Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 4

“Ndi Mphamvu Zanga Zonse, Ndidzateteza Dzina Langa Loyera”​—Satana Analephera Kuthetsa Kulambira Koyera

“Ndi Mphamvu Zanga Zonse, Ndidzateteza Dzina Langa Loyera”​—Satana Analephera Kuthetsa Kulambira Koyera

EZEKIELI 39:25

MFUNDO YAIKULU: Yehova adzateteza anthu ake pa chisautso chachikulu

Yehova amakonda anthu, komabe tikuyenera kuyankha mlandu kwa iye chifukwa cha zochita zathu. Koma kodi amamva bwanji akaona anthu amene amati amamulambira akuchita zinthu zoipa? Kodi adzadziwa bwanji anthu oyenera kuwapulumutsa pa chisautso chachikulu? Nanga n’chifukwa chiyani Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi, adzaphe anthu mamiliyoni ambirimbiri?

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 15

“Ndidzathetsa Uhule Wako”

Kodi tikuphunzira chiyani tikaona mmene m’buku la Ezekieli komanso la Chivumbulutso anafotokozera mahulewa?WEB:OnSiteAdTitle“Ndidzathetsa Uhule Wako”

BOKOSI 16

“Ulembe Chizindikiro Pazipumi”

Tingaphunzire zambiri tikaona mmene anthu a m’nthawi ya Ezekieli anawaikira chizindikiro kuti apulumuke.

MUTU 17

“Ine Ndikupatsa Chilango Iwe Gogi”

Kodi Gogi wa ku Magogi, ndi ndani, nanga kodi adzalowa m’dziko liti?

MUTU 18

“Ndidzakhala ndi Mkwiyo Waukulu”

Gogi akadzaukira anthu a Mulungu, Yehova adzakwiya ndipo zimenezi zidzachititsa kuti Mulungu ateteze anthu ake.