Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 18

“Ndidzakhala ndi Mkwiyo Waukulu”

“Ndidzakhala ndi Mkwiyo Waukulu”

EZEKIELI 38:18

MFUNDO YAIKULU: Gogi akadzaukira anthu a Mulungu adzaputa mkwiyo wa Yehova. Yehova adzateteza anthu ake pa nkhondo ya Aramagedo

1-3. (a) Kodi zotsatira za “mkwiyo waukulu” wa Yehova zidzakhala zotani? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi tsopano tikambirana chiyani?

 AZIBAMBO, azimayi komanso ana aimirira ndipo akuimba nyimbo ya Ufumu. Kenako mkulu akupereka pemphero lochokera pansi pamtima kupempha Yehova kuti awateteze. Onse mumpingo sakukayikira kuti Yehova awasamalira koma akufunikira kutonthozedwa komanso kulimbikitsidwa. Kunja kukumveka phokoso lalikulu la anthu amene akumenyana. Nkhondo ya Aramagedo yayambika.​—Chiv. 16:14, 16.

2 Pa nkhondo ya Aramagedo Yehova adzapha anthu ali ndi “mkwiyo waukulu” koma sadzachita zimenezo mwachisawawa. (Werengani Ezekieli 38:18.) Iye sadzasonyeza mkwiyo wake waukuluwo pa gulu limodzi la asilikali kapena dziko limodzi koma adzausonyeza kwa anthu ambirimbiri a padziko lapansi. Tsiku limenelo anthu amene adzaphedwe ndi Yehova “adzachokera kumalekezero a dziko lapansi kukafika kumalekezero ena a dziko lapansi.”​—Yer. 25:29, 33.

3 Kodi n’chiyani chimene chidzachititse Yehova amene amadziwika kuti ndi Mulungu “wachifundo ndi wokoma mtima” ndiponso “wosakwiya msanga” kuti adzachite zimenezi ali ndi “mkwiyo waukulu”? (Eks. 34:6; 1 Yoh. 4:16) Tiyeni tione mmene yankho la funso limeneli lingatilimbikitsire, kutithandiza kukhala olimba mtima komanso kutipatsa mphamvu pa ntchito yathu yolalikira masiku ano.

Kodi N’chiyani Chimene Chidzachititse Kuti Yehova Akhale Ndi “Mkwiyo Waukulu”?

4, 5. Kodi mmene Yehova amasonyezera mkwiyo zimasiyana bwanji ndi mmene anthu, omwe si angwiro amasonyezera mkwiyo?

4 Choyamba tikufunika tidziwe kuti mkwiyo wa Yehova ndi wosiyana ndi wa anthu omwe si angwiro. Munthu akakwiya kwambiri kenako n’kuchita chinachake zotsatira zake sizikhala zabwino. Mwachitsanzo, Kaini, mwana woyamba wa Adamu, “anapsa mtima kwambiri” chifukwa chakuti Yehova anakana nsembe yake koma anavomereza nsembe ya Abele. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Kaini anapha m’bale wake yemwe anali wolungama. (Gen. 4:3-8; Aheb. 11:4) Ganiziraninso za Davide amene Baibulo limanena kuti anali munthu wa pamtima pa Yehova. (Mac. 13:22) Munthu wabwinoyu nayenso anangotsala pang’ono kupalamula mlandu waukulu atamva kuti Nabala amene anali wolemera, ananyoza anyamata ake komanso iyeyo. Atakwiya kwambiri, Davide ndi asilikali ake ‘anamangirira malupanga awo mʼchiuno’ kuti akaphe Nabala amene anali wosayamika komanso munthu aliyense wamwamuna amene ankakhala m’nyumba mwake. Mwamwayi, Abigayeli amene anali mkazi wa Nabala anakwanitsa kuchonderera Davide limodzi ndi anyamata ake kuti asabwezere choipa. (1 Sam. 25:9-14, 32, 33) Mpake kuti Yehova anauzira Yakobo kulemba kuti: “Munthu amene wakwiya sachita zinthu mogwirizana ndi chilungamo cha Mulungu.”​—Yak. 1:20.

