Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 17

“Ine Ndikupatsa Chilango Iwe Gogi”

“Ine Ndikupatsa Chilango Iwe Gogi”

EZEKIELI 38:3

MFUNDO YAIKULU: Kutithandiza kuti timudziwe “Gogi” komanso “dziko” limene adzaukire

1, 2. Kodi kutsogoloku kuchitika nkhondo yaikulu iti, nanga zimenezi zikubweretsa mafunso otani? (Onani chithunzi choyambirira.)

 KWA zaka masauzande ambiri anthu akhala akuphedwa pa nkhondo kuphatikizapo nkhondo zikuluzikulu ziwiri zimene zachitika m’zaka za m’ma 1900. Koma nkhondo yaikulu kwambiri m’mbiri yonse ya anthu ichitika posachedwapa. Nkhondo imeneyi sidzakhala mkangano wa anthu chabe umene udzachititse kuti mayiko amenyane pa zifukwa zadyera. M’malomwake, nkhondo imeneyi idzakhala ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ (Chiv. 16:14) Nkhondo imeneyi idzachitika mdani akadzalowa m’dziko limene Mulungu amaliona kuti ndi lamtengo wapatali. Mdaniyo akadzachita zimenezi, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa adzasonyeza mphamvu zake zowononga m’njira yaikulu kwambiri imene sanasonyezepo padziko lonse lapansi.

2 Zimenezi zikubweretsa mafunso ena ofunika akuti: Kodi mdani ameneyu ndi ndani? Kodi adzalowa m’dziko liti? Kodi n’chifukwa chiyani adzalowe m’dziko limeneli, nanga adzalowa liti komanso adzalowa bwanji? Popeza kuti zinthu zimenezi zidzakhudza ifeyo anthu amene tikulambira Mulungu woona padziko lapansi, tikuyenera kudziwa mayankho a mafunso amenewa. Tingapeze mayankho mu ulosi wochititsa chidwi umene ukupezeka m’buku la Ezekieli chaputala 38 ndi 39.

Mdani Wathu ndi Gogi wa ku Magogi

3. Fotokozani mfundo yaikulu ya ulosi wa Ezekieli wokhudza Gogi wa ku Magogi.

 3 Werengani Ezekieli 38:1, 2, 8, 18; 39:4, 11. Mfundo zikuluzikulu za ulosiwu ndi izi: “Pakadzapita zaka zambiri,” mdani wotchedwa “Gogi wa . . . Magogi,” adzalowa “m’dziko” la anthu a Mulungu. Koma mdaniyo akadzaukira anthu a Yehova mwankhaza, Yehova adzakhala ndi “mkwiyo waukulu,” ndipo adzalowererapo n’kugonjetsa Gogi. a Yehova akadzagonjetsa mdaniyu komanso onse amene ali kumbali yake, adzawapereka ‘kwa mbalame zamitundumitundu zodya nyama ndi zilombo zakutchire kuti zikhale chakudya chawo.’ Pamapeto pake, Yehova adzapatsa Gogi “malo kuti akhale manda ake.” Kuti timvetse mmene ulosi umenewu udzakwaniritsidwire, choyamba tikuyenera kudziwa kuti Gogi ameneyu ndi ndani?

4. Kodi tikuphunzira zotani zokhudza Gogi wa ku Magogi?

4 Ndiye kodi Gogi wa ku Magogi ndi ndani? Malinga ndi zimene Ezekieli anafotokoza, tinganene kuti Gogi ndi mdani wamkulu wa anthu amene akulambira Mulungu woona. Kodi Gogi ndi dzina lina la Satana amene ndi mdani wamkulu wa anthu onse amene akulambira Mulungu woona? Kwa zaka zambiri, izi ndi zimene mabuku athu akhala akunena. Koma titaphunziranso mozama ulosi wa Ezekieli, taona kuti m’pofunika kusintha zimene timakhulupirira. Nsanja ya Olonda inanena kuti dzina lakuti Gogi wa ku Magogi silikunena za cholengedwa chosaoneka chauzimu koma likunena za anthu amene amadana ndi anthu a Mulungu kapena kuti mgwirizano wa mayiko amene adzalimbane ndi kulambira koyera. b Tisanakambirane chifukwa chake tikunena zimenezi, choyamba tiyeni tione zifukwa ziwiri kuchokera mu ulosi wa Ezekieli zimene zikusonyeza kuti Gogi si cholengedwa chauzimu.

