi munalinso alendo ambiri ochokera m’madera akutali monga ku Elamu, Mesopotamiya, Kapadokiya, Ponto, Iguputo komanso Roma. b Kodi kunkachitika chiyani? Kunali Chikondwerero cha Pentekosite, chimene chimatchedwanso kuti chikondwerero cha “tsiku la zipatso zoyamba kucha.” (Num. 28:26) Chikondwerero chimenechi chinkachitika chaka ndi chaka pa nthawi imene ankamaliza kukolola balere n’kuyamba kukolola tirigu. Pa tsikuli anthu ankasangalala kwambiri.

2. Kodi pa Pentekosite mu 33 C.E. panachitika zinthu zotani?

2 Pa tsikuli kunja kunacha bwino ndipo cha m’ma 9 koloko m’mawa, kunachitika zinthu zimene zakhala zikudabwitsa anthu kwa zaka zambiri. Mwadzidzidzi, “kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu.” (Mac. 2:2) Mkokomo wamphamvuwo unadzaza m’nyumba yonse imene ophunzira a Yesu pafupifupi 120 anasonkhanamo. Kenako panachitika zozizwitsa. Panaoneka malawi amoto ooneka ngati malilime ndipo malawiwo anakhala pa aliyense wa ophunzirawo. c Zitatero ophunzirawo “anadzazidwa ndi mzimu woyera” ndipo anayamba kulankhula zilankhulo zachilendo. Ophunzirawo atatuluka m’nyumbamo, anakumana ndi alendo aja m’misewu ya mu Yerusalemu ndipo alendowo anadabwa kwambiri chifukwa chakuti ophunzirawo ankatha kulankhula nawo m’zilankhulo za kwawo. Ndithudi, aliyense wa iwo anawamva “akulankhula m’chilankhulo chake.”​—Mac. 2:1-6.

3. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti pa Pentekosite mu 33 C.E., panachitika zinthu zosaiwalika mu mbiri ya kulambira koona? (b) Kodi mawu a Petulo akusonyeza bwanji kuti iye anagwiritsa ntchito “makiyi a Ufumu”?

3 Nkhani yochititsa chidwiyi ikufotokoza za chinthu chinachake chofunika kwambiri chokhudza kulambira koona chimene chinachitika pa tsikuli. Chinthu chimenechi ndi kubadwa kwa mtundu wa Isiraeli wauzimu, womwe ndi mpingo wa Akhristu odzozedwa. (Agal. 6:16) Koma si zokhazi zimene zinachitika. Pamene Petulo analankhula ndi gulu la anthu pa tsikulo, iye anagwiritsa ntchito kiyi woyamba mwa “makiyi [atatu] a Ufumu.” Kiyi aliyense mwa makiyi amenewa anali woti adzatsegule mwayi woti anthu a gulu linalake adzalandire madalitso apadera. (Mat. 16:18, 19) Kiyi woyambayu anathandiza kuti Ayuda ndi anthu omwe analowa Chiyuda alandire uthenga wabwino komanso kuti adzozedwe ndi mzimu woyera wa Mulungu. d Choncho iwo anakhala mbali ya Isiraeli wauzimu ndipo zimenezi zinawathandiza kukhala ndi chiyembekezo chodzalamulira monga mafumu ndi ansembe mu Ufumu wa Mesiya. (Chiv. 5:9, 10) Patapita nthawi Asamariya kenako anthu a mitundu ina anapatsidwanso mwayi umenewu. Kodi Akhristu masiku ano angaphunzire chiyani pa zinthu zosaiwalika zimene zinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E.?

“Onse Anali Atasonkhana Pamodzi” (Machitidwe 2:1-4)

4. Kodi mpingo wa Chikhristu masiku ano ukugwirizana bwanji ndi mpingo umene unayamba pa Pentekosite mu 33 C.E.?

4 Mpingo wa Chikhristu unayamba ndi ophunzira pafupifupi 120 amene “anali atasonkhana pamodzi” m’chipinda cham’mwamba ndipo anadzozedwa ndi mzimu woyera. (Mac. 2:1) Pofika madzulo tsiku limenelo, anthu masauzande anabatizidwa. Uku kunali kuyamba chabe kwa kukula kwa gulu limene likupitirizabe kukula mpaka pano. Gulu la amuna ndi akazi oopa Mulungu, amene ndi mpingo wa Chikhristu masiku ano, ndi limene likulalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse,’ mapeto a dzikoli asanafike.​—Mat. 24:14.

5. Kuyambira m’nthawi ya atumwi mpaka masiku ano, kodi Akhristu amapeza madalitso otani akamasonkhana ndi mpingo wa Chikhristu?