Nthawi zonse Yehova amalamulira mkwiyo wake ndipo amausonyeza pa zifukwa zomveka

5 Mosiyana ndi anthufe amene timakhala ndi mkwiyo wosalamulirika, Yehova amalamulira mkwiyo wake nthawi zonse ndipo amakwiya pa zifukwa zomveka. Ngakhale pamene wakwiya kwambiri, Yehova amachitabe zinthu mwachilungamo. Akamawononga adani ake, sawononga “olungama pamodzi ndi oipa.” (Gen. 18:22-25) Kuwonjezera pamenepo, Yehova amakwiya pokhapokha ngati pali zifukwa zomveka komanso zachilungamo. Tiyeni tione zifukwa ziwiri zimene zimachititsa kuti Yehova akwiye komanso zimene tingaphunzirepo.

6. Kodi Yehova amachita chiyani dzina lake likadetsedwa?

6 Chifukwa choyamba: Dzina la Yehova likudetsedwa. Anthu amene amati amalambira Yehova koma n’kumachita zinthu zoipa, amaipitsa mbiri ya Yehova komanso amachititsa kuti akwiye. (Ezek. 36:23) Monga mmene tinaonera m’machaputala am’mbuyo a m’bukuli, mtundu wa Isiraeli unanyozetsa dzina la Yehova. N’zomveka kuti mtima komanso zochita za Aisiraeli zinachititsa kuti Yehova akwiye. Koma Yehova sanalephere kulamulira mkwiyo wake. Iye analanga anthu ake pamlingo woyenera ndipo sanapitirire malire. (Yer. 30:11) Ndipotu Yehova akamaliza kupereka chilango, mkwiyo wake umathera pompo ndipo sapitiriza kusunga zifukwa.​—Sal. 103:9.

7, 8. Kodi tikuphunzira chiyani tikaona mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli?

7 Zimene tikuphunzirapo: Zimene Yehova anachita ndi Aisiraeli zimatipatsa chenjezo lamphamvu. Mofanana ndi Aisiraeli akale, tili ndi mwayi wodziwika ndi dzina la Yehova. Ndife Mboni za Yehova. (Yes. 43:10) Zimene timalankhula komanso kuchita zimakhudza mmene anthu amaonera Yehova. Sitikufuna kumachita zoipa mopanda manyazi n’kunyozetsa dzina la Yehova. Yehova amakwiya ndi moyo wachiphamaso ngati umenewu ndipo posachedwapa adzachitapo kanthu pofuna kuteteza mbiri yake.—Aheb. 3:13, 15; 2 Pet. 2:1, 2.

8 Kodi chenjezo lakuti Yehova amatha kusonyeza “mkwiyo waukulu” likuyenera kutichititsa kuti tisamuyandikire? Ayi. Tikudziwa kuti Yehova ndi woleza mtima komanso amakhululuka. (Yes. 55:7; Aroma 2:4) Koma tikudziwanso kuti iye si wolekerera zinthu ndipo amapereka chilango pakafunika kutero. Ndipotu timalemekeza kwambiri ulamuliro wa Yehova chifukwa timadziwa kuti iye adzasonyeza mkwiyo wake kwa anthu amene amachita zinthu zimene akudziwa kuti ndi zoipa ndipo sadzalola munthu aliyense wochita zimenezi kuti apitirize kukhala pakati pa anthu ake. (1 Akor. 5:11-13) Yehova watiuza momveka bwino zinthu zimene amakwiya nazo. Zili ndi ife kupewa kumaganizira komanso kumachita zinthu zimene zingamukwiyitse.​—Yoh. 3:36; Aroma 1:26-32; Yak. 4:8.

9, 10. Kodi Yehova amachita chiyani anthu ake okhulupirika akaopsezedwa? Perekani zitsanzo.