5, 6. Kodi n’chiyani mu ulosi wa Ezekieli chimene chikusonyeza kuti Gogi wa ku Magogi si cholengedwa chauzimu?

5 “Ndidzakuperekani kwa mbalame zamitundumitundu zodya nyama . . . kuti mukhale chakudya chawo.” (Ezek. 39:4) Kawirikawiri Malemba amagwiritsa ntchito chitsanzo cha mbalame zimene zikudya nyama ngati chenjezo la chiweruzo cha Mulungu. Mulungu anapereka machenjezo ngati amenewa kwa mtundu wa Isiraeli komanso kwa mitundu ina. (Deut. 28:26; Yer. 7:33; Ezek. 29:3, 5) Koma tingaone kuti machenjezo a Mulunguwa sanaperekedwe kwa zolengedwa zauzimu koma kwa anthu amene ali ndi mnofu komanso magazi. Ndipotu mbalame komanso zilombo zakutchire ndi zimene zimadya nyama osati zolengedwa zauzimu. Choncho chenjezo la Mulungu limene lili mu ulosi wa Ezekieli likusonyeza kuti Gogi si cholengedwa chauzimu.

6 “Gogi ndidzamupatsa malo kuti akhale manda ake ku Isiraeli.” (Ezek. 39:11) Malemba sanena kuti zolengedwa zauzimu zimaikidwa m’manda padziko lapansi. M’malomwake amanena kuti Satana ndi ziwanda zake adzatsekeredwa kuphompho kwa zaka 1,000 ndipo pambuyo pake adzaponyedwa m’nyanja yamoto yophiphiritsa imene ikuimira chiwonongeko chamuyaya. (Luka 8:31; Chiv. 20:1-3, 10) Popeza kuti Baibulo likunena kuti Gogi adzapatsidwa “malo kuti akhale manda ake” padziko lapansi, tinganene kuti Gogi si cholengedwa chauzimu.

7, 8. Kodi “mfumu yakumpoto” idzawonongedwa liti, nanga kodi zimenezi zikufanana bwanji ndi zimene zidzachitikire Gogi wa ku Magogi?

7 Ndiye ngati Gogi si cholengedwa chauzimu, kodi mdani ameneyu amene adzaukire komaliza anthu amene akulambira Mulungu woona ndi ndani? Tiyeni tione maulosi awiri a m’Baibulo amene angatithandize kumudziwa Gogi wa ku Magogi.

8 “Mfumu yakumpoto.” (Werengani Danieli 11:40-45.) Danieli analosera kuti padzakhala maulamuliro amphamvu padziko lonse kuyambira m’nthawi yake mpaka m’nthawi yathu ino. Ulosiwu umatchulanso “mfumu yakum’mwera” ndi “mfumu yakumpoto” omwe ndi adani amene akulimbana pandale. Kwa zaka zambiri, mafumu amenewa akhala akusintha chifukwa chakuti mayiko ambiri padziko lapansili akhala akulimbirana kutchuka. Ponena zimene mfumu yakumpoto idzachite “mu nthawi yamapeto,” Danieli ananena kuti: “Idzapita ndi mkwiyo waukulu kukafafaniza ndi kuwononga ambiri.” Kwenikweni mfumu yakumpotoyi idzaukira anthu amene akulambira Yehova. c Koma mofanana ndi Gogi wa ku Magogi, mfumu yakumpotoyi idzawonongedwa italephera kukwaniritsa cholinga chake poukira anthu a Mulungu.

9. Kodi zimene zichitikire Gogi wa ku Magogi zikufanana bwanji ndi zimene zidzachitikire “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu”?