5 Mpingo wa Chikhristu unathandiza kuti anthu a mumpingowo, odzozedwa komanso pambuyo pake Akhristu a “nkhosa zina,” azilimbikitsana kwambiri mwauzimu. (Yoh. 10:16) Pamene Paulo analembera Akhristu a ku Roma, anasonyeza kuti ankayamikira kwambiri zimene Akhristu ankachita pothandizana. Iye anati: “Ndikulakalaka nditakuonani kuti ndikupatseni mphatso inayake yauzimu kuti mukhale olimba, kapena kuti ndidzalimbikitsidwe ndi chikhulupiriro chanu, nanunso mudzalimbikitsidwe ndi chikhulupiriro changa.”​—Aroma 1:11, 12.

6, 7. Kodi mpingo wa Chikhristu masiku ano ukuchita zotani pokwaniritsa ntchito imene Yesu anapereka yolalikira kwa anthu a mitundu yonse?

6 Masiku anonso, mpingo wa Chikhristu uli ndi cholinga chofanana ndi chimene unali nacho m’nthawi ya atumwi. Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yovuta koma yosangalatsa. Iye anawauza kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera, ndipo muziwaphunzitsa kuti azisunga zinthu zonse zimene ndinakulamulani.”​—Mat. 28:19, 20.

7 Masiku ano, mpingo wa Chikhristu wa Mboni za Yehova ndi umene ukugwira ntchito imeneyi. N’zoona kuti nthawi zina zimakhala zovuta kulalikira kwa anthu a zilankhulo zina. Komabe, a Mboni za Yehova akufalitsa mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zilankhulo zoposa 1,000. Ngati mumapezeka pamisonkhano ya Chikhristu nthawi zonse, ndiponso ngati mukugwira nawo ntchito yolalikira za Ufumu ndi kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu, ndiye kuti muli ndi chifukwa chokhalira osangalala. Muyenera kusangalala chifukwa muli m’gulu la anthu ochepa padziko lapansi amene ali ndi mwayi wochitira umboni mokwanira za dzina la Yehova.

8. Kodi mpingo wa Chikhristu umatithandiza bwanji?

8 Pofuna kutithandiza kupirira mosangalala pa nthawi yovuta ino, Yehova Mulungu watipatsa gulu la abale lapadziko lonse. Paulo analembera Akhristu a Chiheberi kuti: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa nkhani yosonyezana chikondi ndiponso kuchita zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, ngati mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane ndipo tizichita zimenezi kwambiri, makamaka panopa pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheb. 10:24, 25) Mpingo wa Chikhristu ndi mphatso yochokera kwa Yehova yotithandiza kuti tizilimbikitsana. Choncho musatalikirane ndi abale komanso alongo anu auzimu. Musasiye kupita kumisonkhano ya Chikhristu.

“Aliyense Anawamva Akulankhula M’chilankhulo Chake” (Machitidwe 2:5-13)

“Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu m’zilankhulo zathu.”—Machitidwe 2:11

9, 10. Kodi ena achita chiyani kuti athe kulalikira anthu olankhula chilankhulo china?

9 Tangoganizani mmene Ayuda ndi anthu omwe analowa Chiyuda anasangalalira atakumana pamodzi pa Pentekosite mu 33 C.E. N’kutheka kuti ambiri mwa anthu amenewa ankadziwa chilankhulo chimodzi chofala, mwina Chigiriki kapena Chiheberi. Koma pa nthawiyi “aliyense anawamva [ophunzirawo] akulankhula m’chilankhulo chake.” (Mac. 2:6) N’zosakayikitsa kuti uthenga wabwino unawafika pamtima anthuwo chifukwa anaumva m’chilankhulo chawo. N’zoona kuti Akhristu masiku ano sanapatsidwe mphatso yolankhula zilankhulo zachilendo mozizwitsa. Komabe, ambiri adzipereka kufalitsa uthenga wa Ufumu kwa anthu a mitundu yonse. Kodi akukwanitsa bwanji zimenezi? Ena aphunzira chilankhulo china kuti azikatumikira mumpingo wa chilankhulo chimenecho kapena kuti asamukire kudziko lina. Anthu amenewa nthawi zambiri amaona kuti ena amachita nawo chidwi kwambiri chifukwa cha khama lawo.

10 Mwachitsanzo, Christine anaphunzira chilankhulo cha Chigujarati pamodzi ndi anzake ena 7 a Mboni. Tsiku lina iye atakumana ndi mtsikana wina wolankhula Chigujarati amene amagwira naye ntchito, anam’patsa moni m’chilankhulo chimenechi. Mtsikanayo anachita chidwi kwambiri ndipo anafuna kudziwa chifukwa chake Christine ankayesetsa kuphunzira Chigujarati chomwe ndi chilankhulo chovuta. Pamenepa Christine anapeza mwayi wolalikira. Kenako mtsikanayo anauza Christine kuti: “Mwayenera kukhala kuti mulidi ndi uthenga wofunika kwambiri woti muuze anthu ena.”