9 Chifukwa chachiwiri: Anthu a Yehova akuopsezedwa. Yehova amakwiya adani ake akaukira anthu ake amene mokhulupirika amasakasaka chitetezo pansi pa mapiko ake. Mwachitsanzo, Aisiraeli atachoka ku Iguputo, Farao ndi gulu lake la asilikali amphamvu analondola Aisiraeli amene ankaoneka kuti asowa mtengo wogwira pamene ankayenda m’mbali mwa Nyanja Yofiira. Koma pamene asilikali amphamvuwo ankathamangitsa Aisiraeliwo pakati pa nyanja pamene panali pouma, Yehova anagulula mawilo a magaleta awo ankhondo ndipo anakankhira Aiguptowo pakati pa nyanja. “Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.” (Eks. 14:25-28) Mkwiyo wa Yehova unayakira Aigupto chifukwa cha ‘chikondi chake chokhulupirika’ kwa anthu ake.​—Werengani Ekisodo 15:9-13.

Mofanana ndi mmene mngelo anatetezera anthu a Mulungu kwa Asuri m’nthawi ya Hezekiya, ifenso angelo adzatiteteza (Onani ndime 10, 23)

10 Mofanana ndi zimenezi, m’nthawi ya Mfumu Hezekiya, Yehova anachitapo kanthu kuti apulumutse anthu ake chifukwa choti ankawakonda. Asuri omwe anali ndi gulu lamphamvu komanso lankhanza la asilikali pa nthawiyo, anafika ndipo anali okonzeka kuukira mzinda wa Yerusalemu. Asuri anaopseza anthu okhulupirika a Yehova kuti azungulira mzinda wawo zimene zikanapangitsa kuti afe mwapang’onopang’ono koma mopweteka kwambiri. (2 Maf. 18:27) Pofuna kuteteza anthu ake, Yehova anatumiza mngelo mmodzi yekha amene anapha asilikali a Asuri okwana 185,000 usiku umodzi wokha. (2 Maf. 19:34, 35) Tangoganizani mmene zinthu zinalili mumsasa wa Asuri m’mawa wake. Mumsasawo munali mikondo, zishango komanso malupanga opanda owagwira. Palibe chitoliro chimene chikanadzutsa asilikaliwo. Palibe mkulu wa asilikali amene akanalamula asilikaliwo kuti asonkhane. Mumsasawo simunkamveka phokoso lililonse ndipo mitembo inali mbwee paliponse.

11. Kodi zitsanzo za m’Malemba zosonyeza mmene Yehova amachitira anthu ake akaopsezedwa, zimatitonthoza komanso kutilimbikitsa bwanji?

11 Zimene tikuphunzirapo: Zitsanzo zimenezi zikusonyeza mmene Yehova amachitira anthu ake akawopsezedwa, ndipo zikupereka chenjezo lamphamvu kwa adani athu lakuti: “Kupatsidwa chilango ndi Mulungu wamoyo nʼkoopsa,” mkwiyo wake ukayaka. (Aheb. 10:31) Koma kwa ifeyo, zitsanzo zimenezi zimatithandiza kukhala ndi chiyembekezo komanso kukhala olimba mtima. Timalimbikitsidwa tikadziwa kuti mdani wathu Satana, sadzapambana. Posachedwapa “kanthawi kochepa” kamene wakhala akulamulira dzikoli katha. (Chiv. 12:12) Poyembekezera kuti nthawi imeneyo ifike, panopa tizitumikira Yehova molimba mtima ndipo tizikhulupirira kuti palibe munthu, bungwe kapena boma limene lingatilepheretse kuchita zimene Mulungu amafuna. (Werengani Salimo 118:6-9.) Mawu amene mtumwi Paulo analemba mouziridwa amafotokoza mmene ifeyo tikumvera. Iye analemba kuti: “Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?”​—Aroma 8:31.