9 “Mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Werengani Chivumbulutso 16:14, 16; 17:14; 19:19, 20.) Buku la Chivumbulutso linalosera kuti “mafumu a dziko lonse lapansi” adzaukira “Mfumu ya mafumu,” yemwe ndi Yesu amene ali kumwamba. Koma mafumuwa sangathe kuukira Yesu chifukwa choti ali kumwamba. M’malomwake adzaukira anthu amene ali kumbali ya Ufumu wa Mulungu padziko lapansi. Kenako mafumu a dziko lonse lapansi adzagonjetsedwa pa nkhondo ya Aramagedo. Onani kuti mafumuwa adzawonongedwa pambuyo poukira anthu a Yehova. Izi zikufanana ndi zimene zidzachitikire Gogi wa ku Magogi. d

10. Kodi tinganene kuti Gogi wa ku Magogi ndi ndani?

10 Malinga ndi zimene takambiranazi, kodi tinganene kuti Gogi ndi ndani? Choyamba, Gogi si cholengedwa chauzimu. Chachiwiri, Gogi akuimira mayiko a padziko lapansi amene adzaukire anthu a Mulungu m’tsogolomu. Mosakayikira mayiko amenewa adzapanga mgwirizano, kutanthauza kuti adzapanga gulu limodzi. Chifukwa chiyani? Popeza kuti anthu a Mulungu akupezeka padziko lonse lapansi, mayikowa akuyenera kukhala ndi cholinga chimodzi komanso kudzachita zinthu zofanana kuti akwanitse kuukira anthu a Mulunguwa. (Mat. 24:9) Ngakhale kuti mayikowa ndi amene adzaukire anthu a Mulungu, Satana ndi amene azidzatsogolera zochita za mayikowa. Kwa nthawi yaitali, Satana wakhala akulimbikitsa mayiko a m’dzikoli kuti azitsutsa kulambira koona. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:17) Koma mawu a ulosi amene Ezekieli ananena okhudza Gogi wa ku Magogi, akufotokoza zimene mayiko a padziko lapansi adzachite poukira anthu a Yehova. e

Kodi “Dziko” Lake ndi Liti?

11. Kodi ulosi wa Ezekieli umafotokoza bwanji “dziko” limene Gogi adzalowe?

11 Monga taonera  m’ndime 3, Gogi wa ku Magogi adzachititsa kuti Yehova akhale ndi mkwiyo waukulu akadzalowa m’dziko limene ndi lamtengo wapatali kwa Yehova. Kodi dziko limeneli ndi liti? Tiyeni tionenso ulosi wa Ezekieli. (Werengani Ezekieli 38:8-12.) Ulosiwo ukunena kuti Gogi ‘adzalowa mʼdziko la anthu amene anabwerera kwawo’ ndipo “anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera kumitundu ina ya anthu.” Onaninso zimene ulosiwu ukunena zokhudza anthu amene anabwerera kwawowa ndipo akukhala m’dzikoli. Ulosiwu ukunena kuti: Iwo “akukhala mʼdzikoli motetezeka,” midzi yawo ndi “yopanda mipanda ndipo alibe zotsekera ndiponso mageti,” ndipo “akusonkhanitsa chuma.” Limeneli ndi dziko limene anthu olambira Yehova padziko lonse lapansi akukhalamo. Kodi tingalidziwe bwanji dzikoli?

12. Kodi ndi kubwezeretsa kotani kumene kunachitika kalekale m’dziko la Isiraeli?

12 Tingachite bwino kuganizira za kubwezeretsa kumene kunachitika mu Isiraeli wakale, dziko limene anthu osankhidwa a Mulungu ankakhala, kugwiramo ntchito komanso kulambiriramo kwa zaka zambiri. Aisiraeli atasonyeza kusakhulupirika, Yehova kudzera mwa Ezekieli, ananeneratu kuti dziko lawo lidzawonongedwa ndipo lidzakhala bwinja. (Ezek. 33:27-29) Koma Yehova analoseranso kuti Ayuda otsala adzabwerera kudziko lakwawo kuchoka ku Babulo ndipo adzabwezeretsa kulambira koyera m’dziko lawo. Mothandizidwa ndi Yehova, dziko la Isiraeli likanasintha n’kukhala lokongola ngati “munda wa Edeni.” (Ezek. 36:34-36) Kubwezeretsa kumeneku kunachitika kuyambira mu 537 B.C.E., pamene Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo anabwezeretsa kulambira koyera m’dziko lawo lokondedwa.