11. Kodi tingatani kuti tizilalikira anthu a m’zilankhulo zina?

11 N’zoona kuti si aliyense amene angaphunzire chilankhulo chatsopano. Komabe tiyenera kukhala okonzeka kulalikira kwa anthu olankhula zilankhulo zina. Tingachite bwanji zimenezi? Njira imodzi yochitira zimenezi ndi kugwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Language® kuti muphunzire kupereka moni m’chilankhulo chimene anthu ambiri m’dera lanu amalankhula. Mungaphunzirenso mawu ochepa a m’chilankhulocho amene angathandize anthuwo kukhala ndi chidwi chophunzira Baibulo. Mungawauze za webusaiti yathu ya jw.org n’kuwasonyeza mavidiyo komanso mabuku osiyanasiyana amene alipo m’chilankhulo chawo. Tikamagwiritsa ntchito zinthu zimenezi mu utumiki, tikhoza kumasangalala ngati mmene Akhristu a m’nthawi ya atumwi anasangalalira pamene anthu ochokera m’mayiko ena anadabwa kwambiri kumva uthenga wabwino “aliyense . . . m’chilankhulo chake.”

“Petulo Anaimirira” (Machitidwe 2:14-37)

12. (a) Kodi mneneri Yoweli analemba mfundo iti imene ikugwirizana ndi zimene zinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E.? (b) N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu oyambirira ankayembekezera kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yoweli?

12 “Petulo anaimirira” kuti alankhule ndi gulu la anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana. (Mac. 2:14) Iye anauza anthu onse amene ankamumvetsera kuti Mulungu ndi amene anachititsa kuti ophunzirawo azilankhula zilankhulo zosiyanasiyana mozizwitsa, pokwaniritsa ulosi wa Yoweli wakuti: “Ndidzapereka mzimu wanga kwa chamoyo chilichonse.” (Yow. 2:28) Yesu asanapite kumwamba anauza ophunzira ake kuti: “Ndidzapempha Atate ndipo adzakupatsani mthandizi wina.” Yesu ananena kuti mthandizi ameneyu ndi “mzimu.”​—Yoh. 14:16, 17.

13, 14. Kodi Petulo anachita chiyani kuti awafike pamtima anthu amene ankamumvetsera, nanga tingamutsanzire bwanji?

13 Pomaliza kulankhula ndi gulu la anthulo, Petulo ananena mawu amphamvu akuti: “Nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu kuti Yesu ameneyu, amene inu munamuphera pamtengo, Mulungu anamuika kukhala Ambuye ndi Khristu.” (Mac. 2:36) N’zoona kuti ambiri mwa anthu amene ankamvetsera Petulo kunalibe pamene Yesu ankaphedwa pamtengo wozunzikirapo. Ngakhale zinali choncho, mtundu wonsewo unali ndi mlandu wopha Yesu. Koma mungaone kuti Petulo analankhula ndi Ayuda anzakewo mwaulemu ndipo anawafika pamtima. Cholinga cha Petulo chinali kuwalimbikitsa kuti alape, osati kuwaimba mlandu. Ndiye kodi anthuwo anakhumudwa ndi zimene Petulo ananena? Ayi. M’malomwake iwo “anavutika kwambiri mumtima” ndipo anafunsa kuti: “Tichite chiyani pamenepa?” Zimene Petulo anachita polankhula nawo mwaulemu zinathandiza ambiri mwa anthuwo kuti uthengawo uwafike pamtima ndipo analapa.​—Mac. 2:37.

14 Ifenso tingathe kuwafika pamtima anthu potsanzira zimene Petulo anachita. Tikamalalikira tisamangotsutsa mfundo iliyonse yosemphana ndi Malemba imene munthu amene takumana naye mu utumiki anganene. Koma tingachite bwino kukambirana mfundo zimene tonse tingagwirizane nazo. Tikamakambirana ndi munthuyo n’kufika pa mfundo imene tonse tagwirizana, mwaluso tingakambirane naye mfundo za m’Mawu a Mulungu zogwirizana ndi nkhaniyo. Tikamafotokoza choonadi cha m’Baibulo potsanzira mmene Petulo ankaphunzitsira, anthu a mtima wabwino akhoza kumvetsera uthenga wathu.

“Aliyense Abatizidwe” (Machitidwe 2:38-47)

15. (a) Kodi Petulo analankhula mawu otani ndipo anthu anachita chiyani? (b) N’chifukwa chiyani anthu ambirimbiri amene anamva uthenga wabwino pa Pentekosite anayenerera kubatizidwa tsiku lomwelo?