12. Pa chisautso chachikulu, n’chiyani chimene chidzachititse kuti Yehova akwiye?

12 Pa nthawi ya chisautso chachikulu chimene chikubwerachi, Yehova adzatiteteza mofanana ndi mmene anatetezera Aisiraeli atapanikizidwa ndi Aigupto komanso mmene anatetezera Ayuda, Yerusalemu atazunguliridwa ndi Asuri. Adani athu akadzafuna kutiwononga mkwiyo wa Yehova udzayaka chifukwa chakuti amatikonda kwambiri. Amene adzaganize mopusa n’kutiukira, adzakhala kuti akugwira mwana wa diso la Yehova. Iye adzachita zinthu mwamsanga komanso mosazengereza potiteteza. (Zek. 2:8, 9) Zotsatira zake zidzakhala nkhondo yoopsa yoti sinachitikepo. Koma adani a Mulungu adzakhala alibe chifukwa chomveka chowapangitsa kuti adabwe, Yehova akadzasonyeza mkwiyo wake. N’chifukwa chiyani tikutero?

Kodi Yehova Wapereka Machenjezo Otani?

13. Kodi Yehova wapereka machenjezo otani?

13 Yehova ndi “wosakwiya msanga” ndipo wakhala akupereka machenjezo okwanira oti adzawononga anthu amene amatsutsana naye komanso amene amaopseza anthu ake. (Eks. 34:6, 7) Yehova anagwiritsa ntchito aneneri monga Yeremiya, Ezekieli, Danieli ndi Khristu Yesu komanso atumwi ngati Petulo, Paulo ndi Yohane kuti achenjeze anthu za nkhondo imene ikubwera.​—Onani bokosi lakuti “Yehova Akuchenjeza Anthu Kuti Kukubwera Nkhondo Yaikulu.”

14, 15. Kodi Yehova wagwira ntchito yotani, nanga n’chifukwa chiyani?

14 Yehova anachititsa kuti machenjezo amenewa alembedwe m’Mawu ake. Iye anaonetsetsanso kuti Baibulo limasuliridwe komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa buku lililonse. Padziko lonse lapansi, Yehova ali ndi gulu lalikulu kwambiri la asilikali amene anadzipereka kuti azithandiza anthu ena kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu komanso amachenjeza anthu za “tsiku lalikulu la Yehova” limene likubwera. (Zef. 1:14; Sal. 2:10-12; 110:3) Iye walimbikitsa anthu ake kuti amasulire mabuku othandiza anthu kuphunzira Baibulo m’zilankhulo mahandiredi ambiri komanso wawathandiza kugwiritsa ntchito maola mamiliyoni ambiri chaka chilichonse kuuza anthu ena zokhudza malonjezo komanso machenjezo amene amapezeka m’Mawu ake.

15 Yehova wachita zonsezi “chifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Tili ndi mwayi waukulu woimira Mulungu wathu yemwe ndi wachikondi komanso woleza mtima ndiponso tili ndi mwayi wothandiza kulengeza nawo uthenga wake. Koma posachedwapa nthawi itha ndipo anthu amene sakumvera machenjezowo adzakhala kuti alibe mwayi woti asinthe.

Kodi Mkwiyo wa Yehova ‘Udzayaka’ Liti?

16, 17. Kodi Yehova anaika tsiku limene nkhondo yomaliza idzayambike? Fotokozani.

16 Yehova anaika tsiku la nkhondo yomaliza. Iye akudziwiratu nthawi imene anthu ake adzaukiridwe. (Mat. 24:36) Kodi Yehova akudziwa bwanji nthawi imene adani ake adzaukire?

17 Monga tinaonera m’mutu wapita uja, Yehova anauza Gogi kuti: ‘Ine ndidzakukola chibwano ndi ngowe.’ Choncho Yehova adzachititsa kuti mayiko ayambitse nkhondo yoopsa. (Ezek. 38:4) Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova ndi amene adzayambitse nkhondoyo komanso sizikutanthauza kuti amalanda ufulu wosankha wa anthu amene amamutsutsa. M’malomwake, zikusonyeza kuti Yehova amadziwa zimene zili m’mitima ya anthu ndipo amadziwa zimene adani ake adzachite, zinthu zina zake zikadzachitika.​—Sal. 94:11; Yes. 46:9, 10; Yer. 17:10.