13, 14. (a) Kodi paradaiso wauzimu ndi chiyani? (b) N’chifukwa chiyani paradaisoyu ndi wamtengo wapatali kwa Yehova?

13 Masiku ano anthu amene akulambira Mulungu woona akukumananso ndi kubwezeretsa kofanana ndi kumeneku. Mogwirizana ndi zimene tinaphunzira m’Mutu 9 wa buku lino, pofika mu 1919 anthu a Mulungu anali atamasulidwa mu ukapolo wa Babulo Wamkulu kumene anakhalako zaka zambiri. M’chaka chimenechi, Yehova anabwezeretsa anthu ake m’dziko lophiphiritsira. Dziko limeneli ndi paradaiso wauzimu. Zimenezi zikutanthauza kuti anayamba kulambira Yehova m’njira yovomerezeka komanso anadzipereka kuti azilambira iye yekha monga Mulungu woona. Kungoyambira nthawi imeneyo, anthu a Mulungu zinthu zakhala zikuwayendera bwino ndipo akukhala mogwirizana komanso mwamtendere. (Miy. 1:33) Timalandira chakudya chauzimu chochuluka ndipo tili ndi ntchito yambiri yosangalatsa yolalikira za Ufumu wa Mulungu. Kunena zoona, timaona kuti mwambi wopezeka pa Miyambo 10:22 ndi woona. Mwambiwu umati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa munthu, ndipo popereka madalitsowa Mulungu sawonjezerapo ululu.” Kulikonse kumene tingakhale m’dziko lapansili, tili m’dziko limeneli lomwe ndi paradaiso wauzimu. Zimenezi zili choncho ngati tikulimbikitsa nawo kulambira koyera m’mawu athu komanso m’zochita zathu.

14 Paradaiso wauzimu ameneyu ndi wamtengo wapatali kwa Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Yehova amaona kuti anthu amene ali m’dziko limeneli ndi “zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu,” anthu amene anawakoka yekha kuti ayambe kulambira koyera. (Hag. 2:7; Yoh. 6:44) Anthuwa akuyesetsa kuvala umunthu watsopano umene umasonyeza makhalidwe apamwamba a Mulungu. (Aef. 4:23, 24; 5:1, 2) Popeza kuti akulambira Mulungu woona, iwo amamutumikira modzipereka ndi mtima wawo wonse ndipo amachita zimenezi kuti amulemekeze komanso kusonyeza kuti amamukonda. (Aroma 12:1, 2; 1 Yoh. 5:3) N’zodziwikiratu kuti Yehova amasangalala kwambiri akamaona anthu amene amamulambira akugwira ntchito mwakhama kukongoletsa paradaiso wauzimu. Tangoganizani: Mukamaika kulambira koyera pamalo oyamba pa moyo wanu, mudzathandiza kuti paradaiso wauzimu akhale wokongola kwambiri komanso mudzasangalatsa mtima wa Yehova.​—Miy. 27:11.

Kulikonse kumene tili, ngati tikulimbikitsa kulambira koyera ndiye kuti tili m’paradaiso wauzimu (Onani ndime 13, 14)

N’chifukwa Chiyani Gogi Adzalowe M’dziko Lauzimu, Nanga Adzalowamo Liti Ndipo Adzalowamo Bwanji?

15, 16. Kodi Gogi wa ku Magogi adzalowa liti m’paradaiso wathu wobwezeretsedwa?