15 Pa tsiku losangalatsa la Pentekosite mu 33 C.E., Petulo anauza Ayuda komanso anthu omwe analowa Chiyuda amene anamvetsera uthenga wake kuti: “Lapani, ndipo aliyense abatizidwe.” (Mac. 2:38) Choncho anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa. Mwina anabatizidwa m’madamu amene anali ku Yerusalemu kapena amene anali pafupi ndi mzindawu. e Kodi anthuwa anangothamangira kubatizidwa? Kodi nkhaniyi ikusonyeza kuti anthu amene akuphunzira kumene Baibulo ndiponso ana amene makolo awo ndi Akhristu azithamangira kubatizidwa asanakonzekere? Ayi ndithu. Kumbukirani kuti Ayuda ndiponso anthu omwe analowa Chiyuda amene anabatizidwa pa tsikuli ankaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndiponso anali mu mtundu umene unali wodzipereka kwa Yehova. Kuwonjezera apo, iwo anali atasonyeza kale kuti amakonda Mulungu chifukwa ena mwa iwo anayenda mtunda wautali kwambiri kuti akapezeke pachikondwererochi, chomwe chinkachitika chaka ndi chaka. Atavomereza mfundo za choonadi chokhudza udindo umene Yesu Khristu ali nawo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu, iwo anali okonzeka kubatizidwa kuti apitirize kutumikira Mulungu monga otsatira a Khristu.

16. Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi anasonyeza bwanji kuti anali opatsa?

16 N’zodziwikiratu kuti Yehova anadalitsa gulu la anthu amenewo. Nkhaniyo imati: “Onse amene anakhala okhulupirira ankakhala limodzi ndipo ankagawana zinthu zonse zimene anali nazo. Ankagulitsa malo awo ndi zinthu zina zimene anali nazo, n’kugawa kwa onse zimene apeza, mogwirizana ndi zimene aliyense akufunikira.” f (Mac. 2:44, 45) Akhristu onse oona ayenera kusonyeza chikondi poyesetsa kukhala opatsa potsanzira zimene ophunzirawo anachita.

17. Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti ayenerere kubatizidwa?

17 Kuti munthu adzipereke kwa Mulungu ndiponso kuti abatizidwe n’kukhala Mkhristu, amafunika kuchita zinthu zina zogwirizana ndi Malemba. Ayenera kuphunzira Mawu a Mulungu. (Yoh. 17:3) Amafunika kukhala ndi chikhulupiriro ndipo ayenera kulapa machimo amene anachita m’mbuyomu komanso kusonyeza kuti ali ndi chisoni chifukwa cha zimene ankachitazo. (Mac. 3:19) Kenako ayenera kutembenuka n’kuyamba kuchita zinthu zabwino zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Aroma 12:2; Aef. 4:23, 24) Akachita zimenezi, ayenera kudzipereka kwa Mulungu mwa kupemphera ndipo kenako angabatizidwe.​—Mat. 16:24; 1 Pet. 3:21.

18. Kodi ophunzira a Khristu omwe ndi obatizidwa ali ndi mwayi wapadera uti?

18 Kodi ndinu wophunzira wa Yesu Khristu ndipo munadzipereka kwa Mulungu komanso munabatizidwa? Ngati ndi choncho, muyenera kusangalala chifukwa mwapatsidwa mwayi wapadera. Mofanana ndi ophunzira a m’nthawi ya atumwi amene anadzazidwa ndi mzimu woyera, Yehova angakugwiritseni ntchito kwambiri kuti muchite chifuniro chake pochitira umboni mokwanira.

a Onani bokosi lakuti “ Likulu la Chiyuda Linali ku Yerusalemu,”.

c “Malilime” amenewa sanali amoto weniweni, koma anali “ooneka ngati malawi amoto.” Zimenezi zikusonyeza kuti pamene mzimu woyera unafika pa aliyense wa ophunzirawo, unkaoneka ngati moto.

e Imeneyi sinali nthawi yokhayo imene panabatizidwa anthu ambiri. Pa 7 August 1993, anthu 7,402 anabatizidwa tsiku limodzi pamsonkhano wa mayiko wa Mboni za Yehova umene unachitika mumzinda wa Kiev m’dziko la Ukraine. Anthuwo anabatizidwa m’madamu 6 ndipo ubatizo wonse unachitika kwa maola awiri ndi 15 minitsi.

f Akhristuwo anachita zimenezi kwa nthawi yochepa pofuna kuthandiza alendo amene anatsalira ku Yerusalemu kuti apitirizebe kuphunzira zina ndi zina zokhudza chikhulupiriro chawo chatsopanocho. Iwo anapereka zinthu zawo mwa kufuna kwawo chifukwa cha chikondi ndipo sitiyenera kuganiza kuti anachita zimenezi potsatira mfundo imene anthu ena amanena, yoti munthu aliyense ali ndi ufulu wogwiritsa ntchito zinthu za ena mmene akufunira.​—Mac. 5:1-4.