18. N’chiyani chidzachititse anthu kumenya nkhondo ndi Wamphamvuyonse?

18 Ngati Yehova sadzayambitsa mkangano kapena kukakamiza adani ake kuti amenye nkhondo, n’chifukwa chiyani anthu adzapezeke kuti akulimbana ndi Wamphamvuyonse? Chifukwa chimodzi n’chakuti pofika pa nthawi imeneyo iwo adzakhala atatsimikiza m’mitima yawo kuti Mulungu kulibe kapena kuti sangalowerere pa zochitika za anthu. Mwina adzaganiza mwa njira imeneyi chifukwa pa nthawiyo adzakhala atawononga mabungwe onse azipembedzo zabodza padziko lapansi. Iwo ayenera kuti azidzaganiza kuti zikanakhala kuti Mulungu alipo, n’zosakayikitsa kuti akanateteza mabungwe amene amanena kuti amamuimira. Iwo sadzazindikira kuti anali Mulungu amene anaika maganizo m’mitima yawo kuti awononge zipembedzo zimene zimanena kuti zimamuimira koma zikuchita zosiyana ndi zimene iye amafuna.​—Chiv. 17:16, 17.

19. N’chiyani chingadzachitike pambuyo poti chipembedzo chabodza chawonongedwa?

19 Pa nthawi ina pambuyo poti chipembedzo chabodza chawonongedwa, Yehova adzachititsa kuti anthu ake alengeze uthenga wowawa, womwe buku la Chivumbulutso limauyerekezera ndi matalala amene limodzi ndi lolemera makilogalamu 20. (Chiv. 16:21) Uthenga umenewu, womwe mwina udzakhala woti mabungwe andale komanso amalonda atsala pang’ono kuwonongedwa, udzapsetsa mtima anthu amene adzamvetsere moti adzafika ponyoza Mulungu. N’zodziwikiratu kuti uthenga umenewu ndi umene udzapangitse kuti mayiko aukire anthu a Mulungu n’cholinga choti awathetseretu. Iwo adzaganiza kuti ndife osatetezeka ndipo akhoza kutiwononga mosavuta. Komatu zimenezi zidzawabweretsera mavuto aakulu.

Kodi Yehova Adzasonyeza Bwanji Mkwiyo Wake?

20, 21. Kodi Gogi ndi ndani ndipo n’chiyani chimene chidzamuchitikire?

20 Monga mmene taonera m’Mutu 17 wa buku lino, Ezekieli anagwiritsa ntchito dzina lakuti, “Gogi wa kudziko la Magogi,” ponena za mgwirizano wa mayiko amene adzatiukire. (Ezek. 38:2) Koma mayiko amene adzapange mgwirizano umenewu sadzakhala ogwirizana kwa nthawi yaitali. Ngakhale adzaoneke ngati akugwirizana, mayikowa adzapitiriza kusonyeza mtima wokonda mikangano, kunyada komanso wokonda dziko lawo. Yehova sadzavutika kupangitsa aliyense kutenga lupanga lake kuti ‘aphe mʼbale wake.’ (Ezek. 38:21) Koma mayikowa sadzawonongedwa ndi tsoka lochititsidwa ndi anthu.

21 Adani asanawonongedwe adzakhala ataona chizindikiro cha Mwana wa munthu ndipo mosakayikira zimenezi zidzakhala zodabwitsa zimene zidzasonyeze mphamvu zimene Yehova ndi Yesu ali nazo. Adani athu adzaona zinthu zimene zidzawachititse kuti akhale ndi nkhawa yaikulu. Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, “anthu adzakomoka chifukwa cha mantha komanso chifukwa choyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi kumene kuli anthu.” (Luka 21:25-27) Iwo adzachita mantha akadzazindikira kuti analakwitsa kwambiri kuukira anthu a Yehova. Adaniwo adzakakamizika kudziwa kuti Mlengi wathu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, ndi mkulu wa asilikali ankhondo. (Sal. 46:6-11; Ezek. 38:23) N’zosakayikitsa kuti Yehova adzamasula magulu ankhondo akumwamba komanso adzagwiritsa ntchito mphamvu za m’chilengedwe mwa njira yakuti adzateteza anthu ake okhulupirika koma n’kuwononga adani ake.​—Werengani 2 Petulo 2:9.