15 N’zochititsa mantha tikaganizira kuti mayiko a padziko lapansi adzagwirizana n’kulowa m’dziko lathu lauzimu lomwe ndi lamtengo wapatali. Popeza kuti anthu onse amene akulambira Yehova m’njira yovomerezeka adzakhudzidwa ndi kuukira kumeneku, tikufunitsitsa kudziwa zambiri zokhudza nkhaniyi. Tiyeni tikambirane mafunso atatu amene tingakhale nawo.

16 Kodi Gogi wa ku Magogi adzalowa liti m’dziko lathu lauzimu lobwezeretsedwa? Ulosiwu ukuyankha kuti: ‘Pakadzapita zaka zambiri, adzalowa mʼdziko.’ (Ezek. 38:8) Zimenezi zikusonyeza kuti adzalowa m’dzikoli chakumapeto kwa dziko loipali. Kumbukirani kuti chisautso chachikulu chidzayamba ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zabodza. Mabungwe onse a zipembedzo zabodza akadzawonongedwa koma nkhondo ya Aramagedo isanayambike, Gogi adzaukira komaliza anthu amene akulambira Mulungu woona.

17, 18. Kodi Yehova adzayendetsa bwanji zinthu pa chisautso chachikulu?

17 N’chifukwa chiyani Gogi adzalowe m’dziko lobwezeretsedwa la anthu omwe akulambira Yehova movomerezeka? Ulosi wa Ezekieli ukusonyeza zifukwa ziwiri. Choyamba, Yehova ndi amene adzachititse zimenezi ndipo chachiwiri, ndi zolinga zoipa za Gogi.

18 Yehova ndi amene adzachititse zimenezi. (Werengani Ezekieli 38:4, 16.) Taonani zimene Yehova akuuza Gogi. Iye akuti: ‘Ine ndidzakukola chibwano ndi ngowe’ komanso “ndidzakubweretsa kuti uukire dziko langa.” Kodi mawu amenewa akutanthauza kuti Yehova adzakakamiza mayiko kuti aukire anthu amene akumulambira? Ayi si choncho. Iye sangachititse kuti anthu ake akumane ndi mavuto. (Yobu 34:12) Koma Yehova amawadziwa bwino adani ake. Amadziwa kuti adzadana ndi anthu amene amamulambira m’njira yovomerezeka ndipo akadzapeza mwayi woti awawononge, adzaugwiritsa ntchito. (1 Yoh. 3:13) Yehova adzapangitsa kuti zinthu zina zichitike mogwirizana ndi chifuniro chake komanso nthawi yake ndipo zimenezi zidzakhala ngati wakola chibwano cha Gogi ndi ngowe n’kumamukoka. Pa nthawi ina, Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, Yehova angadzachititse mwa njira inayake kuti mayiko achite zimene zili kale mumtima mwawo. Pamenepo zidzakhala ngati watsegula njira kuti anthu ake aukiridwe ndipo zotsatira zake zidzakhala nkhondo ya Aramagedo, yomwe idzakhala yayikulu kwambiri padziko lonse. Pa nthawi imeneyi, Mulungu adzapulumutsa anthu ake ndipo adzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira komanso adzayeretsa dzina lake.​—Ezek. 38:23.

Mayiko adzakonza zolanda kulambira koyera chifukwa choti amadana nako komanso amadana ndi anthu amene akulambira Mulungu woona

19. N’chiyani chidzapangitse Gogi kuganiza zolanda kulambira koyera?

19 Zolinga zoipa za Gogi. Mayiko adzakonza “chiwembu choipa kwambiri.” Iwo adzasonyeza mkwiyo umene akhala nawo kwa nthawi yaitali komanso chidani chawo pa anthu amene amalambira Yehova. Anthu amenewa adzaoneka ngati osatetezeka ngati kuti “akukhala mʼmidzi yopanda mipanda ndipo alibe zotsekera ndiponso mageti.” Mayikowa adzayesetsanso ‘kulanda komanso kutengako zinthu zambiri,’ za anthu “amene akusonkhanitsa chuma.” (Ezek. 38:10-12) Kodi “chuma” chake ndi chiti? Anthu a Yehova ali ndi chuma chambiri chauzimu. Chuma chamtengo wapatali chimene tili nacho ndi kulambira koyera ndipo timalambira Yehova yekha. Mayikowa adzayesetsa kulanda kulambira koyera osati chifukwa chakuti akuona kuti n’kofunika koma chifukwa chakuti amadana nako komanso amadana ndi anthu amene akulambira Mulungu woona.