Anthu ake akadzaopsezedwa, Yehova adzagwiritsa ntchito magulu ake ankhondo akumwamba kuti asonyeze mkwiyo wake. (Onani ndime 21)

22, 23. Ndi ndani amene adzateteze anthu a Mulungu, ndipo sitikukayikira kuti adzamva bwanji ndi ntchito yawoyo?

Kodi kudziwa zokhudza tsiku la Yehova kukuyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?

22 Taganizirani mmene Yesu adzasonyezere kuti ndi wofunitsitsa kutsogolera gulu la nkhondo polimbana ndi adani a Mulungu komanso kuteteza anthu amene amakonda ndi kutumikira Atate ake. Taganiziraninso mmene odzozedwa adzamvere pa nthawiyo. Pa nthawi ina, Aramagedo isanayambe, odzozedwa omaliza amene adzakhale adakali padziko lapansi, adzaukitsidwa n’kupita kumwamba kuti onse a 144,000 akamenye nkhondo limodzi ndi Yesu. (Chiv. 17:12-14) Popeza akhala akugwira ntchito limodzi ndi a nkhosa zina m’masiku otsiriza, mosakayikira odzozedwa ambiri ali pa ubwenzi wabwino ndi ankhosa zina. Pa nthawi imeneyo, odzozedwa adzakhala kuti ali ndi ulamuliro komanso mphamvu zoteteza anthu amene anawathandiza mokhulupirika pa mayesero awo.​—Mat. 25:31-40.

23 Nawonso angelo adzakhala mbali ya kumwamba ya gulu la asilikali a Yesu. (2 Ates. 1:7; Chiv. 19:14) Angelowa anathandizapo kale Yesu kuchotsa Satana komanso ziwanda kumwamba. (Chiv. 12:7-9) Ndipo akhala akuthandiza kusonkhanitsa anthu padziko lapansi amene akufuna kulambira Yehova. (Chiv. 14:6, 7) Zidzakhalatu zoyenera kuti Yehova alole angelo kuti ateteze anthu ake okhulupirika padziko lapansi. Koma chofunika kwambiri n’chakuti asilikali onse a Yehova adzakhala ndi mwayi wokweza komanso kuyeretsa dzina la Yehova kapena kuti mbiri yake. Izi zidzachitika akadzathandiza nawo kuwononga adani a Mulungu.​—Mat. 6:9, 10.

24. Kodi khamu lalikulu la nkhosa zina lidzachita chiyani?

24 Chifukwa chokhala ndi gulu lamphamvu komanso lofunitsitsa kumenya nkhondo kuti liwateteze, a khamu lalikulu, sadzakhala ndi chifukwa chilichonse chochitira mantha. Iwo ‘adzaimirira ndi kutukula mitu yawo, chifukwa chipulumutso chawo chidzakhala chikuyandikira.’ (Luka 21:28) N’zofunika kwambiri kuti tsiku la Yehova lisanafike, tithandize anthu ambiri mmene tingathere kuti adziwe Bambo athu omwe ndi achikondi komanso achifundo ndipo amatiteteza.​—Werengani Zefaniya 2:2, 3.

Pa Aramagedo, anthu a Yehova sadzamenya nkhondo. Pamene adani akuukirana okhaokha, angelo adzateteza anthu a Mulungu.​—Ezek. 38:21 (Onani ndime 22-24)

25. Kodi tikambirana chiyani m’mutu wotsatira?

25 Nkhondo zimene anthu amayambitsa zimabweretsa chisokonezo komanso chisoni. Koma mosiyana ndi zimenezi, zotsatira za Aramagedo zidzakhala mtendere komanso chisangalalo. Kodi zinthu zidzakhala bwanji mkwiyo wa Yehova ukadzatha, asilikali ake akadzamaliza kumenya nkhondo ndiponso phokoso la nkhondo likamadzatha pang’onopang’ono? M’mutu wotsatira tidzakambirana mmene zinthu zidzakhalire m’tsogolo.