Gogi adzakonza “chiwembu choipa kwambiri” pofuna kuthetseratu kulambira koyera (Onani ndime 19)

20. Kodi Gogi adzalowa bwanji m’paradaiso wauzimu?

20 Kodi Gogi adzalowa bwanji m’dziko lauzimu kapena kuti m’paradaiso? Mayiko angayese kusokoneza zimene tikuchita pa moyo wathu komanso kutiletsa kulambira Mulungu woona. Kuti akwanitse kuchita zimenezi, mwina adzayesa kusokoneza njira imene timalandirira chakudya chauzimu, kutilepheretsa kuti tisamasonkhane, kusokoneza mgwirizano wathu komanso kutiletsa kulengeza uthenga wabwino mwakhama. Zinthu zonsezi ndi zimene timachita m’paradaiso wauzimu. Satana adzalimbikitsa mayiko kuti awononge olambira oona komanso kuthetsa kulambira koyera padziko lapansi.

21. N’chifukwa chiyani mukuyamikira kuti Yehova watichenjezeratu zimene zichitike m’tsogolo?

21 Gogi wa ku Magogi akadzaukira anthu onse amene akulambira Mulungu woona, zidzakhudza aliyense amene ali m’paradaiso wauzimu amene Mulungu watipatsa. Tikuthokoza kuti Yehova watichenjeza pa zimene zichitike m’tsogolo. Panopa, pamene tikuyembekezera chisautso chachikulu, tikhale ofunitsitsa kulimbikitsa kulambira koyera ndipo tiziika kulambiraku pamalo oyamba pa moyo wathu. Tikamachita zimenezi, tidzathandiza kuti dziko lathu lobwezeretsedwali likhale lokongola. Zimenezi zidzatithandiza kuti tidzaone zinthu zochititsa chidwi zimene zidzachitike m’tsogolo. Tidzaona mmene Yehova adzathandizire anthu ake komanso kuyeretsa dzina lake pa Aramagedo ndipo mutu wotsatira udzafotokoza zimenezi.

a M’mutu wotsatira wabukuli, tidzakambirana mmene Yehova adzasonyezere mkwiyo waukulu pa Gogi wa ku Magogi. Tidzakambirananso kuti zimenezi zidzachitika liti ndipo zidzakhudza bwanji anthu amene akulambira Mulungu woona.

b Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2015, tsamba 29-30.

c Lemba la Danieli 11:45 limasonyeza kuti mfumu yakumpoto idzaukira anthu a Mulungu chifukwa limanena kuti: “Mfumuyo idzamanga matenti achifumu pakati pa nyanja yaikulu [Mediterranean] ndi phiri lopatulika la Dziko Lokongola [kumene poyamba kunali kachisi wa Mulungu komanso kumene anthu ankalambirira].”

d Baibulo limanenanso kuti “Asuri” wa masiku ano adzaukira anthu a Mulungu n’cholinga chowawonongeratu. (Mika 5:5) Baibulo linaneneratu kuti anthu a Mulungu adzaukiridwa maulendo 4. Linanena kuti adzaukiridwa ndi Gogi wa ku Magogi, mfumu yakumpoto, mafumu a dziko lonse lapansi komanso Asuri. Pamenepa akunena za kuukiridwa kumodzi kumene kwatchulidwa ndi mayina osiyanasiyana.

e Onani Mutu 22 wa bukuli kuti mudziwe kuti “Gogi wa ku Magogi” amene watchulidwa pa Chivumbulutso 20:7-9 ndi ndani.